Chisonkhezero cha Mabwenzi—Kodi Chingakuthandizeni?
Tonsefe mwachibadwa timafunitsitsa kuti mabwenzi athu atikonde. Palibe amene amafuna kudedwa, kapena kukanidwa. Choncho, pam’lingo wosiyanasiyana, mabwenzi athu amatisonkhezera.
LIWU lakuti bwenzi limatanthauza “munthu amene ali ndi mikhalidwe yofanana ndi wina; . . . amene ali m’gulu limodzimodzi la anthu amene umacheza nawo, [makamaka] amene amalingana zaka zawo zakubadwa, malo, kapena udindo.” Ndiyeno, chisonkhezero cha mabwenzi ndi mphamvu imene mabwenzi ali nawo pa ife, yoti, mosazindikira kaya mozindikira, tigwirizane ndi mmene iwo amaganizira kapena kuchitira zinthu. Kaŵirikaŵiri chisonkhezero cha mabwenzi chimaoneka kukhala chosathandiza. Komabe, monga mmene tionere, tingachisinthe kuti chitithandize.
Mphamvu Yake Ikhudza Anthu Amisinkhu Yonse
Chisonkhezero cha mabwenzi sichikhala pa achinyamata okha; komanso pa anthu amisinkhu ina yonse. Mphamvu yake imaoneka pamene tidzifunsa ife eni mafunso akuti: “Ena akuchita zimenezi, n’chifukwa chiyani ine sindikutero?” “Kodi n’chifukwa chiyani nthaŵi zonse ndiyenera kusiyana ndi ena?” “Kodi anthu ena aziganiza chiyani kapena kunenanji?” “Anzanga onse akupeza zibwenzi ndipo akukwatira ndi kukwatiwa, koma ine ayi. Kodi vuto langa n’chiyani?”
Ngakhale kuti chisonkhezero chimenechi chimakhudza anthu amisinkhu yonse, chimakhala champhamvu kwambiri pa zaka za kusinkhuka. The World Book Encyclopedia imati “ambiri pazaka za kusinkhuka amayanjana kwambiri ndi mabwenzi awo—ndiko kuti, anzawo komanso anthu amene amawadziŵa. Achinyamata amenewa amafuna mabwenzi awo kuwayanja, koma osati makolo awo, ndipo angasinthe khalidwe lawo kuti apeze chiyanjo chimenechi.” Achinyamata, ikupitiriza motero, “amaganiza kuti akukula bwino ngati mabwenzi awo akuwayanja ndi kuwakonda.” N’chifukwa chake “amaloŵerera kuchita zinthu zimene amaganiza kuti ziwatchukitsa, monga kavalidwe, luso lotsogolera komanso kupeza zibwenzi.”
Mwamuna ndi mkazi okwatirana angaone kuti zosankha zawo pa mtundu wa nyumba yomwe azidzakhala, mtundu wa galimoto lomwe azidzayendera, kaya ngati adzakhala ndi ana kapena ayi, ndi zina zotero zimasonkhezeredwa ndi mabwenzi—zimene zimaloledwa kwawo, zimene anzawo amafuna, komanso mtundu wawo. Mabanja ena afika pakugwa m’ngongole chifukwa chofuna kupeza katundu wofanana ndi yemwe anansi kapena mabwenzi ali naye. Inde, zolinga zathu, zoganiza zathu, ndiponso zosankha zathu kaŵirikaŵiri zimaonetsa kuti tikukhudzidwa ndi mphamvu yovuta kuzindikira ya chisonkhezero cha mabwenzi. Poganiza za mphamvu yake, kodi tingachite ndi chisonkhezero cha mabwenzi mwanjira yopindulitsa, yotithandiza pa zimene tifuna kuchita? Inde, tingatero!
Kugwiritsa Bwino Ntchito Chisonkhezero cha Mabwenzi
Madokotala ndi akatswiri azachipatala amadziŵa kufunika kwa odwala awo kucheza ndi anthu olimbikitsa komanso othandiza. Zinthu ngati zimenezi zingathandize wodwala kuchira msanga. Mwachitsanzo, anthu amene aduka dzanja kapena mwendo, kaŵirikaŵiri amathandizidwa kuchira mwakuthupi pang’onopang’ono komanso kulimbika mtima chifukwa cha chitsanzo chabwino ndi chilimbikitso za amene anadwalapo matenda ofananawo. Mwachionekere, kukhala ndi mayanjano abwino ophatikizapo anthu opereka chitsanzo chabwino komanso olimbikitsa ndiko kugwiritsa ntchito chisonkhezero cha mabwenzi mwanjira yabwino.
Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito mumpingo wachikristu, popeza kuti chimodzi mwa zifukwa zomwe Yehova wauzira anthu ake kusonkhana pamodzi nthaŵi zonse n’chakuti mabwenzi awo aziwasonkhezera kuchita zabwino. Mulungu akutilimbikitsa kuti ‘tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino ndipo tidandaulirane.’ (Ahebri 10:24, 25) Chilimbikitso chimenechi n’chofunika kwambiri chifukwa cha zopsinja zofooketsa ndi zopweteka zimene zili m’dziko lerolino. Chifukwa cha zopsinja zoterezi, Akristu ayenera ‘kuyesetsa’ kukhalabe olimba mwauzimu. (Luka 13:24) N’chifukwa chake timafunikira komanso timayamikira chichirikizo chachikondi cha okhulupirira anzathu. Kuwonjezera pamenepa, ena akupirira ‘minga m’thupi,’ mwinamwake matenda kapena chilema. (2 Akorinto 12:7) Ena angakhale akulimbana ndi zizoloŵezi zawo zoipa ndi kupsinjika maganizo, kapena akulephera kupeza zinthu zofunika pa moyo wa munthu. Choncho, tingachite bwino kuyanjana ndi anthu omwe ali pafupi ndi Yehova Mulungu komanso amene amakonda kumam’tumikira. Mabwenzi otere adzatilimbikitsa ndi kutithandiza ‘kulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro.’—Mateyu 24:13.
Tikasankha mabwenzi abwino, tingathe kuyang’anira chisonkhezero chawo pa ife. Ndiponso, chakudya chabwino chauzimu komanso malangizo othandiza operekedwa pamisonkhano yachikristu zimawonjezera chilimbikitso chomwe mabwenzi amapereka.
N’zoona, kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse si kwapafupi. Ena mwina amalimbikitsidwa pang’ono kapena salimbikitsidwa konse ndi anzawo muukwati, ena angakhale ndi ana ofunika kuwakonzekeretsa kuti apite nawo, ndiponso kwa ena kayendedwe kangakhale kovuta. Koma taganizani izi: Ngati simulephera kumisonkhano chifukwa cha mavuto ngati amenewa, chitsanzo chanu chingalimbikitse ena amene ali ndi mavuto ofananawo. Kunena kwina, inu ndi enanso onga inu simukungopereka chitsanzo chabwino, komanso chisonkhezero chabwino cha mabwenzi—ndipo mumatero popanda kukakamiza.
Inde, mtumwi Paulo, yemwe anakumana ndi mavuto ndi zopinga zambiri, analimbikitsa Akristu kutsatira chitsanzo chake chabwino ndi cha Akristu ena aakulu msinkhu. Iye anati: “Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang’anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.” (Afilipi 3:17; 4:9) Akristu oyambirira ku Tesalonika anatsatira chitsanzo chabwino cha Paulo. Ponena za iwo Paulo analemba kuti: “Munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, mmene mudalandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera; kotero kuti munayamba kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupira m’Makedoniya ndi m’Akaya.” (1 Atesalonika 1:6, 7) Choncho, maganizo athu abwino komanso chitsanzo chathu zingawakhudze mofananamo aja omwe timayanjana nawo.
Peŵani Zosonkhezera Zoipa
Ngati tifuna kuti tipeŵe chisonkhezero choipa, tiyenera kukaniza aja ‘amene ayendayenda monga mwa thupi.’ (Aroma 8:4, 5; 1 Yohane 2:15-17) Apo ayi, chisonkhezero choipa cha mabwenzi chidzatichotsa kwa Yehova ndi uphungu wake wanzeru. Miyambo 13:20 imati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru, koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” Kodi mungaganize za wina wake amene anapwetekedwa chifukwa cha chisonkhezero choipa cha mabwenzi? Mwachitsanzo, Akristu ena ayamba kukonda chuma, achita chiwerewere, kapenanso kumwa mankhwala osokoneza bongo komanso moŵa mwauchidakwa chifukwa chotengeka ndi mabwenzi awo.
Ngakhale mumpingo wachikristu, tingasonkhezeredwe moipa ndi mabwenzi ngati tisankha anthu ofooka mwauzimu n’kumayanjana nawo kwambiri. (1 Akorinto 15:33; 2 Atesalonika 3:14) Otereŵa kaŵirikaŵiri alibe chizoloŵezi chokamba nkhani zauzimu; iwo angamanyodole ngakhale ena amene amakonda kukambirana zauzimu. Ngati tisankha anthu otere kukhala mabwenzi athu apamtima, chisonkhezero chawo chingatikakamize kukhala ngati iwo, ndipo posakhalitsa tidzapeza kuti tikuonetsa maganizo awo komanso mzimu wawo. Tingayambe ngakhale kusuliza anzathu achikhulupiriro cholimba amene akuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu.—1 Timoteo 4:15.
N’kwanzeru kwambiri bwanji kupalana ubwenzi ndi anthu amene akuyesetsa kukondweretsa Yehova, amene amakonda zinthu zauzimu! Mabwenzi otere adzatithandiza kusonyeza “nzeru yochokera kumwamba.” Imeneyo “iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, . . . ” (Yakobo 3:17) Zimenezi sizitanthauza kuti anthu okonda zauzimu sangathe kulankhula zinthu zina kusiyapo zauzimu. Si zimenezo ayi! Tangoganizani za nkhani zosangalatsa zosiyanasiyana zimene zofalitsa za Watch Tower monga magazini ya Galamukani! zimafotokoza. Ndithudi nkhani zabwino zoti n’kukambirana n’zosatha, ndipo mwa kuchita chidwi ndi nkhani zosiyanasiyana zimenezi, timasonyeza kuti timakonda moyo komanso ntchito imene Yehova anachita ndi manja ake.
Monga momwe woseŵera mpira amanolera luso lake mwa kuseŵera ndi akatswiri anzake, momwemonso mayanjano abwino amatilimbikitsa maganizo, mtima ndiponso mwauzimu. Koma mayanjano oipa angatichititse kukhala achinyengo mwa kutilimbikitsa kutsata moyo wachiphamaso. N’kwabwino zedi kukhala ndi chikumbumtima chabwino komanso kusunga ulemu wako!
Ena Amene Anapindula
Anthu ambiri amapeza kuti kuphunzira ziphunzitso za Baibulo ndi miyezo yake ya makhalidwe ndi yauzimu n’kosavuta. Komabe, chovuta n’chakuti uchite zimene waphunzira. Monga momwe zitsanzo zotsatira zikusonyezera, chisonkhezero cha mabwenzi abwino chingatithandize kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse.
Mboni ina imene ili muutumiki wa nthaŵi zonse pamodzi ndi mkazi wake inanena kuti chitsanzo cha mabwenzi ake chinakhudza zolinga zake m’moyo. Pamene anali kukula, anakumana ndi zisonkhezero zoipa. Komabe, anasankha mabwenzi ake anthu amene ankam’limbikitsa kukhala wokhazikika muutumiki ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu. Kugwirizana kwake ndi mabwenzi amenewo kunam’thandiza kukula mwauzimu.
Mboni inanso inalemba kuti: “Titangokwatirana, ine ndi mkazi wanga tinasamukira ku mpingo kumene mwamuna ndi mkazi wake amisinkhu yofanana ndi yathu anali apainiya okhazikika. Chitsanzo chawo chinatilimbikitsa kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse. Ndipo nafenso tinathandiza kukulitsa mzimu wochita upainiya mumpingowo. Motero, anthu ambiri anayambanso upainiya kugwirizana nafe.”
Kuyanjana ndi anthu amene ali ndi zolinga zateokalase kumachititsa kumvera Yehova kukhala kosavuta. Limeneli ndi phindu lina la chisonkhezero chabwino cha mabwenzi. Mboni ina imene inayamba utumiki wa nthaŵi zonse idakali mnyamata komanso n’kudzakhala woyang’anira woyendayenda, tsopano ikutumikira pa imodzi ya maofesi a nthambi za Watch Tower Society. Inalemba kuti: “Zina zosangalatsa zimene ndikukumbukira ndidakali wamng’ono, ndizo kucheza kwa atumiki anthaŵi zonse kunyumba kwathu. Nthaŵi zonse tinali ndi mpata wakudya chakudya ndi mlendo m’chipinda chathu chodyera. Woyang’anira dera wina anandipatsa chola chopita nacho muumboni pamene ndinali ndi zaka khumi zakubadwa. Ndimachikonda chola chimenechi mpaka pano.”
Pokumbukira zaka zake zaunyamata, Mboni imeneyi inawonjeza kuti: “Achinyamata ambiri mumpingo anafuna kutengamo mbali m’zochitika za mumpingo, ndipo chitsanzo chawo chinalimbikitsa enafe kukhumba zofananazo.” Mabwenzi abwino anathandiza wachinyamata ameneyu kukula ngati mphukira ndi kukhala Mkristu wonga mtengo wabwino wowongoka. Makolo, kodi mumaitana anthu olimbikitsa komanso amene angasonkhezere ana anu m’njira yabwino?—Malaki 3:16.
Inde, si aliyense amene angakhale mu utumiki wa nthaŵi zonse monga amene tawatchula kumene. Komabe, tonsefe tingaphunzire kukonda Yehova ‘ndi mtima wathu wonse, moyo wathu, ndi nzeru zathu.’ (Mateyu 22:37) Kusankha kwathu mabwenzi kumathandiza kwambiri kukulitsa chikondi chimenechi, ndiiko komwe, chiyembekezo chathu cha moyo wosatha.
Wamasalmo anapereka njira yapafupi koma yothandiza kuti tipambane m’moyo. Anati: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.”—Salmo 1:1-3.
N’chitsimikizo chabwino bwanji chimenechi! Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro ndipo timalakwa, tidzapambana m’moyo ngati tilola Yehova kutitsogolera komanso ngati titunga kwambiri m’chitsime chija cha chisonkhezero chabwino cha mabwenzi chimene Mulungu wapereka—“abale [athu] ali m’dziko.”—1 Petro 5:9.
[Chithunzi patsamba 24]
Mpingo uli ndi chisonkhezero chabwino cha mabwenzi
[Chithunzi patsamba 25]
Makolo, limbikitsani ana anu kucheza ndi mabwenzi olimbikitsa