Kodi Yehova Amafuna Zimene Sitingathe?
“Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—MIKA 6:8.
1. Kodi pangakhale chifukwa chotani chimene ena sakutumikirira Yehova?
PALI zimene Yehova amafuna kwa anthu ake. Koma mutaŵerenga mawu omwe ali pamwambawo a mu ulosi wa Mika, mutha kuona kuti zimene Mulungu amafuna ndi zinthu zomwe tingathe kuchita. Komabe, anthu ambiri satumikira Mlengi wathu Wamkuluyo, ndipo ena amene anali kum’tumikira asiya kutero. Chifukwa chiyani? Chifukwa amalingalira kuti Mulungu amafuna zosatheka kwa ife. Kodi n’zoona? Kapena kodi vuto limakhala ndi malingaliro a munthuyo ponena za zimene Yehova amafuna? Mbiri yakale imathandiza kumvetsa nkhaniyi.
2. Kodi Namani anali yani, ndipo mneneri wa Yehova anamuuza kuchita chiyani?
2 Namani, kazembe wankhondo wa ku Suriya anali ndi khate, koma anauzidwa kuti ku Israyeli kuli mneneri wa Yehova amene angam’chiritse. Chotero Namani ndi om’perekeza anapita ku Israyeli, ndipo kenako anafika kunyumba kwa Elisa mneneri wa Mulungu. M’malo motuluka m’nyumba mwake kuti akalandire mlendo wake wolemekezekayo, Elisa anatumiza mtumiki wake kuti akauze Namani kuti: “Kasambe m’Yordano kasanu ndi kaŵiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.”—2 Mafumu 5:10.
3. N’chifukwa chiyani poyamba Namani anakana kuchita zimene Yehova anafuna kuti achite?
3 Kuti Namani achiritsidwe nthenda yonyansayo, anayenera kuchita zimene mneneri wa Mulungu anamuuza. Chotero, kodi Yehova anali kufuna chinthu chosatheka? Iyayi. Komabe, Namani sanali kufuna kuchita zimene Yehova anafuna. Iye anatsutsa, amvekere: “Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m’Israyeli? Ndilekerenji kukasamba m’mwemo, ndi kukonzeka?” Atatero, Namani anabwerera mokwiya.—2 Mafumu 5:12.
4, 5. (a) Kodi Namani anafupidwa motani chifukwa cha kumvera kwake, ndipo anamva bwanji atafupidwa? (b) Kodi tidzapenda chiyani tsopano?
4 Kodi vuto lenileni la Namani linali chiyani? Si kuti zimene anauzidwa kuchita zinali zovuta kwambiri. Mwanzeru, anyamata a Namani anati: “Mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?” (2 Mafumu 5:13) Vuto linali ndi mmene Namani anaonera zinthu. Iye anaona kuti sanapatsidwe ulemu umene anayenera kupatsidwa ndi kuti wauzidwa kuchita zinthu zimene anaziona kukhala zopanda pake komanso zosapereka ulemu. Ngakhale zinali motero, Namani anamvera langizo la nzeru la anyamata ake ndipo anakasamba m’Mtsinje wa Yordano kasanu ndi kaŵiri. Talingalirani chisangalalo chake pamene “mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng’ono, nakonzeka”? Anali kungothokoza mumtima. Komanso, Namani ananena kuti kuyambira pamenepo, sadzalambira mulungu wina aliyense kupatulapo Yehova.—2 Mafumu 5:14-17.
5 M’mbiri yonse ya anthu, Yehova wakhala akuika malangizo amene amafuna kuti anthu ake aziŵatsatira. Tikukupemphani kuti mupende angapo mwa ameneŵa. Pamene mukuwapenda, dzifunseni kuti inuyo mukanatani ngati Yehova akanafuna kuti muchite zinthu zimenezo. Kenako, tidzapenda zimene Yehova amafuna kwa ife lerolino.
Zimene Yehova Anali Kufuna Kalelo
6. Kodi anthu aŵiri oyambirira anauzidwa kuchita chiyani, ndipo inuyo mukanatani ndi malangizo amenewo?
6 Yehova analangiza mwamuna ndi mkazi oyambawo, Adamu ndi Hava, kuti akhale ndi ana, aligonjetse dziko lapansi, ndi kulamulira nyama zonse. Mwamuna ndi mkazi wake amenewo anapatsidwanso malo okhalamo otakasuka ndiponso okongola kwabasi. (Genesis 1:27, 28; 2:9-15) Koma panali chiletso. Iwo sanayenere kudya zipatso za mtengo winawake, umodzi wokha pakati pa mitengo yambirimbiri ya zipatso m’munda wa Edene. (Genesis 2:16, 17) Kumeneko sikunali kufuna zosatheka, si choncho? Kodi inuyo simukanakonda kuchita ntchito imeneyo, podziŵa kuti mudzakhala ndi moyo kosatha ndi thanzi langwiro? Ngakhale m’mundamo mutabwera woyesa, kodi simukanatsutsa zonena zake? Ndipo kodi simukanavomereza kuti Yehova anali ndi ufulu wopereka chiletso chimodzi chaching’ono chimenecho?—Genesis 3:1-5.
7. (a) Kodi Nowa anapatsidwa ntchito yotani, ndipo anakumana ndi chitsutso chotani? (b) Kodi mukuziona motani zimene Mulungu anafuna kwa Nowa?
7 Patapita nthaŵi, Yehova anauza Nowa kumanga chingalawa kuti adzapulumukiremo pa chigumula cha padziko lonse. Popeza kuti chingalawacho chinali chachikulu zedi, ntchitoyo siinali yapafupi ndipo ayenera kuti anakumana ndi chitonzo komanso chitsutso choopsa poichita. Komabe, unali mwayi waukulu kwambiri kwa Nowa kupulumutsa banja lake, ngakhalenso nyama zambirimbiri! (Genesis 6:1-8, 14-16; Ahebri 11:7; 2 Petro 2:5) Mukanakhala kuti ndinu amene munapatsidwa ntchito imeneyo, kodi mukanalimbikira kuichita mpaka mutamaliza? Kapena kodi mukanaganiza kuti Yehova akufuna kuti muchite zinthu zimene simungakwanitse?
8. Kodi Abrahamu anapemphedwa kuchita chiyani, ndipo zimenezo zinaphiphiritsa chiyani chifukwa cha kumvera kwakeko?
8 Mulungu anapempha Abrahamu kuchita chinthu chovuta kwambiri, nati: “Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; num’pereke iye kumeneko nsembe yopsereza.” (Genesis 22:2) Popeza Yehova anali atalonjeza kuti Isake, amene panthaŵiyo analibe ana, adzakhala ndi ana, chikhulupiriro cha Abrahamu chakuti Mulungu akhoza kubwezeretsa moyo wa Isake chinayesedwa. Abrahamu atatsala pang’ono kupereka nsembe Isake, Mulungu anam’pulumutsa mnyamatayo. Chochitika chimenechi chinaphiphiritsa kuti Mulungu adzapereka Mwana wake kaamba ka anthu ndi kumuukitsa pambuyo pake.—Genesis 17:19; 22:9-18; Yohane 3:16; Machitidwe 2:23, 24, 29-32; Ahebri 11:17-19.
9. N’chifukwa chiyani Yehova sanali kufuna zoposa muyezo kwa Abrahamu?
9 Ena angaganize kuti Yehova Mulungu anali kufuna chinthu chosatheka kwa Abrahamu. Koma kodi ndi zoona? Kodi n’kusoŵadi chikondi kwa Mlengi wathu, amene angaukitse akufa, kutiuza kuti tikhalebe omvera kwa iye ngakhale ngati zimenezi zingatichititse kugona pang’ono mu imfa? Si zimene Yesu Kristu ndi otsatira ake oyambirira anaganiza. Anali okonzeka kuzunzidwa, ngakhale kufa kumene, pofuna kuchita chifuno cha Mulungu. (Yohane 10:11, 17, 18; Machitidwe 5:40-42; 21:13) Ngati zinthu zitati zikhale motero, kodi mungakhale wokonzeka kuchita zofananazo? Taonani zina mwa zinthu zimene Yehova anafuna kwa awo amene anavomera kukhala anthu ake.
Chilamulo cha Yehova kwa Israyeli
10. Kodi ndani analonjeza kuti adzachita zonse zimene Yehova angafune, ndipo iye anawapatsa chiyani?
10 Mbadwa za Abrahamu kudzera mwa mwana wake Isake ndi mdzukulu wake Yakobo, kapena kuti Israyeli, zinachuluka kufikira zinakhala mtundu wa Israyeli. Yehova analanditsa Aisrayeli ku ukapolo ku Igupto. (Genesis 32:28; 46:1-3; 2 Samueli 7:23, 24) Posapita nthaŵi, iwo analonjeza kuti adzachita zonse zimene Mulungu angafune kwa iwo. Iwo anati: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” (Eksodo 19:8) Mogwirizana ndi chikhumbo cha Aisrayeli chakuti Yehova aziwatsogolera, iye anapatsa mtunduwo malamulo oposa 600, kuphatikizapo Malamulo Khumi. M’kupita kwa nthaŵi, malamulo a Mulungu ameneŵa, amene anaperekedwa kudzera mwa Mose, anayamba kutchulidwa ndi dzina limodzi lakuti Chilamulo.—Ezara 7:6; Luka 10:25-27; Yohane 1:17.
11. Kodi cholinga cha Chilamulo chinali chiyani, ndipo ndi malamulo ena ati amene anathandiza kukwaniritsa chifunocho?
11 Cholinga chimodzi cha Chilamulo chinali kuteteza Aisrayeli mwa kupereka malamulo abwino okhudza nkhani za kugonana, malonda, ndi kusamala ana. (Eksodo 20:14; Levitiko 18:6-18, 22-24; 19:35, 36; Deuteronomo 6:6-9) Malamulo okhudza mmene ayenera kukhalira ndi anthu anzawo komanso kusamala nyama anaperekedwa. (Levitiko 19:18; Deuteronomo 22:4, 10) Zofunika zokhudza mapwando apachaka ndi kusonkhana pamodzi polambira zinathandiza kuteteza mkhalidwe wauzimu wa anthuwo.— Levitiko 23:1-43; Deuteronomo 31:10-13.
12. Kodi cholinga chachikulu cha Chilamulo chinali chiyani?
12 Cholinga chachikulu cha Chilamulo chinatchulidwa ndi mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Chinawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu [Kristu] imene adailonjezera.” (Agalatiya 3:19) Chilamulo chinali kukumbutsa Aisrayeli kuti si aungwiro. Chotero zinali zoonekeratu kuti akufunikira nsembe yangwiro imene ingachotseretu machimo awo. (Ahebri 10:1-4) Choncho Chilamulo chinakhalapo kuti chikonzekeretse anthu kulandira Yesu, amene anali Mesiya, kapena kuti Kristu. Paulo analemba kuti: “Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.”—Agalatiya 3:24.
Kodi Chilamulo cha Yehova Chinali Chotopetsa?
13. (a) Kodi anthu opanda ungwiro ankachiona motani Chilamulo, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi Chilamulo chinalidi chotopetsa?
13 Ngakhale kuti Chilamulo chinali “choyera, ndi cholungama, ndi chabwino,” ambiri ankachiona ngati chotopetsa. (Aroma 7:12) Popeza kuti Chilamulo chinali changwiro, Aisrayeli analephera kukwaniritsa miyezo yake yapamwamba. (Salmo 19:7) Ndiye chifukwa chake mtumwi Petro anachitcha kuti “goli, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife.” (Machitidwe 15:10) Komabe, Chilamulo chenichenicho sichinali chotopetsa, ndipo anthu anapindula pochitsatira.
14. Kodi ndi zitsanzo zochepa ziti zimene zikusonyeza kuti Chilamulo chinali ndi cholinga chopindulitsa kwambiri kwa Aisrayeli?
14 Mwachitsanzo, malinga ndi Chilamulo, wakuba sanali kuponyedwa m’ndende koma anayenera kugwira ntchito kuti abweze zimene anaba kuziŵirikiza kaŵiri kapena kuposapo. Chotero woberedwayo sanali kutayikidwa katundu wake, ndiponso anthu olimbikira kugwira ntchito sanali kukakamizidwa kupereka ndalama zothandizira kuyendetsa ndende. (Eksodo 22:1, 3, 4, 7) Zakudya zoyambitsa matenda zinali zoletsedwa. Ngati sinaphikidwe bwino, nyama yankhumba ingayambitse matenda a m’mimba ndi kusanza, ndipo nyama yakalulu ingayambitse matenda a mutu ndi kutentha kwa thupi. (Levitiko 11:4-12) Mofananamo, Chilamulo chinkawateteza mwa kuwaletsa kugwira nyama yakufa. Ngati munthu wakhudza mtembo, anafunikira kusamba ndi kuchapa zovala zake zonse. (Levitiko 11:31-36; Numeri 19:11-22) Zonyansa za munthu zinayenera kufotseredwa, kuletsa tizilombo toyambitsa matenda kufala, timene asayansi angotitulukira kumene m’zaka za mazana a posachedwapa.—Deuteronomo 23:13.
15. N’chiyani chimene chinali chotopetsa kwa Aisrayeli?
15 Chilamulo sichinali kufuna zinthu zosatheka kwa anthu. Koma si mmene tingafotokozere anthu amene amati ndi omasulira Chilamulo. Ponena za malamulo amene iwo anapanga, buku lotchedwa A Dictionary of the Bible, lokonzedwa ndi James Hastings, limati: “Pa lamulo lililonse la m’Baibulo anawonjezapo timalamulo tina tambirimbiri. . . . Chotero iwo ankafuna kuti nkhani ina iliyonse imene ingachitike itchulidwe m’Chilamulo, ndiponso ankafuna kulamulira khalidwe lonse la anthu mwa malamulo okhwima ndi opanda chifundo. . . . Chikumbumtima cha anthu chinaponderezedwa; mphamvu ya mawu a Mulungu inasukulutsidwa ndi kuphimbidwa ndi zimalamulo zowonjezera zosaŵerengeka.”
16. Kodi Yesu anati chiyani ponena za malamulo ndi miyambo yotopetsa ya atsogoleri achipembedzo?
16 Yesu Kristu anadzudzula atsogoleri achipembedzo amene anaika malamulo ambirimbiriwo, pamene anati: “Amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pamapeŵa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:2, 4) Iye ananena kuti malamulo ndi miyambo yawo yotopetsa, kuphatikizapo kusamba konyanyira, zinapangitsa ‘mawu a Mulungu kukhala achabe.’ (Marko 7:1-13; Mateyu 23:13, 24-26) Komabe, ngakhale Yesu asanabwere padziko lapansi, aphunzitsi achipembedzo m’Israyeli anali kuwonjeza pophunzitsa zimenedi Yehova amafuna.
Zimenedi Yehova Akufuna
17. N’chifukwa chiyani Yehova sanali kukondwera ndi nsembe zopsereza za Aisrayeli osakhulupirikawo?
17 Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng’ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.” (Yesaya 1:10, 11) N’chifukwa chiyani Mulungu sanalinso kukondwera ndi nsembe zimene iye mwini anafuna m’Chilamulo? (Levitiko 1:1–4:35) Chifukwa chakuti anthu sanali kum’patsa ulemu. Chotero, Mulungu anawachenjeza kuti: “Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa; phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.” (Yesaya 1:16, 17) Kodi zimenezi sizikutithandiza kuzindikira zimene Yehova amafuna kwa atumiki ake?
18. N’chiyani kwenikweni chimene Yehova anali kufuna kwa Aisrayeli?
18 Yesu anasonyeza zenizeni zimene Mulungu amafuna. Anasonyeza zimenezi pamene anafunsidwa funso lakuti, “Lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo?” Yesu anayankha kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini. Pa malamulo aŵa aŵiri m’pokoloŵekapo chilamulo chonse ndi aneneri.” (Mateyu 22:36-40; Levitiko 19:18; Deuteronomo 6:4-6) Mneneri Mose anatchulanso mfundo yofananayo pamene anafunsa kuti: “Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake?”—Deuteronomo 10:12, 13; 15:7, 8.
19. Kodi Aisrayeli anayesa motani kuoneka ngati opatulika, koma Yehova anawauza chiyani?
19 Mosasamala kanthu za kuchimwa kwawo, Aisrayeli ankafuna kuoneka ngati opatulika. Ngakhale kuti Chilamulo chinkafuna kuti pachaka chonse azingosala kudya pa Tsiku la Chitetezo pokha, iwo anayamba kusala kudya nthaŵi zambirimbiri. (Levitiko 16:30, 31) Koma Yehova anawadzudzula kuti: “Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse? Kodi sindiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nawo kunyumba kwako aumphaŵi otayika? Pakuona wamaliseche kuti um’veke, ndi kuti usadzibisire wekha achibale chako?”—Yesaya 58:3-7.
20. N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula anthu achipembedzo onyengawo?
20 Aisrayeli odzilungamitsawo anali ndi vuto lofanana ndi lija la anthu achipembedzo onyenga amene Yesu anawauza kuti: “Mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.” (Mateyu 23:23; Levitiko 27:30) Kodi mawu a Yesu sakutithandiza kuzindikira zimenedi Yehova amafuna kwa ife?
21. Kodi mneneri Mika anafotokoza motani mwachidule zimene Yehova amafuna kwa ife ndi zimene safuna?
21 Pofuna kumveketsa zimene Yehova amafuna kwa ife ndi zimene safuna, mneneri wa Mulungu Mika anafunsa kuti: “Ndidzafika kwa Yehova ndi chiyani, ndi kuŵerama kwa Mulungu Wam’mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi ana a ng’ombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga? Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—Mika 6:6-8.
22. Kodi n’chiyani kwenikweni chimene Yehova anali kufuna kwa anthu otsatira Chilamulo?
22 Motero, kodi n’chiyani kwenikweni chimene Yehova anafuna kwa awo amene anali kutsatira Chilamulo? N’zoona kuti anafunikira kukonda Yehova Mulungu. Komanso, mtumwi Paulo anati: “Mawu amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Agalatiya 5:14) Mofananamo, Paulo anauza Akristu a ku Roma kuti: “Iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo. . . . Chikondanocho chili chokwanitsa lamulo.”—Aroma 13:8-10.
Si Zosatheka
23, 24. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuona zimene Yehova amafuna kuti tichite kukhala zosatheka? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
23 Kodi sitikuchita chidwi poona kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, woganizira ena, ndi wachifundo? Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu, anabwera padziko lapansi kudzasonyeza bwino chikondi cha Mulungu—kudzadziŵitsa anthu kuti iwo ndi ofunika kwambiri kwa Yehova. Posonyeza chikondi cha Mulungu, Yesu anati ponena za mpheta zazing’onong’onozo: “Imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa].” Ndiye anafotokoza kuti: “Musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Ndithudi, zilizonse zimene Mulungu wachikondi ngati ameneyu afuna kwa ife sitiyenera kuziona monga kuti n’zosatheka!
24 Komabe, kodi n’chiyani chimene Yehova akufuna kwa ife lerolino? Nanga n’chifukwa chiyani ena akuoneka kuti amaganiza kuti Mulungu amafuna zimene iwo sangathe? Mwa kupeza mayankho a mafunso ameneŵa, tidzatha kuona chifukwa chimene kuchita chilichonse chimene Yehova atipempha kulili mwayi waukulu kwabasi.
Kodi Mungayankhe?
◻ N’chifukwa chiyani ena angakane kutumikira Yehova?
◻ Kodi zimene Yehova amafuna zakhala zosiyanasiyana motani m’zaka zonsezi?
◻ Kodi Chilamulo chinali ndi zolinga zotani?
◻ N’chifukwa chiyani zimene Yehova amafuna kwa ife sizili zosatheka?
[Chithunzi patsamba 18]
Malamulo opangidwa ndi anthu, monga kusamba konyanyira, apangitsa kulambira kukhala kotopetsa