Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 7/15 tsamba 29-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • ‘Musaleme pakuchita Zabwino’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuyesetsa Kuti Anthu Mumpingo Apitirize Kukhala Amtendere Komanso Oyera
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • “Muzilemekeza Anthu Amene Akugwira Ntchito Mwakhama Pakati Panu”
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 7/15 tsamba 29-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi ‘kuyang’anira’ kotchulidwa pa 2 Atesalonika 3:14 kumachitidwa ndi mpingo, kapena kodi kumachitidwa ndi Mkristu aliyense payekha mwa kupewa anthu osaweruzika?

Zimene mtumwi Paulo analembera Atesalonika zimasonyeza kuti akulu a mpingo ndiwo amachitapo kanthu ‘kuyang’anirako.’ Komanso, Akristu onse aliyense payekha amatsatira zimenezo, ndi zolinga zauzimu. Titha kumvetsa zimenezi titapenda uphungu wa Paulo malinga ndi mmene mikhalidwe inalili panthaŵi imeneyo.

Paulo anathandiza kukhazikitsa mpingo wa ku Tesalonika, ndipo anathandiza amuna ndi akazi kukhala okhulupirira. (Machitidwe 17:1-4) Pambuyo pake anawalembera kalata ali ku Korinto kuwathokoza ndi kuwalimbikitsa. Komanso Paulo anapereka uphungu wofunikira. Anawalimbikitsa ‘kukhala chete ndi kuchita za iwo eni ndi kugwira ntchito ndi manja awo.’ Ena sanali kuchita zimenezo, choncho Paulo anawonjezera kuti: “Tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi [“adwakedwake,” NW], limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka.” Inde, pakati pawo panali anthu “adwakedwake”a amene anafunikira uphungu.​—1 Atesalonika 1:2-10; 4:11; 5:14.

Patapita miyezi ingapo, Paulo analemba kalata yake yachiŵiri kwa Atesalonika, yokhala ndi mawu ena onena za kukhalapo kwa Yesu m’tsogolo. Paulo anaperekanso chitsogozo chokhudza mmene iwo akanachitira ndi anthu adwakedwake amene ‘sanali kugwira ntchito konse, koma ochita mwina ndi mwina [“oloŵerera pankhani zosawakhudza,” NW].’ Ntchito zawo zinali zosiyana kwambiri ndi chitsanzo cha Paulo monga munthu wakhama pantchito komanso zinasiyana ndi lamulo lake lomveka lakuti munthu azigwira ntchito kuti athandizike. (2 Atesalonika 3:7-12) Paulo ananena kuti panafunikira kuchitapo kanthu. Anachita zimenezi pambuyo poti akulu apereka kale chenjezo kapena uphungu kwa anthu adwakedwake. Paulo analemba kuti:

“Ndipo tikulamulirani, abale, . . . kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife. Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino. Koma ngati wina samvera mawu athu m’kalata uyu, yang’anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi. Koma musamuyese mdani, koma mumuyambirire [“mum’chenjeze,” Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono] ngati mbale.”​—2 Atesalonika 3:6, 13-15.

Zina zimene anafunikira kuchita zinaphatikizapo kupewa anthu adwakedwake, kuwayang’anira, kusiya kuyanjana nawo, komano kuwachenjeza ngati abale. Kodi n’chiyani chikanachititsa ziŵalo za mpingo kuchita zimenezo? Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tione nkhani zitatu zimene Paulo sanali kufotokoza panopo.

1. Tikudziŵa kuti Akristu ali opanda ungwiro komanso ali ndi zophophonya. Ngakhale zili choncho, chikondi chili chizindikiro cha Chikristu choona, ndipo chimafuna kuti tizimvetsa ena akalakwa ndi kuwakhululukira. Mwachitsanzo, Mkristu angakwiye koopsa nthaŵi zina, monga momwe zinachitikira pakati pa Barnaba ndi Paulo. (Machitidwe 15:36-40) Nthaŵi zina chifukwa chotopa, wina angalankhule mwaukali komanso ndi mawu opyoza. Zitatero, ifeyo mwa kusonyeza chikondi ndi kutsata uphungu wa Baibulo, tingakwirire mphulupuluyo, kupitiriza ndi moyo wathu, kuyanjana, ndi kugwira ntchito limodzi ndi Mkristu mnzathu. (Mateyu 5:23-25; 6:14; 7:1-5; 1 Petro 4:8) Ndithudi, kulakwa ngati kumeneku si kumene Paulo anali kufotokoza mu 2 Atesalonika.

2. Paulo sanali kulongosola za nkhani pamene Mkristu payekha asankha kusayanjana kwambiri ndi wina amene moyo wake kapena maganizo ake sali abwino​—mwachitsanzo, munthu amene amaoneka kuti amakondetsa zosangalatsa kapenanso zinthu zakuthupi. Nthaŵi zinanso kholo lingaletse mwana kusayanjana kwambiri ndi ana amene salemekeza makolo, amene saseŵera bwino kapenanso okonda maseŵera angozi, kapena amene saona kufunika kwa Chikristu. Zimenezo zimangokhala zosankha zaumwini zogwirizana ndi zimene timaŵerenga pa Miyambo 13:20 kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:33.

3. Pankhani ina yaikulu yosiyana kwambiri, Paulo analembera Akorinto za munthu amene ali ndi chizoloŵezi chochita tchimo lalikulu komanso wosalapa. Anthu ochimwa komanso osalapa amenewo anayenera kuchotsedwa mumpingo. Munthu “woipayo” anafunikira kuperekedwa kwa Satana, titero kunena kwake. Zitatero, Akristu okhulupirika sanafunikire kuyanjana nawo anthu oipawo; mtumwi Yohane analimbikitsa Akristu kuti asamawapatse ndi moni womwe. (1 Akorinto 5:1-13; 2 Yohane 9-11) Koma zimenezi sizikugwirizananso ndi uphungu wa pa 2 Atesalonika 3:14.

Nkhani yokhudza anthu “adwakedwake” yofotokozedwa mu 2 Atesalonika ikusiyana ndi nkhani zitatu tatchulazo. Paulo analemba kuti amenewo anali ‘abale’ ndithu, ofunikira kuchenjezedwa ndi kuonedwa ngati abale ndithu. Chotero, vuto la abale “adwakedwake” silinali ngati lija longosemphana maganizo pakati pa Akristu kapenanso loopsa ndithu lofuna kuti akulu a mpingo aloŵererepo ndi kuwachotsa, monga momwe Paulo anachitira pamlandu wa chiwerewere wa ku Korinto. Anthu “adwakedwake” sanali ndi mlandu wochita tchimo lalikulu, monga munthu uja amene anachotsedwa ku Korinto.

Anthu ‘adwakedwake’ a ku Tesalonika anali ndi mlandu wopatuka ndithu pa Chikristu. Iwo sankagwira ntchito, kaya mwina chifukwa choganiza kuti Kristu anali pafupi kubwera mwinanso chifukwa cha ulesi. Kuwonjezera apo, ankachititsa msokonezo kwambiri mwa ‘kuloŵerera pankhani zosawakhudza.’ Akulu a mumpingo angakhale atawapatsa uphungu mobwerezabwereza, malinga ndi langizo la Paulo m’kalata yake yoyamba komanso ndi mauphungu ena aumulungu. (Miyambo 6:6-11; 10:4, 5; 12:11, 24; 24:30-34) Chikhalirechobe, anapitiriza ndi khalidwe limene linapereka chithunzi choipa pa mpingo komanso limene Akristu ena akanatengera. Chotero, Paulo monga mkulu wachikristu, anatchula poyera kayendedwe kawo kadwakedwake popanda kuwatchula mayina awo, navumbula njira zawo zolakwika.

Komanso anauza mpingo kuti Mkristu aliyense anayenera payekha ‘kuyang’anira’ anthu adwakedwakewo. Zimenezi zinatanthauza kuti aliyense anayenera kusamala ndi aja amene zochita zawo zinagwirizana ndi khalidwe limene mpingo unachenjezedwa poyera. Paulo anawalangiza kuti ‘abwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake.’ Zimenezo sizinatanthauze kum’peweratu munthuyo, pakuti iwo anayenera ‘kum’chenjeza ngati mbale.’ Iwo akapitiriza kuyanjana naye monga Mkristu pamisonkhano mwinanso mu ulaliki. Akayenera kukhulupirira kuti mbale wawoyo adzalabadira chenjezolo ndi kusiya njira zake zosokonezazo.

Kodi ndi motani mmene iwo ‘akabwevukira’ kwa iye? Maumboni akusonyeza kuti ndi panthaŵi yocheza. (Yerekezani ndi Agalatiya 2:12.) Kupewa kwawo kucheza naye kapena kusangalala limodzi naye kukanam’sonyeza kuti anthu akhalidwe akunyansidwa ndi njira zake. Ngakhale ngati sakanachita manyazi kapena sanasinthe, ena ndithu sakanatengera njira zake kukhala ngati iyeyo. Komanso, Akristu amenewo yense payekha anafunikira kuyesetsa kuchita zabwino. Paulo anawalangiza kuti: “Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.”​—2 Atesalonika 3:13.

Ndithudi, uphungu wa mtumwi umenewu suli maziko onyozera kapena kuweruzira abale athu amene amaphophonya kapena kulakwa pang’ono. M’malo mwake, cholinga chake ndicho kuthandiza munthu amene watsata njira yosokoneza imene ikuwombana kwambiri ndi Chikristu.

Paulo sanapereke malamulo ambirimbiri ngati kuyesa kukhazikitsa ndondomeko yovuta. Koma n’zachionekere kuti akulu choyamba ayenera kupereka uphungu komanso kuyesa kuthandiza munthu wadwakedwakeyo. Koma ngati munthuyo wakanika napitiriza ndi njira yake yosokoneza komanso imene ena angatengereko, angagamule zoti mpingo uchenjezedwe. Angakonze nkhani yofotokoza chifukwa chake kuyenda dwakedwake koteroko kuyenera kupewedwa. Sadzatchula dzina, koma nkhani yawo yochenjeza idzathandiza kuteteza mpingo chifukwa anthu olabadira adzayesetsa kupewa kucheza ndi wina aliyense amene asonyeza mosapeneka khalidwe ladwakedwake limenelo.

Chikhulupiriro chimakhalapo chakuti m’kupita kwa nthaŵi, woyenda dwakedwake ameneyo adzachita manyazi ndi njira zake ndipo adzasintha. Pamene akulu ndi ena mumpingo aona kusintha kwake, aliyense payekha angasankhe kuyambanso kucheza naye.

Nachi chidule chake: Akulu a mpingo amatsogolera kupereka thandizo ndi uphungu ngati wina akuyenda dwakedwake. Ngati iye alephera kuzindikira cholakwa chake napitiriza kumaika ena pangozi, akulu angachenjeze mpingo mwa kukamba nkhani yomveketsa bwino zimene Baibulo limanena​—kaya za kukhala pachibwenzi ndi osakhulupirira, kapena khalidwe lina lililonse losayenera. (1 Akorinto 7:39; 2 Akorinto 6:14) Akristu mumpingo amene achenjezedwa mwanjira imeneyo angasankhe kusacheza ndi aja amene mosapeneka akutsata njira yadwakedwake komano adakali abale ndithu.

[Mawu a M’munsi]

a Liwu lake lachigiriki ankaligwiritsa ntchito ponena za asilikali amene sankatsata dongosolo kapena mwambo, komanso ophunzira aukamberembere, amene ankakhala osapita ku sukulu masiku ena.

[Zithunzi patsamba 31]

Akulu achikristu amachenjeza anthu adwakedwake komano amawaonabe ngati okhulupirira anzawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena