Kufunafuna Maulosi Odalirika
MWAMSANGA pamene Alexander Wamkulu mfumu ya Makedoniya anakhala pa mpando wachifumu mu 336 B.C.E, anapita ku kachisi wa ku Delphi m’chigawo chapakati cha dziko la Girisi. Zolinga zake za m’tsogolo zinali zakuti akagonjetse mayiko ambiri a panthaŵiyo. Komabe anafuna chitsimikizo chaumulungu chakuti akapambana. Malinga ndi nthano, tsiku lomwe anapita ku Delphi kukaonana ndi mlauli silinali lovomerezeka. Alexander pofunabe yankho, analimbikira kukakamiza wansembe wamkazi kulosera. Atatopa naye, wansembeyo anafuula kuti: “Ee, mwanawe ndiwe wosagonjetseka!” Mfumu yachinyamatayo inaona yankholo kukhala ulosi—wolonjeza kuti idzapambana pankhondo zake zonse.
Komabe, Alexander akanadziŵa bwino zotsatira za nkhondo zake ngati akanaŵerenga maulosi a Baibulo m’buku la Danieli. Mosaphonya konse, analosera za kupambana kwake kofulumira. Malinga ndi nthano, Alexander m’kupita kwa nthaŵi anaona zimene Danieli analemba za iye. Malinga ndi Josephus wolemba mbiri wachiyuda, pamene mfumu ya Makedoniya inafika mu Yerusalemu, anaisonyeza ulosi wa Danieli—mwinamwake chaputala 8 cha bukuli. (Danieli 8:5-8, 20, 21) Akuti chifukwa cha zimenezi, mzindawo unasiyidwa ndi magulu ankhondo owononga a Alexander.
Chosoŵa Chachibadwa Chimene Anthu Ali Nacho
Mfumu kaya munthu wamba, kale ngakhale tsopano—aliyense amafuna maulosi odalirika onena za m’tsogolo. Monga zolengedwa zanzeru, anthufe timaphunzira mbiri yakale ndipo timadziŵa za m’nthaŵi ino, komanso timafuna kwambiri kudziŵa za m’tsogolo. Mwambi wachitchaina umati: “Iye amene angaoneretu zomwe zidzachitika masiku atatu otsatira adzalemera kwazaka zikwizikwi.”
M’mibadwo yonse, anthu miyandamiyanda ayesetsa kufufuza zam’tsogolo mwa kufunsira kwa imene aiyesa milungu. Mwachitsanzo, Agiriki. Iwo anali ndi akachisi ambiri, monga aja a ku Delphi, Delos, Dodona, kumene ankapita kukafunsira kwa milungu yawo pa zandale kapena zankhondo ngakhalenso zinthu zina zaumwini monga maulendo, ukwati, ndi ana. Mafumu, atsogoleri ankhondo komanso mafuko onse ndi mizinda ankafuna chitsogozo kwa mizimu mwa mayankho ameneŵa.
Malinga ndi polofesa wina, tsopano “mabungwe ofufuza zam’tsogolo akuwonjezeka mwadzidzidzi.” Komabe, ambiri amanyalanyaza gwero lokha la ulosi woona—Baibulo. Amatsutsa lingaliro lililonse lakuti maulosi a Baibulo ali ndi mfundo zonse zimene akufuna. Anthu ophunzira ambiri amafika ponena kuti ulosi wa Baibulo umafanana ndi zonena za alauli akale. Anthu okayikira amakono kaŵirikaŵiri sakhulupirira ulosi wa Baibulo.
Tikukupemphani kudzifufuzira nokha nkhaniyi. Kodi kuyerekeza mosamalitsa maulosi a Baibulo ndi zonena za alauli kumavumbulanji? Kodi mungakhulupirire ulosi wa Baibulo kusiyana ndi zonena za alauli akale? Ndipo kodi mungadalire maulosi a Baibulo m’moyo wanu?
[Chithunzi patsamba 3]
Baibulo linalosera zakuti Alexander akagonjetsa ena mofulumira
[Mawu a Chithunzi]
Cortesíadel Museo del Prado, Madrid, Spain
[Chithunzi patsamba 4]
Alexander Wamkulu
[Mawu a Chithunzi]
Musei Capitolini, Roma
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
CHIKUTO: Kazembe Titus ndi Alexander Wamkulu: Musei Capitolini, Roma