N’chifukwa Chiyani Anthu Akuopa Tsiku Lachiweruzo?
“KWA zaka zambiri ndithu, Akristu oumirira mwambo akhala akulosera kuti kuwonongeka [kwinakwake] kwa mitundu ya anthu kuli pafupi,” anatero Damian Thompson, wolemba nkhani zokhudza chipembedzo, m’magazini a Time. “Koma tsopano akudabwa kuti anthu sakungokhulupirira nkhanizo, koma zikufalitsidwa ndi anthu amodzimodziwo omwe ankawaseka poyamba: opanga zamakompyuta, akadaulo amalonda ndi andale.” Iye ananena motsimikiza kuti mantha akuti m’chaka cha 2000 makompyuta onse padziko lapansi adzasiya kugwira ntchito “apangitsa anthu otengeka maganizo ndi zinthu zadziko kukhala anthu okhulupirira nkhani ya zaka chikwi” amene akuopa kuyambika kwa masoka monga “kusokonezeka maganizo kwa anthu onse chifukwa cha mantha, kutha mphamvu kwa maboma, kumenyanirana chakudya, kugwa kwa ndege poomba nyumba zitalizitali za m’mizinda.”
Zimene zikuwonjezeranso mantha a anthu ndizo zochita zosoŵetsa mtendere za magulu ang’onoang’ono achipembedzo ndiponso osiyanasiyana, amene nthaŵi zambiri amawatcha kuti “okhulupirira za chiwonongeko chachikulu.” Mu January 1999, nkhani yamutu wakuti “Yerusalemu ndi Machenjezo a Chiwonongeko Chachikulu,” m’nyuzipepala ya ku France ya Le Figaro inati: “Azachitetezo [m’dziko la Israyeli] akuti pali ‘okhulupirira zaka chikwi’ oposa zana limodzi pa Phiri la Azitona kapena chapafupi amene akudikira kubweranso kwa Yesu kapena tsiku la chiweruzo.”
Buku lotchedwa 1998 Britannica Book of the Year lili ndi nkhani yapadera yokhudza “Magulu Ampatuko Okhulupirira za Tsiku Lachiweruzo Chachikulu.” Mwa magulu ena, limatchula magulu odzipha okha, monga a Heaven’s Gate, People’s Temple, ndi Order of the Solar Temple, komanso gulu la Aum Shinrikyo (Choonadi Chachikulu), limene linakonza chiwembu chopha anthu ndi mpweya wapoizoni pamalo okwerera sitima ya pansi pa nthaka ku Tokyo mu 1995, pamene anapha anthu 12 ndi kuvulaza enanso zikwi zambiri. Pomaliza nkhani yapaderayo, Martin E. Marty, mphunzitsi wamkulu wazachipembedzo pa Yunivesite ya Chicago, analemba kuti: “Kuvundukula tsamba la kalendala kupita ku chaka cha 2000 n’kochititsa nthumanzi ndipo kuyenera kuti kudzasonkhezera maulosi ndi kuyambika kwa magulu amitundumitundu. Ena angadzakhale oopsa. Idzakhala nthaŵi yosakondweretsa kuiona.”
Mmene Anthu Anayambira Kuopa Tsiku Lachiweruzo
Chivumbulutso, ndi dzina la buku lomaliza la m’Baibulo lomwe linalembedwa chakumapeto kwa zaka za m’zana loyamba C.E. Pokhala lamaulosi ndi maphiphiritso ambiri, anthu anayamba kuliyerekezera ndi mabuku amene analembedwa kalekale buku la m’Baibulo la Chivumbulutsolo lisanalembedwe. Nthano zamaphiphiritso za m’mabuku ameneŵa zinachokera ku Perisiya wakale ngakhalenso kale kuposa pamenepo. Chotero, buku la The Jewish Encyclopedia limanena za “malingaliro oonekeratu achibabulo m’nthanthi zophatikizidwa m’mabuku [achiyuda amavumbulutso] ameneŵa.”
Kuchiyambi kwa zaka zana lachiŵiri B.C.E. mpaka kumapeto kwa zaka zana lachiŵiri C.E. m’pamene mabuku amavumbulutso achiyuda anachuluka kwambiri. Polongosola chifukwa chimene anthu analembera mabuku ameneŵa, katswiri wina wa za Baibulo analemba kuti: “Ayuda anagaŵa nthaŵi yonse kukhala nyengo ziŵiri. Panali nyengo ino, imene ili yoipa yonse . . . Chotero Ayuda ankadikira kutha kwa zinthu monga momwe zilili. Panali nyengo imene ikudza imene inali kudzakhala yabwino yonseyo, nyengo ya Mulungu ya chimwemwe ndi zinthu za mwanaalirenji pamene kunali kudzakhala mtendere, kutukuka ndi chilungamo . . . Kodi nyengo ino inali kudzasintha motani kukhala nyengo imene ikudza? Ayuda ankakhulupirira kuti palibe munthu amene angapangitse kusinthako ndipo, motero, ankadikira kuloŵererapo kwa Mulungu. . . . Tsiku la kudza kwa Mulungu linali kutchedwa Tsiku la Ambuye ndipo linali kudzakhala nthaŵi yochititsa mantha kwabasi ndiponso yachiwonongeko ndi chiweruzo chosaneneka zimene zinali kudzakhala chiyambi cha nyengo yatsopano. Mabuku onse amavumbulutso amanena za zochitika zimenezi.”
Kodi Anthu Ayeneradi Kuopa Tsiku Lachiweruzo?
Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limanena za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” kapena kuti Armagedo, pamene oipa adzaphedwa, ndipo pambuyo pake padzakhala nyengo ya zaka chikwi pamene Satana adzaponyedwa m’phompho ndipo Kristu adzaweruza mtundu wa anthu. (Chivumbulutso 16:14, 16; 20:1-4) M’Nyengo Zapakati, maulosi ameneŵa anamvedwa molakwa ndi anthu ena chifukwa chakuti “Woyera” wachikatolika Augustine (354-430 C.E.) anali atanena kuti Zaka Chikwizo zinayamba Kristu atabadwa ndipo pambuyo pake panali kudzakhala Chiweruzo Chomaliza. Mwachionekere, Augustine sanaganizire kwambiri za nthaŵi, koma pamene chaka cha 1000 chinali kuyandikira, anthu anayamba kuchita mantha kwambiri. Odziŵa mbiri yakale sakugwirizana ponena za kufala kwa nkhani yoopsa yakaleyo ya tsiku lachiweruzo. Kaya nkhaniyo inali yofala motani, zinadzadziŵikabe kuti inali nkhambakamwa chabe.
Momwemonso lerolino, pali mantha ochititsidwa ndi zachipembedzo komanso ena ochititsidwa ndi zamaphunziro akuti m’chaka cha 2000 kapena cha 2001, kudzakhala tsiku lachiweruzo loopsa kwabasi. Koma kodi anthu ayeneradi kuopa? Ndipo kodi uthenga womwe uli m’buku la m’Baibulo la Chivumbulutso ndi wochititsa mantha kapena m’malo mwake kodi uwo n’ngwotipatsa chiyembekezo chabwino? Ŵerengani nkhani zotsatirazo.
[Chithunzi patsamba 4]
Mantha a anthu akale a Tsiku Lachiweruzo anali opanda pake
[Mawu a Chithunzi]
© Cliché Bibliothèque Nationale de France, Paris
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Maya/Sipa Press