Yehova Amakonza Njira
“Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa.”—MATEYU 24:14.
1. Kodi ndi chiyani chimene chakwaniritsidwa ndi ntchito yolalikira m’zaka za zana loyamba ndiponso la 20?
CHIFUKWA chakuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, chili chifuno chake kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Zimenezi zachititsa ndawala ya padziko lonse yolalikira ndi kuphunzitsa. M’zaka za zana loyamba, kulalikira kumeneku kunapangitsa mpingo wachikristu kukhala “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Kenako panabwera nyengo yaitali ya mpatuko pamene kuwala kwa choonadi kunachepa. M’nthaŵi za posachedwapa, mu “nthaŵi ya chimaliziro,” “chidziŵitso choona” chachulukanso, kupereka kwa anthu ochuluka chiyembekezo cha mu Baibulo cha chipulumutso chosatha.—Danieli 12:4, NW.
2. Kodi Yehova wachitanji mogwirizana ndi ntchito yolalikira?
2 Mosasamala kanthu za zoyesayesa za Satana za kulepheretsa chifuno cha Mulungu, ntchito yolalikira m’zaka za zana loyamba ndiponso la 20 yayenda bwino kwambiri. Imatikumbutsa ulosi wa Yesaya. Ponena za kubwerera ku Yuda kwa andende achiyuda m’zaka za zana la chisanu ndi chimodzi B.C.E., Yesaya analemba kuti: “Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzawongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala.” (Yesaya 40:4) Yehova wakonzanso ndi kusalaza njira ya ndawala zikuluzikulu za kulalikira za m’zaka za mazana onse aŵiri, loyamba ndi la 20.
3. Kodi Yehova ali wokhoza kukwaniritsa zifuno zake m’njira ziti?
3 Izi sizitanthauza kuti Yehova anasonkhezera mwachindunji chochitika chilichonse padziko lapansi kuti apititse patsogolo kulalikira uthenga wabwino; komanso sikuti Yehova anachita kuoneratu zimene zili m’tsogolo kuti adziŵe mwatsatanetsatane chilichonse chimene chidzachitika. Zoona, iye amatha kuoneratu ndi kukonza zinthu za m’tsogolo. (Yesaya 46:9-11) Koma amathanso kuchitapo kanthu pamene zinthuzo zikuchitika. Monga mbusa wozoloŵera ntchito yake amene amadziŵa mmene angatsogozere ndiponso mmene angatetezere nkhosa zake, Yehova amatsogolera anthu ake. Amawatsogolera kuti apulumuke, nateteza mkhalidwe wawo wauzimu ndi kuwasonkhezera kugwiritsa ntchito mikhalidwe ndi zinthu zimene zimawachirikiza kulalikira bwino uthenga wabwino padziko lonse.—Salmo 23:1-4.
Ntchito Yovuta
4, 5. Kodi ndi chifukwa chiyani kulalikira uthenga wabwino kwakhala ntchito yovuta?
4 Monga momwe kupanga chingalawa kunalili m’masiku a Nowa, m’zaka za zana loyamba ndiponso m’masiku ano ntchito yolalikira Ufumu yakhala ntchito yaikulu kwambiri. Ntchito yopereka uthenga wina uliwonse kwa anthu amitundu yonse ndi yovuta, koma ntchito iyi inalidi yovuta kwambiri. M’zaka za zana loyamba, ophunzira anali ochepa kwambiri. Mtsogoleri wawo, Yesu, anaphedwa monga munthu woganiziridwa kuti anali woukira boma. Chipembedzo cha Ayuda chinali chokhazikitsidwa bwino. Ku Yerusalemu kunali kachisi wochititsa kaso. Zipembedzo zosakhala zachiyuda m’dera la ku Mediterranean zinalinso zokhazikitsidwa bwino, zinali ndi akachisi ndi unsembe. Mofananamo, pamene “nthaŵi ya chitsiriziro” inayamba mu 1914, Akristu odzozedwa anali ochepa, ndipo anthu amene anali m’zipembedzo zina zimene zimati zikutumikira Mulungu anali ambiri.—Danieli 12:9.
5 Yesu anachenjeza otsatira ake kuti adzazunzidwa. Iye anati: “Adzakuperekani ku nsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Kuwonjezera pa mavuto otereŵa, makamaka mu “masiku otsiriza,” Akristu adzapezeka ali pakati pa “nthaŵi zoŵaŵitsa zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1, NW) Kukula kwa ntchitoyi, kuchitikadi kwa zizunzo, ndi kuvuta kwa nthaŵi zapangitsa ntchito yolalikira kukhala yosautsa ndi yovuta. Panafunika chikhulupiriro chachikulu.
6. Kodi Yehova anatsimikizira anthu ake motani kuti ntchito yawo idzayenda bwino?
6 Pamene kuli kwakuti Yehova anadziŵa kuti padzakhala mavuto, anadziŵanso kuti palibe chimene chidzalepheretsa ntchitoyo. Kuyenda bwino kwa ntchitoyi kunanenedweratu mu ulosi wodziŵika bwino umene wakwaniritsidwa modabwitsa m’zaka za zana loyamba ndiponso la 20 wakuti: ‘Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.’—Mateyu 24:14.
7. Kodi ntchito yolalikira inachitika kwa ukulu wotani m’zaka za zana loyamba?
7 Pokhala ndi chikhulupiriro ndiponso podzazidwa ndi mzimu woyera, atumiki a Mulungu m’zaka za zana loyamba anapita kukagwira ntchito yawo. Chifukwa chakuti Yehova anasonyeza kuti anali nawo, iwo anachita bwino kwambiri kuposa mmene amayembekezera. Panthaŵi imene Paulo analembera kalata Akolose, pafupifupi zaka 27 Yesu atamwalira, iye anakamba za uthenga wabwino kuti ‘unalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Mofananamo kumapeto kwa zaka za zana la 20, uthenga wabwino ukulalikidwa m’mayiko 233.
8. Kodi ambiri alandira uthenga wabwino m’mikhalidwe yotani? Perekani zitsanzo.
8 Anthu mamiliyoni ambiri alandira uthenga wabwino m’zaka za posachedwapa. Ambiri atero m’mikhalidwe yovuta—m’nthaŵi za nkhondo, chiletso, ndi chizunzo chachikulu. Zinalinso choncho m’zaka za zana loyamba. Panthaŵi ina Paulo ndi Sila anakwapulidwa mwankhanza ndi kuikidwa m’ndende. Unali mkhalidwe wokayikitsa kwambiri kuti n’kupanga ophunzira! Komatu, Yehova anagwiritsa ntchito mkhalidwe umenewowo kuchita zomwezo. Paulo ndi Sila anamasulidwa, ndipo wosunga ndende pamodzi ndi banja lake anakhala okhulupirira. (Machitidwe 16:19-33) Zokumana nazo zoterezi zimasonyeza kuti uthenga wabwino sungaletsedwe ndi aja amene amautsutsa. (Yesaya 54:17) Komabe, mbiri ya Chikristu sili kokha ndi chidani ndi chizunzo chosalekeza. Tsopano tiyeni tione zinthu zina zabwino zimene zathandiza kusalaza njira kuti kulalikira uthenga wabwino m’zaka za zana loyamba ndiponso la 20 kuyende bwino.
Mkhalidwe wa Chipembedzo
9, 10. Kodi m’zaka za zana loyamba ndi la 20, Yehova anapangitsa bwanji anthu kuyembekezera kuti uthenga wabwino udzalalikidwa?
9 Talingalirani za nthaŵi pamene ndawala za padziko lonse za kulalikira zinayamba. Ponena za zochitika za m’zaka za zana loyamba, ulosi wa masabata 70 a zaka, wopezeka pa Danieli 9:24-27, unasonya molondola chaka chimene Mesiya adzaoneka—29 C.E. Ngakhale kuti Ayuda a m’zaka za zana loyamba sanazindikire nthaŵi yeniyeni yochitikira zinthu, iwo anali kuyembekezera, anali kudikira Mesiya. (Luka 3:15) Manuel Biblique yachifalansa imati: “Anthu anadziŵa kuti masabata makumi asanu ndi aŵiri a zaka otchulidwa ndi Danieli anali kutha; panalibe amene anadabwa kumva Yohane Mbatizi akulengeza kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.”
10 Nanga bwanji za zochitika za makono? Eya, chochitika chachikulu chinali pamene Yesu anakhazikitsidwa pa mpando wachifumu kumwamba, kumene kunali kuyamba kwa kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu. Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti izi zinachitika mu 1914. (Danieli 4:13-17) Kuzindikira chochitika chimenechi kunapangitsanso anthu ena opembedza a masiku ano kuchiyembekezera. Chiyembekezo chinali kuonekanso mwa Ophunzira Baibulo oona mtima amene anayamba kufalitsa magazini ino mu 1879 monga Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence (Nsanja ya Olonda ya Ziyoni ndi Cholengeza Kukhalapo kwa Kristu). Motero, m’zaka za zana loyamba ndiponso m’masiku ano, ziyembekezo zachipembedzo zinakonza mkhalidwe wabwino wolalikiramo uthenga wabwino.a
11. Kodi ndi maziko achipembedzo otani amene anamangidwa kuthandiza kulalikira uthenga wabwino?
11 China chimene chinathandiza ntchito ya Akristu m’mazana onse aŵiri chinali chakuti anthu ambiri anali ozoloŵera Malemba Opatulika. M’zaka za zana loyamba, Ayuda anamwazikira m’mitundu ya Akunja owazungulira. Ayuda amenewo anali ndi masunagoge kumene anthu anali kupitako kaŵirikaŵiri kukamva Malemba akuŵerengedwa ndi kulongosoledwa. Motero, Akristu oyambirira anatha kumanga pa chidziŵitso chachipembedzo chimene anthu anali nacho kale. (Machitidwe 8:28-36; 17:1, 2) Kuchiyambiyambi kwa nyengo yathu ino, anthu a Yehova anasangalalanso ndi mkhalidwe wofananawo m’mayiko ambiri. Baibulo linali lofala kwambiri m’Dziko Lachikristu, makamaka m’mayiko achipolotesitanti. Linali kuŵerengedwa m’matchalitchi ambiri; anthu ochuluka anali ndi lawolawo. Baibulo linali kale m’manja mwa anthu, koma iwo anali kufunika thandizo kuti amvetsetse chimene anali nacho.
Kuthandizidwa ndi Lamulo
12. Kodi ndi motani mmene lamulo la Roma kaŵirikaŵiri linalili chitetezo m’zaka za zana loyamba?
12 Akristu polalikira kaŵirikaŵiri athandizidwa ndi malamulo aboma. Ufumu wa Roma ndiwo unali kulamulira dziko m’zaka za zana loyamba, ndipo malamulo ake olembedwa anali kukhudza kwambiri moyo watsiku ndi tsiku. Malamulo ameneŵa anali kupereka chitetezo, ndipo Akristu oyambirira anapindula nawo. Mwachitsanzo, Paulo anatulutsidwa m’ndende ndiponso sanakwapulidwe chifukwa chakuti iye anapempha kuweruzidwa mwa lamulo la Aroma. (Machitidwe 16:37-39; 22:25, 29) Kutchula zimene dongosolo la zamalamulo lachiroma linali kunena kunathandiza kutontholetsa gulu lochita chiwawa mu Efeso. (Machitidwe 19:35-41) Nthaŵi ina, Paulo anapulumutsidwa ku chiwawa mu Yerusalemu chifukwa chakuti anali nzika ya Roma. (Machitidwe 23:27) Kenako, lamulo la Roma linamulola kutchinjiriza chikhulupiriro chake mwalamulo pamaso pa Kaisara. (Machitidwe 25:11) Ngakhale kuti a Kaisara ambiri anali kulamulira mwankhanza, kaŵirikaŵiri malamulo a m’zaka za zana loyamba anali kulola “kutchinjiriza ndi kukhazikitsa uthenga wabwino mwalamulo.”—Afilipi 1:7, NW.
13. Kodi ntchito yolalikira kaŵirikaŵiri yapindula motani ndi malamulo masiku athu ano?
13 Zilinso mofananamo m’mayiko ambiri lerolino. Ngakhale kuti pakhala anthu amene ‘apanga chovuta kukhala lamulo,’ malamulo olembedwa m’mayiko ambiri amaona ufulu wa chipembedzo kukhala ufulu wofunika. (Salmo 94:20) Pozindikira kuti Mboni za Yehova sizisokoneza mtendere wa anthu, maboma ambiri aloleza ntchito yathu mwalamulo. Ku United States, kumene kumasindikizidwa zinthu zambiri za Mboni, malamulo amene aliko apangitsa kukhala kotheka kuti magazini ya Nsanja ya Olonda ikhale ikutulutsidwa mosalekeza kwa zaka 120 ndi kumaŵerengedwa padziko lonse.
Nyengo za Mtendere ndi Kulolerana
14, 15. Pamene anthu anali kukhalako mwabata m’zaka za zana loyamba, kodi zinathandiza motani ntchito yolalikira?
14 Ntchito yolalikira yathandizidwanso ndi nyengo za mtendere. Ngakhale kuti molondola Yesu analosera kuti m’nthaŵi zokhudzidwazo “mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina,” pakhala nyengo za bata zimene zatheketsa kulalikira Ufumu n’chamuna chonse. (Mateyu 24:7) Akristu a m’zaka za zana loyamba anali kukhala mu Pax Romana, kapena kuti Mtendere wa Aroma. Wolemba mbiri wina analemba kuti: “Roma anagonjetseratu anthu okhala m’dera la Mediterranean kwakuti anawathetsera nyengo za pafupifupi nkhondo zosatha.” Nyengo ya bata imeneyi inapatsa Akristu oyambirira mwayi woyenda motetezeka ndithu m’dziko lonse lolamulidwa ndi Aroma.
15 Ufumu wa Roma unkayesa kugwirizanitsa mitundu ya anthu mwa ulamuliro wake wamphamvu. Mfundo imeneyi inachirikiza osati kokha maulendo, kulolerana, ndi kupatsana nzeru, komanso lingaliro la ubale wa m’mayiko osiyanasiyana. Buku lakuti On the Road to Civilization limati: “Kugwirizana kwa Ufumu [wa Roma] kunapangitsa munda [wolalikiramo Akristu] kukhala wabwino. Malire a mayiko anachotsedwa. Nzika ya Roma inali nzika ya dziko lonse. . . . Ndiponso, boma limene linkalingalira za unzika waponseponse likanamvetsetsa chipembedzo chimene chinaphunzitsa ubale wa anthu.”—Yerekezerani ndi Machitidwe 10:34, 35; 1 Petro 2:17.
16, 17. Kodi ndi chiyani chimene chasonkhezera zoyesayesa zochirikiza mtendere m’masiku ano, ndipo kodi anthu ambiri afika pochita chiyani?
16 Bwanji m’nthaŵi yathu? M’zaka za zana la 20 mwachitika nkhondo zowononga kwambiri m’mbiri ya anthu, ndipo nkhondo zomenyedwa m’madera akutiakuti zikuulikabe m’mayiko ena. (Chivumbulutso 6:4) Komatu, pakhalabe nyengonso za kamtendere ndithu. Mayiko amphamvu kwambiri a dziko lapansi sanamenyane m’nkhondo zosonyeza chamuna chawo chonse kwa zaka zoposa 50. Mkhalidwe umenewu wathandiza kwambiri kulalikira uthenga wabwino m’mayiko amenewo.
17 Zovuta za nkhondo za m’zaka za zana la 20 zapangitsa anthu ambiri kuzindikira kufunika kwa boma la dziko lonse. Kuopa nkhondo ya dziko lonse kunachititsa anthu kupanga bungwe la League of Nations ndiponso la United Nations. (Chivumbulutso 13:14) Cholinga chimene mabungwe onse aŵiri analengeza chinali kuchirikiza m’gwirizano ndi mtendere pa dziko lonse. Anthu amene akuona kufunika kumeneku nthaŵi zambiri amamvetsera bwino uthenga wabwino wa boma la dziko lonse limene lidzabweretsa mtendere weniweni ndi wokhalitsa—Ufumu wa Mulungu.
18. Kodi ndi maganizo otani okhudza chipembedzo amene ayanja ntchito yolalikira?
18 Ngakhale kuti panthaŵi zina Akristu azunzidwa mwakhanza kwambiri, m’mazana onse aŵiri loyamba ndi la 20 lino mwakhala nthaŵi zololerana pa chipembedzo. (Yohane 15:20; Machitidwe 9:31) Aroma anatengera ndi kusinthira mosavuta ku milungu yachimuna ndi yachikazi ya anthu amene anawagonjetsa. Polofesa Rodney Stark analemba kuti: “M’zochitika zambiri Roma anali kupereka ufulu wachipembedzo wochulukirapo kusiyana ndi umene unadzaonekanso pambuyo pa Chipanduko cha Aamerica.” Masiku ano, anthu m’mayiko ambiri akumvetsera kwambiri malingaliro a ena, zimene zawachititsa kukhala ofunitsitsa kumvetsera uthenga wa m’Baibulo umene Mboni za Yehova zimapereka.
Zimene Tekinoloje Yachita
19. Kodi Akristu oyambirira anagwiritsa ntchito motani codex?
19 Pomaliza, talingalirani mmene Yehova wathandizira anthu ake kupindula ndi kupita patsogolo kwa tekinoloje. Ngakhale kuti Akristu oyambirira sanali m’nthaŵi yomwe tekinoloje inali kupita patsogolo kwambiri, chinthu china chimene anagwiritsa ntchito chinali codex, kapena kuti buku la masamba. Codex inaloŵa m’malo mwa mpukutu womwe unali wovuta kugwiritsa ntchito. Buku lakuti The Birth of the Codex (Chiyambi cha Codex) limati: “Posiyanitsa kachitidwe kochedwa ndi kapang’onopang’ono kamene codex inaloŵa m’malo mwa mipukutu m’mabuku wamba, zikuoneka kuti Akristu anayamba kuigwiritsa ntchito nthaŵi yomweyo ndiponso kulikonse.” Buku limeneli limanenanso kuti: “Kulikonse Akristu m’zaka za zana lachiŵiri anali kugwiritsa ntchito codex, moti ayenera kuti anayamba kuigwiritsa ntchito kalekale isanafike A.D. 100.” Codex inali yosavuta kugwiritsa ntchito kusiyana ndi mpukutu. Malemba anali kupezedwa mofulumira. Ndithudi zimenezi zinathandiza Akristu oyambirira amene, monga ngati Paulo, sanali kokha kulongosola Malemba komanso anali ‘kutsimikiza ndi maumboni’ zinthu zimene anali kuphunzitsa.—Machitidwe 17:2, 3, NW.
20. Kodi anthu a Mulungu agwiritsa ntchito motani tekinoloje ya masiku ano m’ntchito yolalikira padziko lonse, ndipo kodi n’chifukwa chiyani?
20 M’zana lathu lino tekinoloje yapita patsogolo kwambiri. Makina osindikizira othamanga kwambiri athandiza kuti kukhale kotheka kufalitsa mabuku a Baibulo panthaŵi imodzi m’zinenero zochuluka. Tekinoloje ya masiku ano yafulumizitsa ntchito yotembenuza Baibulo. Magalimoto, sitima zapamtunda ndi zam’madzi, ndi ndege zimatheketsa kupereka mabuku a Baibulo mofulumira m’malo osiyanasiyana padziko lonse. Matelefoni ndi ma fax machine apangitsa kulankhulana ndi wina ali kutali panthaŵi yomweyo kukhala kotheka. Kupyolera mwa mzimu wake, Yehova wasonkhezera atumiki ake kuti agwiritse ntchito mwanzeru tekinoloje yotereyi kuchirikiza kufalitsa uthenga wabwino padziko lonse. Iwo sakugwiritsa ntchito zinthu zimenezi ndi chikhumbo chofuna kudziŵa ndi kumagwiritsa ntchito zinthu zatsopano kwambiri m’dzikoli. M’malomwake, iwo amasangalatsidwa kwambiri ndi chimene chidzawathandiza kugwira bwino kwambiri ntchito yawo yolalikira.
21. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?
21 “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi,” analosera tero Yesu. (Mateyu 24:14) Monga momwe Akristu oyambirira anaonera kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu, ife lerolino tikuziona pamlingo waukulu. Mosasamala kanthu za chidani ndi kuvuta kwa ntchitoyi, nthaŵi zabwino ndi nthaŵi zoipa, pakati pa malamulo ndi maganizo omasinthasintha, mkati mwa nkhondo ndi pa mtendere, ndi pakati pa kupita patsogolo kulikonse kwa tekinoloje, uthenga wabwino wakhala ukulalikidwa ndipo uli kulalikidwabe. Kodi izi sizikudabwitsani kuti Yehova ali ndi nzeru ndiponso kuti amaoneratu za m’tsogolo mochititsa chidwi? Tingakhale otsimikiza kotheratu kuti ntchito yolalikira idzamalizidwa mogwirizana ndi ndondomeko ya zinthu ya Yehova ndi kuti chifuno chake chachikondi chidzakwaniritsidwa mopindulitsa olungama. Iwo adzalandira dziko lapansi nadzakhalamo kosatha. (Salmo 37:29; Habakuku 2:3) Ngati tigwirizanitsa miyoyo yathu ndi chifuno cha Yehova, tidzakhala mmodzi wa anthu amenewo.—1 Timoteo 4:16.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze kulongosola kwa tsatanetsatane kwa maulosi aŵiri ameneŵa a Umesiya, onani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, masamba 36, 97, ndi 98-107, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Mfundo Zobwereza
◻ Kodi ndi chifukwa chiyani kulalikira uthenga wabwino kwakhala ntchito yovuta?
◻ Kodi ntchito ya Akristu yathandizidwa motani ndi makonzedwe aboma ndiponso kukhala mwabata kwa anthu?
◻ Madalitso a Yehova pa ntchito yolalikira akutitsimikizira za zochitika za m’tsogolo zotani?