Musalole Mkwiyo Ukupunthwitseni
“KHAZIKITSANI mtima pansi!” “Musafulumire kunena kanthu!” “Khalani muli chete!” Kodi mawu amenewa ngodziŵika bwino kwa inu? Mwinamwake munaŵaloŵeza pamtima kuti mudekhetse kusokonezeka kwanu maganizo. Ena, mwa kuyesayesa kupeŵa kulankhula mwa ukali, amapita koyenda. Imeneyi ndi imodzi mwa njira zosavuta zochitira ndi mkwiyo ndiponso zothandiza kusunga ubwenzi ndi ena.
M’zaka zaposachedwapa, anthu ambiri akhala osokonezeka maganizo ndi malangizo owombana operekedwa ndi akatswiri ponena za kaya ngati mkwiyo uyenera kutetezeredwa kapena kuthetsedwa. Mwachitsanzo akatswiri ena azamaganizo apititsa patsogolo chiphunzitso chakuti “ngati kumakhala bwino ndi inu, tulutsani mkwiyo wanu.” Pomwe ena achenjeza kuti kulankhula mwa ukali mobwerezabwereza ndi “chochititsa champhamvu cha imfa ya mwamsanga poyerekezera ndi zochititsa zina monga kusuta fodya, BP, kuchuluka kwa cholesterol m’thupi. Mawu a Mulungu amanena mosabisa kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: Usabvutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) N’chifukwa ninji Baibulo limapereka malangizo achindunji amenewa?
Malingaliro osatetezereka amatsogolera ku mchitidwe wosalamulirika. Zimenezi zinachitika pachiyambi m’mbiri ya munthu. Timaŵerenga kuti: “Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake.” Kodi chimenechi chinam’tsogolera kuchitanji? Mkwiyo wake unamukunga ndi kumulamulira, mwakuti analimbitsa mtima wake posalabadira uphungu wa Yehova wakuti ayenera kuchita zabwino. Mkwiyo wosalamulirika wa Kaini unam’tsogolera ku tchimo lalikulu zedi—kupha mbale wake.—Genesis 4:3-8.
Mofananamo, Sauli, mfumu yoyamba ya Israyeli anakwiya pamene anamva Davide akutamandidwa kwambiri. “Ndipo akazi anathirirana mang’ombe m’kuimba kwawo, nati, Sauli anapha zikwi zake, Koma Davide zikwi zake zankhani. Koma Sauli anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira.” Mkwiyo unalamurira malingaliro a Sauli mwakuti unam’sonkhezera kuyesayesa kupha Davide. Ngakhale kuti Davide anali ndi chifuno cholimbikitsa ubwenzi wawo, Sauli sanafune kubwezeretsa mtendere ndi mgwirizano. Pambuyo pake, anataya chiyanjo chake kwa Yehova.—1 Samueli 18:6-11; 19:9, 10; 24:1-21; Miyambo 6:34, 35.
N’kosapeŵeka, kulankhula kapena kuchita zinthu zopweteketsa mitima ya ena, pamene munthu alola mkwiyo wosalamulirika kumutsogolera. (Miyambo 29:22) Kaini ndi Sauli onse anakwiya chifukwa chakuti aliyense payekha anadukidwa komanso anachita nsanje. Komabe, munthu angachite mwa ukali pa zifukwa zosiyanasiyana. Chidzudzulo chosayenera, kudzitukumula, kusamvetsetsana, ngakhalenso kuchitirana mosayenera zingayambitse kulankhula mwa ukali.
Zitsanzo za Kaini ndi Sauli zikutisonyeza chofooka chomwe chinali mwa aŵiriwa. Mwachiwonekere, Kaini analibe chikhulupiriro pa nsembe yake. (Ahebri 11:4) Kulephera kwa Sauli kumvera malamulo a Yehova ndi kudzilungamitsa kwake kunamutayitsa mwayi woyanjidwa ndi Mulungu komanso mzimu wake. Mwachionekere, amuna aŵiri awa, anafafaniza ubwenzi wawo ndi Yehova.
Mungathe kusiyanitsa zochitika zimenezo ndi zija za Davide, yemwe anali ndi chifukwa chabwino chokwiyira pamene anachitiridwa moipa ndi Sauli. Davide anadziletsa. Chifukwa ninji? Iye anati: “Mulungu andiletsa kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova.” Mwachionekere Davide analingalira za ubwenzi wake ndi Yehova, ndipo zinakhudza kachitidwe kake ndi Sauli. Anatula zonse kwa Yehova modzichepetsa. 1 Samueli 24:6, 15.
Ndithudi, zotulukapo za mkwiyo wosalamulirika ndi zoopsa. Mtumwi Paulo anachenjeza motere: “Kwiyani, koma musachimwe.” (Aefeso 4:26) Pamene kuli kwakuti mkwiyo wolungama uli ndi malo ake, nthaŵi zonse pamakhala ngozi yakuti mkwiyo ungakhale chopunthwitsa chathu. Nkosadabwitsa kuti timavutika kuti tilamulire mkwiyo wathu. Kodi tingachite zimenezo motani?
Kupanga ubwenzi wamphamvu ndi Yehova ndiyo njira yoyamba. Amakulimbikitsani kum’tsegulira mtima ndi malingaliro anu. Muuzeni nkhawa zanu ndi mavuto anu, ndipo pemphani kuti akupatseni mtima wabwino kuti mugonjetse mkwiyo. (Miyambo 14:30) Khalani otsimikizira kuti “maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo.”—1 Petro 3:12.
Pemphero lingathe kukuumbani ndi kukutsogolerani. Motani? Lingakhudze mozama kachitidwe kanu ndi ena. Kumbukirani mmene Yehova wachitira ndi inu. Monga mmene Malemba amanenera kuti, Yehova “sanatichitira monga mwa zolakwa zathu.” (Salmo 103:10) Mzimu wokhululukira ndi wofunika kuti “asatichenjerere Satana.” (2 Akorinto 2:10, 11) Ndiponso, pemphero lingatsegule mtima wanu kuti utsogozedwe ndi mzimu woyera, amene ali ndi mphamvu yokhoza kupasula nsinga m’moyo. Ndi chisangalalo, Yehova amapereka ‘mtendere wakupambana chidziŵitso chonse,’ umene ungakumasuleni ku mphamvu ya mkwiyo.—Afilipi 4:7.
Motero pemphero liyenera kugwirizana ndi kusanthula Malemba kuti “tidziŵitse chifuniro cha Ambuye n’chiyani.” (Aefeso 5:17; Yakobo 3:17) Ngati panokha zimakuvutani kulamulira mkwiyo wanu, m’pempheni Yehova kuti akuthandizeni. Werengani malemba omwe mwachindunji akugwirizana ndi kulamulira mkwiyo.
Mtumwi Paulo akutikumbutsa chinthu chofunika kwambiri kuti: “Tichitirane onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Zikani malingaliro ndi zochita zanu ku kuchitira ena zabwino. Kachitidwe kabwino, ndi koyenera kameneka kadzalimbikitsa kuchitirana chifundo ndi kukhulupirirana komanso kadzachepetsa kumvana molakwa kumene mosavuta, kungadzetse mkwiyo.
Wamasalmo anati: “Khazikitsani mapazi anga m’mawu anu; Ndipo zisandigonjetse zopanda pake ziri zonse. Akukonda chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri: Ndipo alibe chokhumudwitsa.” (Salmo 119:133, 165) Zimene zingakhalenso zoona kwa inu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]
ZOMWE TINGACHITE KUTI TILAMULIRE MKWIYO
□ Kupemphera kwa Yehova.—Salmo 145:18.
□ Kusanthula malemba tsiku ndi tsiku.—Salmo 119:133, 165.
□ Kudzitanganitsa ndi ntchito zabwino.—Agalatiya 6:9, 10.