Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 8/15 tsamba 14-19
  • Kukhala ndi Moyo Mokhulupirira Malonjezo a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala ndi Moyo Mokhulupirira Malonjezo a Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Achepetsa Zochita Zake ndi Anthu
  • Mulungu Amachita Zinthu Kuti Akwaniritse Chifuno Chake
  • Mulungu Amaona za m’Tsogolo
  • Ntchito Yomanga Yaikulu Kwambiri
  • Yehova Amachirikiza Ntchito
  • Musaleke!
  • “Anayenda Ndi Mulungu Woona”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Nowa Anayenda ndi Mulungu Woona”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Anapulumutsidwa “Pamodzi ndi Anthu Ena 7”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Chikhulupiriro cha Nowa Chimatsutsa Dziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 8/15 tsamba 14-19

Kukhala ndi Moyo Mokhulupirira Malonjezo a Mulungu

“Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.”​—YESAYA 46:9, 10.

1, 2. Kodi malingaliro ena osiyana onena za kuloŵerera kwa Mulungu m’zochitika za padziko lapansi ndi otani?

KODI Mulungu amaloŵerera kwambiri motani m’zochitika za padziko lapansi? Anthu ali ndi malingaliro osiyanasiyana. Ena amalingalira kuti iye saloŵererapo n’komwe. Atayambitsa zinthu kuyenda mwa kuzilenga, iye mwina safuna kapena sangathe kutichitira zinthu. M’lingaliro limeneli, Mulungu ali ngati atate amene amakhazika mwana wawo panjinga yatsopano naiimika bwinobwino, ndi kuikankha kuti mwana wawoyo ayambe kuyenda pa msewu. Atatero, atatewo amachokapo. Mwanayo akuchita zinthu payekha; akhoza kugwa, kapena sangagwe. Chilichonse chimene chingachitike, atatewo zawachoka.

2 Malingaliro ena ndi akuti Mulungu ndiye amachititsa kalikonse pamoyo wathu ndi kuti iye mwachindunji amaloŵerera pa chochitika chilichonse m’chilengedwe chake chonse. Komatu, ngati izi n’zoona, ena anganene kuti Mulungu amachititsa osati kokha zinthu zabwino zimene zimachitika komanso upandu ndi masoka amene akuvutitsa mtundu wa anthu. Kudziŵa choonadi cha zimene Mulungu amachita kudzatithandiza kudziŵa zimene tiyenera kuyembekezera kwa iye. Kudzalimbitsanso chikhulupiriro chathu podziŵa kuti adzakwaniritsa malonjezo ake.​—Ahebri 11:1.

3. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova ndi Mulungu wa chifuno? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani Yehova amanenedwa kuti ‘akupanga’ kapena ‘kukonza’ chifuno chake?

3 Chofunika kwambiri pa nkhani ya kuloŵerera kwa Mulungu m’zochita za anthu ndi mfundo yakuti Yehova ndi Mulungu wa chifuno. Dzina lake lenilenilo likutanthauza zimenezo. “Yehova” amatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Mwa kuchita zinthu mosalekeza, Yehova amadzipangitsa kukhala Wokwaniritsa malonjezo ake onse. Motero, Yehova akunenedwa kuti ‘akupanga,’ kapena kukonza chifuno chake cha zinthu kapena zochita za m’tsogolo. (2 Mafumu 19:25; Yesaya 46:11) Mawuŵa akuchokera ku liwu la Chihebri lakuti ya·tsarʹ, lomwe limafanana ndi liwu lotanthauza “woumba.” (Yeremiya 18:4) Monga momwe woumba waluso angakonzere tchichi ya dothi kukhala mbiya yokongola, Yehova angakonze, kapena angayendetse, zinthu kuti akwaniritse chifuno chake.​—Aefeso 1:11.

4. Kodi Mulungu anakonza motani dziko lapansi kuti anthu adzakhalepo?

4 Mwachitsanzo, Mulungu anafuna kuti dziko lapansi lidzakhale malo okongola mochititsa chidwi kuti mudzakhale anthu angwiro ndi omvera. (Yesaya 45:18) Kale kwambiri asanalenge mwamuna ndi mkazi oyamba, Yehova anawakonzekera mwachikondi. Machaputala oyambirira a buku la Genesis amalongosola mmene Yehova anakhazikitsira usana ndi usiku, mtunda ndi nyanja. Kenako analenga zomera ndi nyama. Kukonza dziko kumeneku kuti anthu adzakhalemo kunatenga zaka zikwi zochuluka. Ntchitoyo anaimaliza bwino lomwe. Mwamuna ndi mkazi oyambawo anayambira moyo wawo mu Edene, paradaiso wochititsa kaso amene anali ndi chilichonse kotero kuti iwo akanasangalala ndi moyo. (Genesis 1:31) Choncho Yehova anali kuloŵerera mwachindunji m’zochitika za padziko lapansi, akukonza ntchito zake mosalekeza kuti zifike pa chifuno chake chokwezeka. Kodi analeka kuloŵerera kwake chifukwa cha kuchulukana kwa anthu?

Yehova Achepetsa Zochita Zake ndi Anthu

5, 6. Kodi ndi chifukwa chiyani Mulungu amachepetsa zochita zake ndi anthu?

5 Ngakhale kuti ali ndi mphamvu zakuchita tero, Yehova sachititsa kapena kulamulira kalikonse pa zochita za anthu. Pali zifukwa zosachitira zimenezi. Chifukwa chimodzi ndi chakuti anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, okhala ndi ufulu wakudzisankhira, pokhala anthu aufulu. Yehova satikakamiza kuchita zimene amatiuza kuchita; ndiponso sindife zidole. (Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15) Ngakhale kuti iye amatiyembekezera kuyankha pa zimene timachita, Mulungu mwachikondi watipatsa ufulu wokwanira kusankha mmene tidzayendetsera miyoyo yathu.​—Aroma 14:12; Ahebri 4:13.

6 Chifukwa china chimene Mulungu sindiye amene amachititsa chilichonse chimene chimachitika chikukhudza nkhani imene Satana anadzutsa mu Edene. Satana anatsutsa uchifumu wa Mulungu. Anapatsa Hava chimene chinaoneka kukhala mwayi wokhala paufulu​—chimene iye ndipo kenako mwamuna wake, Adamu, analandira. (Genesis 3:1-6) Poyankha zimenezi, Mulungu walola anthu kudzilamulira kwa nthaŵi yakutiyakuti kuti zioneke ngati zimene Satana ananena zinali zoyenera. Pachifukwachi, sitinganene kuti Mulungu ndiye amachititsa zinthu zoipa zimene anthu amachita masiku ano. Ponena za anthu opanduka, Mose analemba kuti: “Anachita zovunda mwa iwo okha; saali ana [a Mulungu], chirema n’chawo.”​—Deuteronomo 32:4, 5, NW.

7. Kodi chifuno cha Yehova cha dziko lapansi ndi mtundu wa anthu ndi chotani?

7 Komabe, pamene kuli kwakuti Yehova wapatsa anthu ufulu wakusankha ndi kuyesa zinthu zosiyanasiyana podzilamulira, pa zochitika za padziko lapansi iye sanatsatire mfundo yakuti asiyeni adzionere okha, imene ikanatipatsa chiyembekezo chochepa zedi chakuti adzakwaniritsa malonjezo ake. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anapandukira uchifumu wa Mulungu, Yehova sanasinthe chifuno chake chachikondi cha dziko lapansi ndi mtundu wa anthu. Mosalephera iye adzasanduliza dzikoli kukhala paradaiso wokhalamo anthu angwiro, omvera, ndi achimwemwe. (Luka 23:42, 43) Nkhani ya mu Baibulo kuchokera ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso imalongosola mmene Yehova mosalekeza wakhala akugwirira ntchito kuti akwaniritse cholinga chimenecho.

Mulungu Amachita Zinthu Kuti Akwaniritse Chifuno Chake

8. Kodi kuloŵetsa Aisrayeli m’Dziko Lolonjezedwa kunaloŵetsamo chiyani?

8 M’zochita zake ndi mtundu wa Israyeli, Mulungu anasonyeza kuti adzakwaniritsa chifuno chake. Mwachitsanzo, Yehova anatsimikizira Mose kuti Iye adzalanditsa Aisrayeli kwa Aigupto ndi kuwaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa, dziko loyenda mkaka ndi uchi. (Eksodo 3:8) Chimenechi chinali chilengezo chofunika kwambiri ndi chopatsa chidaliro. Chinaloŵetsamo kumasula Aisrayeli​—amene analipo pafupifupi mamiliyoni atatu pamodzi ndi mabwenzi awo​—ku mtundu wamphamvu umene unakana kwamtu wagalu kuti iwo achoke. (Eksodo 3:19) M’dziko limene anali kudzaloŵetsedwamo munali kukhala mitundu yamphamvu imene ikawaletsa mwamphamvu kufikamo. (Deuteronomo 7:1) M’njira munali chipululu mmene Aisrayeli anafuna chakudya ndi madzi. Uwu ndiwo unali mkhalidwe umene unalola Yehova kusonyeza mphamvu zake zazikulu ndi Umulungu wake.​—Levitiko 25:38.

9, 10. (a) Kodi ndi chifukwa chiyani Yoswa anatha kuchitira umboni kuti malonjezo a Mulungu ndi odalirika? (b) Kodi ndi kofunika motani kuti tikhale ndi chidaliro chakuti Mulungu ali wokhoza kubwezera mphotho anthu okhulupirika kwa iye?

9 Mulungu anatulutsa Aisrayeli mu Igupto mwa zochita zamphamvu zingapo zotsatizanatsatizana. Choyamba, anakantha mtundu wa Igupto ndi miliri khumi yowononga kwambiri. Kenako, analekanitsa Nyanja Yofiira, nalola Aisrayeli kuthaŵa pamene gulu la nkhondo la Aigupto limene linali kuwalondola linathera pompo. (Salmo 78:12, 13, 43-51) Zitachitika izi, anasamalira Aisrayeli kwa zaka 40 zimene anali m’chipululu, akuwadyetsa mana, kuwapatsa madzi, ndipo ngakhalenso kuonetsetsa kuti zovala zawo sizinali kutha ndi kuti mapazi awo sanali kutupa. (Deuteronomo 8:3, 4) Aisrayeli ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawatsogolera kuti agonjetse adani awo. Yoswa, amene anali kukhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova, anali mboni yoona ndi maso ya zonsezi. Motero, iye anatha kunena mwachidaliro ndi amuna akulu a m’tsiku lake kuti: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.”​—Yoswa 23:14.

10 Mofanana ndi Yoswa wakaleyo, masiku ano Akristu ali ndi chidaliro chonse kuti Mulungu ndi wofunitsitsa ndiponso ndi wokhoza kuchitira zinthu anthu amene amamutumikira. Kukhulupirira zimenezi kuli mbali yofunika kwambiri ya chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumukondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti . . . ali wobwezera mphotho iwo akumufuna Iye.”​—Ahebri 11:6.

Mulungu Amaona za m’Tsogolo

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimatheketsa Mulungu kukwaniritsa malonjezo ake?

11 Kufika pano, taona kuti pamene kuli kwakuti Mulungu amalola ufulu wakudzisankhira ndiponso kuti anthu azidzilamulira okha, iye ali ndi mphamvu ndiponso ndi wofunitsitsa kuchita zinthu kuti akwaniritse chifuno chake. Komatu, pali chifukwa chinanso chimene chimawonjezera kukwaniritsidwa kotsimikizirika kwa malonjezo a Mulungu. Yehova amaona za m’tsogolo. (Yesaya 42:9) Mulungu kupyolera mwa mneneri wake anati: “Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.” (Yesaya 46:9, 10) Mlimi wozoloŵera ntchito yake amadziŵa nthaŵi ndiponso malo odzalapo mbewu, koma angakayikirebe mmene zinthu zidzakhalire. Komatu, “Mfumu yosatha” ili ndi chidziŵitso cholongosoka pa kuoneratu bwino lomwe nthaŵi ndi malo oti ichitirepo zinthu kuti ikwaniritse chifuno chake.​—1 Timoteo 1:17.

12. Kodi Yehova anasonyeza kudziŵiratu za m’tsogolo motani m’masiku a Nowa?

12 Talingalirani mmene Mulungu anasonyezera kudziŵiratu za m’tsogolo m’masiku a Nowa. Chifukwa cha kufalikira kwa kuipa kumene kunali padziko lonse, Mulungu anatsimikiza mtima kuthetsa mtundu wa anthu wosamverawo. Anaika nthaŵi pamene adzachita zimenezi, zaka 120 m’tsogolo. (Genesis 6:3) Poika nthaŵi yeniyeni imeneyo, Yehova analingalira zambiri kuposa chabe kuwononga oipa, chinthu chimene angachite nthaŵi ina iliyonse. Ndondomeko ya zochita za Yehova inaphatikizaponso kupulumutsa olungama. (Yerekezerani ndi Genesis 5:29.) Poti Mulungu n’ngwanzeru, anadziŵa nthaŵi yoyenera kupereka ntchito imene idzakwaniritsa cholinga chimenecho. Anapereka kwa Nowa chidziŵitso chatsatanetsatane chokwanira. Nowa anafunika kumanga chingalawa “cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake,” ndipo anthu oipa anali kudzawonongedwa ndi chigumula cha padziko lonse.​—Ahebri 11:7; Genesis 6:13, 14, 18, 19.

Ntchito Yomanga Yaikulu Kwambiri

13, 14. Kodi ndi chifukwa chiyani kumanga chingalawa inali ntchito yovuta?

13 Talingalirani za ntchito imeneyi monga momwe Nowa anali kuionera. Chifukwa chakuti Nowa anali munthu wa Mulungu, anadziŵa kuti Yehova adzawononga anthu osaopa umulungu. Komabe, zimenezi zisanachitike panali ntchito imene inafunika kugwiridwa​—ntchito imene inafuna chikhulupiriro. Kupanga chingalawa inali ntchito yaikulu kwambiri. Mulungu ananena kukula kwake. M’litali mwa chingalawacho munali motalika kuposa mabwalo ena amaseŵera a masiku ano ndipo msinkhu wake unali wautali ngati nyumba ya sanjika zisanu. (Genesis 6:15) Omanga ake anali osazoloŵera ntchitoyo komanso ochepa. Analibe zida ndi zipangizo zogwirira ntchito zapamwamba zimene zilipo masiku ano. Ndiponso, popeza kuti iye sanali ngati Yehova wokhoza kudziŵa za m’tsogolo, panalibe njira iliyonse imene Nowa akanadziŵira mikhalidwe imene ikanabuka m’kupita kwa zaka imene mwina ikanathandiza kapena ikanachedwetsa ntchito yomangayo. N’kutheka kuti Nowa anali kudzifunsa mafunso ambiri. Kodi milimo ya ntchitoyo akanaisonkhanitsa bwanji? Kodi nyama akanazisonkhanitsa bwanji? Kodi ndi chakudya chotani chimene chidzafunika ndipo chochuluka motani? Kodi Chigumula choloseredwacho chidzachitika liti kwenikweni?

14 Ndiyeno panali mikhalidwe ya anthu. Kuipa kunali ponseponse. Anefili amphamvu​—ana obadwa kwa angelo oipa ndi akazi​—anadzaza chiwawa padziko. (Genesis 6:1-4, 13) Ndiponso, ntchito yopanga chingalawa sinali ntchito yogwiridwa mwamtseri. Anthu anali kudabwa chimene Nowa anali kuchita ndipo anali kuwauza. (2 Petro 2:5) Kodi anayembekezera kuti anthuwo adzaivomereza ntchitoyo? Kutalitali! Zaka zina m’mbuyomo nthaŵiyi isanafike, Enoke wokhulupirikayo analengeza kuti oipa adzawonongedwa. Anthu sanasangalale mpang’ono pomwe ndi uthenga wake kotero kuti Mulungu “anamutenga,” kapena kuti anafupikitsa nthaŵi yake yokhala ndi moyo, mwachionekere kumuteteza kuti angaphedwe ndi adani Ake. (Genesis 5:24; Ahebri 11:5; Yuda 14, 15) Nowa anafunika osati kokha kulengeza uthenga wosakondweretsa wofananawo, komanso kupanga chingalawa. Pamene chingalawa chimenecho chinali kupangidwa, chinali chikumbutso champhamvu chakuti Nowa anali wokhulupirika pamaso pa anthu oipa a m’nthaŵi yake!

15. Kodi ndi chifukwa chiyani Nowa anali ndi chidaliro kuti akatha kugwira ntchito imene anapatsidwa?

15 Nowa anadziŵa kuti Mulungu Wamphamvuyonse anali kuchirikiza ndi kudalitsa ntchitoyo. Kodi Yehova iye mwini sindiye anamupatsa ntchitoyo? Yehova analonjeza Nowa kuti iye pamodzi ndi banja lake adzatsiriza kukonza chingalawacho nadzaloŵamo ndipo adzasungidwa amoyo pa Chigumula cha dziko lonsecho. Mulungu anachita kulumbira ndi pangano kuti asonyeze kuti anali atatsimikizadi kuchita zimenezo. (Genesis 6:18, 19) Ndithudi, Nowa anazindikira kuti Yehova anaoneratu ndiponso anaŵerengera zonse zimene zinali kuloŵetsedwamo asanapereke ntchitoyo. Ndiponso, Nowa anadziŵa kuti Yehova anali ndi mphamvu yoloŵererapo kuti amuthandize pamene anafunika kuthandizidwa. Motero chikhulupiriro cha Nowa chinamupangitsa kugwira ntchitoyo. Mofanana ndi mbadwa yake Abrahamu, Nowa ‘anakhazikika mumtima kuti, chimene [Mulungu] analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.’​—Aroma 4:21.

16. Pamene ntchito yopanga chingalawa inali mkati, kodi chikhulupiriro cha Nowa chinalimbitsidwa motani?

16 Pamene zaka zinali kupita ndipo chingalawa n’kuyamba kuoneka kumaso kwa anthu, chikhulupiriro cha Nowa chinalimba. Mavuto a kamangidwe ndi masamu ake anathetsedwa. Ziyeso zinathetsedwa. Palibe chitsutso chilichonse chimene chikanaimitsa ntchitoyo. Banja la Nowa linaona Yehova akulichirikiza ndi kuliteteza. Pamene Nowa anali kupitirizabe, ‘chiyesedwe cha chikhulupiriro chake chinachita chipiriro.’ (Yakobo 1:2-4) Pomaliza pake, anachitsiriza chingalawacho, Chigumula chinabwera, ndipo Nowa ndi banja lake anapulumuka. Nowa anaona kuti Mulungu anakwaniritsa malonjezo ake, monga momwe kenako Yoswa anadzaonera. Chikhulupiriro cha Nowa chinafupidwa.

Yehova Amachirikiza Ntchito

17. Kodi masiku athu akufanana ndi masiku a Nowa m’njira zotani?

17 Yesu analosera kuti masiku athu adzafanana ndi masiku a Nowa. Mulungu watsimikizanso mtima kuwononga oipa ndipo waika nthaŵi yochitira zimenezi. (Mateyu 24:36-39) Akuyendetsanso zinthu kuti olungama adzapulumuke. Pamene Nowa anafunika kukonza chingalawa, atumiki a Mulungu lerolino afunika kulengeza zifuno za Yehova, kuphunzitsa Mawu ake, ndi kupanga ophunzira.​—Mateyu 28:19.

18, 19. Kodi timadziŵa bwanji kuti kulalikira uthenga wabwino kukuchirikizidwa ndi Yehova?

18 Ngati Yehova sanali ndi Nowa kuti amuchirikize ndi kumulimbikitsa, sakanatha kuchipanga chingalawacho. (Yerekezerani ndi Salmo 127:1.) Mofananamo, popanda kuchirikizidwa ndi Yehova, ndi zokayikitsa kuti Chikristu choona chikanakhalapobe, kufala ndiye sichikanafala. Gamaliyeli, Mfarisi wopatsidwa ulemu ndiponso mphunzitsi wa Chilamulo, anazindikira zimenezi m’zaka za zana loyamba. Pamene Sanihedirini yachiyuda inafuna kuthana ndi atumwi, iye anachenjeza bwalolo kuti: “Lekani anthu ameneŵa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula.”​—Machitidwe 5:38, 39.

19 Kuyenda bwino kwa ntchito yolalikira, m’zaka za zana loyamba ndiponso masiku ano, kwatsimikizira kuti iyi si ntchito yopatsidwa ndi anthu, koma ndi ya Mulungu. Nkhani yotsatira idzalongosola mikhalidwe ndi zochitika zina zosangalatsa zimene zathandiza kupangitsa ntchito imeneyi kuyenda bwino kwambiri pa mlingo waukulu tere.

Musaleke!

20. Kodi ndani amene amatichirikiza pamene tikulalikira uthenga wabwino?

20 Ngakhale kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa,” tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndiye akuyendetsa zinthu ndithu. Iye akuchirikiza ndi kulimbikitsa anthu ake pamene akugwira ntchito kuti amalize kulalikira uthenga wabwino isanafike nthaŵi yoikika ya Mulungu yothetsa dongosolo loipa la zinthuli. (2 Timoteo 3:1; Mateyu 24:14) Yehova akutipempha kuti tikhale “antchito anzake.” (1 Akorinto 3:9) Ndiponso, akutitsimikizira kuti Kristu Yesu ali nafe pantchitoyi ndi kuti tingadalire chichirikizo ndi chitsogozo cha angelo.​—Mateyu 28:20; Chivumbulutso 14:6.

21. Kodi tisaleke kukhulupirira chiyani?

21 Chifukwa chakuti Nowa ndi banja lake anakhulupirira malonjezo a Yehova, anapulumutsidwa ku madzi a Chigumula. Awo amene amasonyeza chikhulupiriro chofananacho lerolino adzapulumutsidwa ku “chisautso chachikulu” chimene chikubwera. (Chivumbulutso 7:14) Tikukhala m’nthaŵi imene ilidi yosangalatsa kwambiri. Zinthu zofunika kwambiri zili m’tsogolo mwathu! Posachedwapa, Mulungu adzachitapo kanthu kuti abweretse miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene mudzakhalitsa chilungamo. (2 Petro 3:13) Musaleke, inde musasiye kukhulupirira kuti chilichonse chimene Mulungu amanena, alinso wokhoza kuchichita.​—Aroma 4:21.

Mfundo Zozikumbukira

◻ Kodi ndi chifukwa chiyani Yehova sachititsa kalikonse kamene anthu amachita?

◻ Kodi zochita za Yehova ndi Aisrayeli zinasonyeza motani kuti iye ndi wokhoza kukwaniritsa chifuno chake?

◻ Kodi m’masiku a Nowa, Yehova anasonyeza bwanji kuti amatha kuona za m’tsogolo?

◻ Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani m’malonjezo a Mulungu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena