Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 9/15 tsamba 4-7
  • Alipo Amene Amasamaladi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Alipo Amene Amasamaladi
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Pali Umphaŵi ndi Kuponderezana?
  • Vuto Loti Anthu Sangalithe
  • “Kufuna Kwanu Kuchitidwe . . . Pansi Pano”
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
    Galamukani!—1998
  • Kodi Alipo Amene Angasinthedi Dzikoli?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Chitonthozo kwa Otsenderezedwa
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 9/15 tsamba 4-7

Alipo Amene Amasamaladi

ANTHU zikwizikwi amasonyeza kuti amasamaladi. Iwo sakhala ouma mtima kapena odzikonda akumaganiza kuti mavuto a anthu ena sakuwakhudza. M’malo mwake, amachita zonse zomwe angathe, nthaŵi zina amaika ngakhale miyoyo yawo pachiswe kuti achepetse mavuto a ena. Imeneyi ndi ntchito yaikulu, imene n’njovuta chifukwa cha mphamvu yaikulu imene anthu sangaigonjetse.

Zinthu ngati umbombo, andale kuchitirana ziŵembu, nkhondo, ndi masoka achilengedwe zingalepheretse ngakhale “anthu amene ali ndi chidziŵitso komanso khama lakuti athetse njala,” anatero munthu wina wogwira ntchito yothandiza anthu pamavuto. Kuthetsa njala ndi limodzi mwa mavuto ambirimbiri omwe anthu amene amasamala akukumana nalo. Iwo amalimbananso ndi zinthu ngati matenda, umphaŵi, chisalungamo ndi mavuto ena aakulu amene nkhondo imadzetsa. Koma kodi akupambana?

Mkulu wa bungwe lina lopereka thandizo kwa anthu ovutika ananena kuti, anthu amene “ali ndi chidziŵitso komanso khama” lakuti achepetse njala ndi mavuto, ali ngati Msamariya wachifundo wofotokozedwa m’fanizo la Yesu Kristu. (Luka 10:29-37) Komabe, mosasamala kanthu za zomwe angachite, iye anatero, chiŵerengero cha anthu ovutika chikuwonjezekabe. Chotero iye anafunsa kuti: “Kodi Msamariya wachifundo angatani ngati akuyenda m’njira yomweyo tsiku ndi tsiku kwa zaka zambiri ndipo amapeza munthu wovulazidwa ndi achifwamba m’mphepete mwa njira mlungu uliwonse?”

Kungakhale kosavuta kutopa ndi kungosiya, vuto lomwe likufotokozedwa kukhala ‘kutopa kwa opereka thandizo konga matenda akupha.’ Koma choyamikika n’chakuti anthu amene amasamaladi salema. (Agalatiya 6:9, 10) Mwachitsanzo, munthu wina amane analembera ku nyuzipepala ya ku Britain yotchedwa Jewish Telegraph anayamikira Mboni za Yehova zimene panthaŵi ya ulamuliro wa Nazi ku Germany “zinathandiza Ayuda zikwizikwi kupulumuka mazunzo ku Auschwitz.” “Amati chakudya chikasoŵa,” anatero wolembayo, “izo zinkagaŵana buledi wawo ndi abale ndi alongo athu [achiyuda]!” Mboni zinapitiriza kuchita chilichonse chomwe zikanatha ndi zinthu zomwe zinali nazo.

Komabe, choonadi n’chakuti kugaŵana chabe buledi sikungathetseretu mavuto a anthu. Zimenezi sizikutanthauza kunyozera zomwe anthu achifundo achita. Chilichonse chomwe chachitika kuti mavuto achepe n’chofunika. Mboni zimenezo kumlingo wakutiwakuti zinachepetsa ululu wa akaidi anzawo, ndipo ulamuliro wa Nazi m’kupita kwa nthaŵi unawonongedwa. Komabe, dongosolo la dziko lomwe limachititsa nsautso ngati zimenezo lidakalipobe, ndipo anthu osasamala alipo ambiri. Inde, “pali mbadwo mano awo akunga malupanga, zibwano zawo zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphaŵi kuwachotsa mwa anthu.” (Miyambo 30:14) Mosakayika, mukudabwa kuti n’chifukwa chiyani izi zili chomwechi.

N’chifukwa Chiyani Pali Umphaŵi ndi Kuponderezana?

Yesu Kristu nthaŵi ina anati: “Muli nawo aumphaŵi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino.” (Marko 14:7) Kodi Yesu ankatanthauza kuti umphaŵi ndi kupondereza sizidzatha mpaka kalekale? Monga anthu ena, kodi iye ankakhulupirira kuti mavuto otere ndi cholinga cha Mulungu kuti anthu achifundo athe kusonyeza mmene amasamalira ena? Kutalitali! Yesu sanakhulupirire zimenezo. Iye ankangonena mfundo yakuti umphaŵi udzakhalapobe ku utali womwe dongosolo la zinthu lilipoli lidzakhala. Komanso Yesu anadziŵa kuti: Sichinali cholinga cha Atate wake wakumwamba pachiyambi kuti padziko lapansi pakhale mavuto otere.

Yehova Mulungu analenga dziko lapansi kuti likhale paradaiso, osati malo odzazidwa ndi umphaŵi, chisalungamo, ndi kupondereza. Iye anasonyeza chisamaliro chake kwa banja la anthu mwa kupanga makonzedwe amene adzakondweretsa moyo kwambiri. Eya, tangoganizirani dzina lokhalo la munda umene makolo anthu oyamba Adamu ndi Hava anakhalamo! Unali kutchedwa Edene, kutanthauza kuti “Chikondwerero.” (Genesis 2:8, 9) Yehova sanangopatsa anthu zinthu zokha zofunika pamoyo m’malo osasangalatsa komanso osautsa. Atatha ntchito yake yolenga, Yehova anayang’anira zomwe anapanga ndipo anati zinali “zabwino ndithu.”​—Genesis 1:31.

Chabwino, bwanji nanga kuli umphaŵi, nsautso, ndi zinthu zina zobweretsa mavuto zochuluka padziko lapansi lerolino? Dongosolo loipa la zinthu lomwe lilipoli linakhalako chifukwa chakuti makolo athu oyamba anasankha kupandukira Mulungu. (Genesis 3:1-5) Zimenezi zinabutsa nkhani yakuti kaya Mulungu ali ndi ufulu wouza zolengedwa zake kuti zizimumvera kapena ayi. Chotero Yehova walola mbadwa za Adamu kudzilamulira kwakanthaŵi. Komabe, Mulungu anasamalabe zomwe zinachitika kwa mtundu wa anthu. Iye anakonza makonzedwe oti achotsenso mavuto onse omwe kupandukira iye kungabweretse. Ndipo posachedwapa, Yehova adzathetsa umphaŵi ndi nsautso, tingoti mavuto onse.​—Aefeso 1:8-10.

Vuto Loti Anthu Sangalithe

Kwa zaka mazana ambiri chilengedwere munthu, mtundu wa anthu walephereratu kufikira miyezo ya Yehova. (Deuteronomo 32:4, 5) Popitiriza kukana kwawo malamulo a Mulungu, anthu amenyana wina ndi mnzake, ndipo “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Zoyesayesa zonse zofuna kubweretsa chilungamo pakati pa anthu, kuthetsa masoka onse omwe amasautsa anthu, zalephereka chifukwa cha kudzikonda kwa anthu amene amafuna kuchita zinthu za m’mutu mwawo, m’malo mogonjera ku uchifumu wa Mulungu.

Palinso vuto lina, limene ambiri anganene kuti n’kukhulupirira malodza chabe. Woyambitsa kupandukira Mulungu akulimbikitsabe anthu kuchita zoipa ndi kudzikonda. Iye ndi Satana Mdyerekezi ndipo Yesu Kristu anamutcha iye “mkulu wa dziko ili lapansi.” (Yohane 12:31; 14:30; 2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) M’chivumbulutso cha mtumwi Yohane, Satana akudziŵika kukhala gwero lamphamvu la tsoka, yemwenso ‘akunyenga dziko lonse.’​—Chivumbulutso 12:9-12.

Mosasamala kanthu za mmene anthu angasamalire anthu anzawo, iwo sadzachotsa Satana Mdyerekezi kapena kusintha dongosolo ili limene likuwonjezera chiŵerengero cha anthu ovutika. Kodi nanga chikufunika n’chiyani kuti mavuto a mtundu wa anthu athe? Kuti izi zitheke sipafunika chabe munthu amene amasamala. M’pofunikira wina amene ali ndi chifuno komanso mphamvu zochotsera Satana ndi dongosolo lake lonse lopanda chilungamo.

“Kufuna Kwanu Kuchitidwe . . . Pansi Pano”

Mulungu akulonjeza kuti awononga dongosolo ili loipa la zinthu. Iye akufuna ndipo ali nazo mphamvu zochitira zimenezi. (Salmo 147:5, 6; Yesaya 40:25-31) Buku laulosi la Baibulo la Danieli likulosera kuti: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire,” inde, mpaka kalekale. (Danieli 2:44) Yesu Kristu ankaganiza za boma lachikhalire komanso labwino lakumwamba limeneli pamene anaphunzitsa ophunzira ake kupempha kwa Mulungu m’pemphero kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”​—Mateyu 6:9, 10.

Yehova adzayankha mapemphero otere chifukwa iye amasamaladi mtundu wa anthu. Malinga ndi kunena kwa ulosi wa pa Salmo 72, Mulungu adzapatsa mphamvu Mwana wake, Yesu Kristu, yopulumutsa aumphaŵi, ozunzika, ndi oponderezedwa amene akugwirizana ndi ulamuliro wa Yesu. Choncho, atauziridwa wamasalmo anaimba kuti: “Adzaweruza [Mfumu ya Umesiya ya Mulungu] ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphaŵi, nadzaphwanya wosautsa. . . . Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”​—Salmo 72:4, 12-14.

M’masomphenya okhudza za m’tsiku lathu, mtumwi Yohane anaona “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano,” dongosolo latsopano zedi la zinthu lokhazikitsidwa ndi Mulungu. Koma ameneŵa ndiye madalitso adzaoneni ku mtundu wa anthu ovutika! Polosera zomwe Yehova adzachita, Yohane analemba kuti: “Ndinamva mawu aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”​—Chivumbulutso 21:1-5.

Inde, tingakhulupirire mawu ameneŵa chifukwa ndi okhulupirika ndi oona. Yehova posachedwapa adzachitapo kanthu kuchotsa padziko lapansi umphaŵi, njala, opondereza, matenda, ndi chisalungamo. Monga momwe magazini ino kaŵirikaŵiri yakhala ikunenera kuchokera m’Malemba, umboni wochuluka ukusonyeza kuti tikukhala m’masiku omwe malonjezo onse ameneŵa adzakwaniritsidwa. Dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu layandikira! (2 Petro 3:13) Yehova posachedwapa, ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’​—Yesaya 25:8.

Mpaka pamene zimenezi zidzachitike, tingakhale okondwa kuti ngakhale tsopano pali anthu amene amasamaladi. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti Yehova Mulungu iyemwini amasamaladi. Posachedwapa adzachotsa nsautso zonse ndi mavuto.

Mungathe kukhala ndi chikhulupiriro cholimba m’malonjezo a Yehova. Ndipo mtumiki wake Yoswa anali nachodi. Ndi mtima wonse, Yoswa anauza anthu a Mulungu akale kuti: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.” (Yoswa 23:14) Choncho, pamene dongosolo ili la zinthu lidakalipobe, musalole ziyeso zomwe mungakumane nazo kukufooketsani. Senzetsani Yehova nkhaŵa zanu zonse pakuti iye amasamaladi.​—1 Petro 5:7.

[Zithunzi patsamba 7]

M’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu, simudzakhala umphaŵi, nsautso, matenda, ndi chisalungamo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena