Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 11/1 tsamba 7-8
  • Konzekerani Zaka Chikwi Zomwe Zili Zofunika!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Konzekerani Zaka Chikwi Zomwe Zili Zofunika!
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kulinganiza Tsopano Kaamba ka Zaka Chikwi Zikudzazo
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mutu wa Njoka Udzaphwanyidwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutso
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 11/1 tsamba 7-8

Konzekerani Zaka Chikwi Zomwe Zili Zofunika!

ULAMULIRO wa Kristu wa Zaka Chikwi udzadzetsa madalitso osaneneka kwa anthu. Pansi pa chitsogozo cha chikondi cha Yesu, mtundu wa anthu udzachotsedwa mu mkhalidwe wonyansa ulipowu ndi kuupatsa ungwiro wa ulemerero. Taganizirani chimene zimenezo zingatanthauze kwa inu. Umoyo wathanzi! Talingalirani kuti mukudzuka m’mawa uliwonse, muli wathanzi kuposa dzulo. Miyandamiyanda ya amuna, akazi, ndi ana akuyembekezera kudzakhala ndi moyo m’nthaŵi yosangalatsa imeneyo. Akuyembekezera, ndi kupempherera nthaŵiyo. Akhutira ndi zomwe aphunzira m’Baibulo kuti madalitso ameneŵa akhoza kukhala awoawo oti adzasangalale nawo.

Komabe, Yesu Kristu asanayambe Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi, ayenera kudzachotsa dziko lapansi loipali ndi onse amene amatsutsana ndi ulamuliro wake. Adzachita zimenezi pa nkhondo yomwe m’Baibulo imatchedwa Armagedo. (Chivumbulutso 16:16) Akristu enieni apadziko lapansi, sadzamenya nawo nkhondo imeneyo. Ndi nkhondo ya Mulungu. Ndipo siidzachitikira pa chigawo chimodzi chokha chadziko lapansi. Baibulo limati idzafika mbali zonse za dziko lapansi. Adani onse a ulamuliro wa Kristu, adzaphedwa. Palibe ndi mmodzi yemwe wa ameneŵa amene adzapulumuke!​—Yeremiya 25:33.

Ndipo kenako, Yesu adzathana ndi Satana Mdyerekezi pamodzi ndi ziŵanda zake. Talingalirani momwe zidzakhalire, monga mmene mlembi wa buku la Chivumbulutso anaonera: “Ndinaona mngelo [Yesu Kristu] anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdyerekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi.” (Chivumbulutso 20:1, 2) Pambuyo pake, Satana ndi ziŵanda zake adzawonongedwa kosatha.​—Mateyu 25:41.

“Khamu lalikulu, loti palibe munthu [angakhoze] kuliŵerenga” lidzapulumuka pa Armagedo. (Chivumbulutso 7:9) Kristu adzatsogolera ameneŵa kuti apindule kotheratu ndi “akasupe a madzi a moyo,” monga mmene mbusa atsogolera nkhosa zake ku madzi opatsa moyo. (Chivumbulutso 7:17) Popeza kuti Satana ndi ziŵanda zake sadzajejemetsa kupita patsogolo kwauzimu kwa anthu omwe adzapulumuke pa Armagedowo, pang’ono ndi pang’ono, adzathandizidwa kugonjetsa zizoloŵezi zawo za uchimo kufikira atakhala angwiro!

Mu ulamuliro wachikondi wa Kristu, pang’ono ndi pang’ono chikhalidwe chidzasintha. Yehova Mulungu, kudzera mwa Yesu Kristu, adzathetsa zopweteka ndi zomvetsa chisoni zonse. “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” (Chivumbulutso 21:4) Mneneri Yesaya akuphera mphongo ndi mawu akuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 35:5, 6) Ndipo akufa, “aakulu ndi aang’ono,” adzaukitsidwa ndipo sadzafanso!–Chivumbulutso 20:12.

Ngakhale tsopano, “khamu lalikulu” lomwe lidzapulumuke pa Armagedo likusonkhanitsidwa. Akukonzekera Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi. Ngakhale kuti sakudziŵa kuti ulamuliro umenewo udzayamba liti, ali ndi chidaliro kuti m’nthaŵi yoikika ya Mulungu, udzayamba. Mungakhale mmodzi wa iwo, koma inunso muyenera kukhala wokonzeka, osati mwa kugulitsa katundu wanu ndi kupanga ulendo wopita ku malo ena, koma mwa kulowetsa m’moyo wanu chidziŵitso cholongosoka cha Yehova Mulungu ndi chifuno chake kupyolera mu kuphunzira Baibulo. Popanda malipiro ena alionse kapena kukukakamizani, Mboni za Yehova mosangalala zidzakusonyezani mmene kuphunzira Baibulo kungapindulire inu ndi banja lanu. Ofalitsa magazini ino, adzakhala okondwa kukuuzani zochuluka.

[Bokosi patsamba 7]

Zaka Chikwi​—Zenizeni Kapena Zophiphiritsa?

Popeza kuti mbali yaikulu ya buku la Baibulo la Chivumbulutso inalembedwa m’chinenero chophiphiritsa, pamabuka funso lakuti. Nanga bwanji ponena za Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi wotchulidwa m’Chivumbulutso? Kodi ndi nyengo yeniyeni kapena yophiphiritsa?

Pali umboni wonse wakuti nyengo ya ulamuliro wa zaka chikwi ndi yeniyeni. Talingalirani: Mtumwi Paulo anayerekezera Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi, pamene adzaweruze mtundu wa anthu, monga tsiku limodzi. (Machitidwe 17:31; Chivumbulutso 20:4) Mtumwi Petro analemba kuti tsiku limodzi (maola 24) kwa Yehova lili ngati zaka chikwi. (2 Petro 3:8) Zimenezo zingachitire umboni kuti “tsiku” la chiweruzo limeneli ndi la utali wa zaka chikwi. Kuwonjezera pamenepo, pa Chivumbulutso 20:3, 5-7, timaŵerenga kanayi za “zaka chikwi.” Izi zikuoneka ngati zikusonyeza nyengo yautali wodziŵika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena