Nkhani Yovuta Kumvetsa ya Thanzi Loipa
OWMADJI WACHICHEPEREYO WATSEGULA M’MIMBA. Hawa, amayi wake, akuda nkhaŵa chifukwa cha kutayika kwa madzi a m’thupi mwake; anamva kuti khanda la msuweni wawo kumudzi, lamwalira posachedwapa mwa njira imeneyo. Agogo a Owmadji, apongozi ake a Hawa, akufuna kuti Owmadji apite naye kwa sing’anga. “Mzimu woipa ndiwo ukudwalitsa mwanayu,” iwo akutero. “Unakana kumuveka njirisi mwanayu kuti zizimuteteza, ndipo tsopano mavuto ayamba!”
ZOCHITIKA ngati zimenezi ndi zofala m’madera ambiri a dziko lapansi. Miyandamiyanda ya anthu amakhulupirira kuti mizimu yoipa ndiyo zoyambitsa zosaoneka za matenda. Kodi zimenezi n’zoona?
Chiyambi cha Kusamvetsetseka
Mwina inuyo simukhulupirira kuti mizimu yosaoneka imayambitsa matenda. Mwinanso mungadabwe kuti n’chifukwa chiyani munthu angaganize choncho, chifukwa asayansi avumbula kuti matenda ambiri amadza chifukwa cha tizilombo toyambitsa matenda. Komatu, kumbukirani kuti mtundu wa anthu sunkadziŵa za tizilombo ting’onoting’ono toyambitsa matenda timeneti. Munali m’zaka za zana la 17, Antonie van Leeuwenhoek atapanga makina oonera tizilombo ting’onoting’ono, pamene tizilombo timeneti tosaoneka ndi maso a munthu tinayamba kuoneka. Ngakhale zitatero, ndi m’zaka za zana la 19, ndi chithandizo cha zofufuza za Louis Pasteur, pamene asayansi anayamba kuzindikira kuti tizilombo ndi timene timayambitsa matenda.
Popeza kuti kwa nthaŵi yaitali m’mbiri ya anthu choyambitsa matenda chinali chosadziŵika, malingaliro ambiri okhulupirira za malodza anayamba, kuphatikizapo chiphunzitso chakuti matenda onse amayamba chifukwa cha mizimu yoipa. Buku lakuti The New Encyclopædia Britannica limafotokozapo imodzi mwa njira zimene zingakhale zitayambira. Ilo limanena kuti asing’anga akale ankagwiritsa ntchito mizu yosiyanasiyana, masamba, ndi china chilichonse chimene angachipeze, pofuna kuthandiza wodwala. Nthaŵi zina, amodzi mwa mankhwalawo amathandiza. Kenako sing’angayo amaphatikizapo zinthu zambiri zosonyeza kukhulupirira malodza m’kuchiza kwakeko. Zimenezi zimabisa mankhwala enieni amene am’chiritsa. Motero, sing’angayo amaonetsetsa kuti anthu akupitirizabe kubwera kwa iye. Mwanjira imeneyi, mankhwala anasanganikirana ndi zamalodza, mwakuti anthu ankalimbikitsidwa kudalira mphamvu ya mizimu kuti athandizidwe.
Njira zakalekale zochizira zimenezi zikugwiritsidwabe ntchito m’mayiko ambiri. Ambiri amanena kuti matenda amayambitsidwa ndi mizimu ya makolo amene anafa. Ena amanena kuti Mulungu ndiye amachititsa kuti tizidwala, ndipo matendawo ndi chilango chifukwa cha machimo athu. Ngakhale anthu ophunzira atadziŵa mmene matenda amayambikiradi m’thupi, iwo amapitirizabe kuopa mizimu.
Openda ula ndi asing’anga ena amadyerera anthu chifukwa cha mantha ameneŵa. Koma kodi tiyenera kukhulupirira chiyani? Kodi kudalira mizimu kumathandiza kusamalira thanzi? Kodi Baibulo limanenapo chiyani?