Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 12/1 tsamba 14-19
  • Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la Chivumbulutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la Chivumbulutso
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mipingo Yotsogozedwa ndi Kristu
  • Kugonjera Uchifumu wa Yehova Mwachimwemwe
  • ‘Wodala Iye Amene Asunga Mawu Aŵa’
  • Mmene Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Akukukhudzirani
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Imvani Chimene Mzimu Unena ku Mipingo
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Zinthu Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 12/1 tsamba 14-19

Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la Chivumbulutso

“Wodala [“wachimwemwe,” NW] iye amene aŵerenga, ndi iwo amene akumva mawu a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo.”​—CHIVUMBULUTSO 1:3.

1. Kodi mtumwi Yohane anali mumkhalidwe wotani pamene analemba Chivumbulutso, nanga masomphenya ameneŵa anawalemberanji?

“INE Yohane, . . . ndinakhala pachisumbu chotchedwa Patmo, chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Ndi mmene zinthu zinalili pamene mtumwi Yohane ankalemba buku la Chivumbulutso. Pali malingaliro akuti anatumizidwa ku Patmo monga mkaidi mu ulamuliro wa Domitian mfumu ya Roma (81-96 C.E.), amene anakakamiza anthu kulambira mfumu nakhala wozunza Akristu. Pamene anali pa Patmo, Yohane analandira masomphenya osiyanasiyana amene anawalemba. Anawasimba, osati pofuna kuopsa Akristu oyambirirawo ayi, koma pofuna kuwalimbitsa, kuwatonthoza, ndi kuwalimbikitsa pamayesero amene anali kukumana nawo komanso amene anali patsogolo pawo.​—Machitidwe 28:22; Chivumbulutso 1:4; 2:3, 9, 10, 13.

2. N’chifukwa chiyani mkhalidwe umene Yohane ndi Akristu anzake analimo uli wochititsa chidwi kwa Akristu lerolino?

2 Mkhalidwe wa zinthu panthaŵi imene bukuli la Baibulo linkalembedwa n’ngwochititsa chidwi kwambiri kwa Akristu lerolino. Yohane anali kuzunzidwa chifukwa chakuti anali mboni ya Yehova ndi Mwana wake, Kristu Yesu. Iyeyo ndi Akristu anzake anali kuchitidwa nkhanza chifukwa chakuti, ngakhale ankachita zonse kuti akhale nzika zabwino, iwo sanali kulambira nawo mfumu. (Luka 4:8) M’mayiko ena lerolino, Akristu oona alinso mumkhalidwe wofananawo, pamene Boma limatenga ufulu wolamula zinthu zomwe zipembedzo ziyenera kuchita ndi kukhulupirira. Chotero mawu opezeka kuchiyambi kwa buku la Chivumbulutso n’ngotonthozadi. Amati: “Wodala [“wachimwemwe,” NW] iye amene aŵerenga, ndi iwo amene akumva mawu a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthaŵi yayandikira.” (Chivumbulutso 1:3) Inde, oŵerenga Chivumbulutso atcheru ndiponso omvera angapeze chimwemwe chenicheni ndi madalitso ambiri.

3. Kodi Gwero la Chivumbulutso choperekedwa kwa Yohane ndani?

3 Kodi Gwero lenileni la Chivumbulutso ndani, ndipo akugwiritsa ntchito njira iti pochipereka kwa ena? Vesi loyambirira limatiuza kuti: “Chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anam’vumbulutsira achionetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa; ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane.” (Chivumbulutso 1:1) Kunena mwachidule, Gwero lenileni la Chivumbulutso ndiye Yehova Mulungu, amene anachipereka kwa Yesu, ndipo Yesu anachipereka kwa Yohane kudzera mwa mngelo. Kufufuzanso pang’ono kukusonyeza kuti Yesu anagwiritsanso ntchito mzimu woyera popereka mauthenga ku mipingo komanso posonyeza Yohane masomphenya.​—Chivumbulutso 2:7, 11, 17, 29; 3:6, 13, 22; 4:2; 17:3; 21:10; yerekezani ndi Machitidwe 2:33.

4. Ndi njira yotani imene Yehova akugwiritsabe ntchito lerolino potsogolera anthu ake padziko lapansi?

4 Yehova akugwiritsabe ntchito Mwana wake, “mutu wa Eklesia,” pophunzitsa atumiki ake padziko lapansi. (Aefeso 5:23; Yesaya 54:13; Yohane 6:45) Yehova akugwiritsanso ntchito mzimu wake polangiza anthu ake. (Yohane 15:26; 1 Akorinto 2:10) Ndiponso monga momwe Yesu anagwiritsira ntchito “kapolo wake Yohane” popereka chakudya chauzimu cholimbitsa ku mipingo ya m’zaka za zana loyamba, lerolinonso akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wopangidwa ndi “abale” ake odzozedwa padziko lapansi, popereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake” ku banja lake ndi anzawo. (Mateyu 24:45-47; 25:40) Achimwemwetu ndi awo amene amazindikira Gwero la ‘mphatso zabwino’ zimene timalandira monga chakudya chauzimu ndi njira imene Iye akugwiritsa ntchito.​—Yakobo 1:17.

Mipingo Yotsogozedwa ndi Kristu

5. (a) Kodi mipingo yachikristu ndi oyang’anira ake akuyerekezedwa ndi chiyani? (b) Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwa anthu, kodi n’chiyani chidzatithandiza kukhala achimwemwe?

5 M’machaputala oyambirira a Chivumbulutso, mipingo yachikristu ikuyerekezedwa ndi zoikapo nyali. Oyang’anira ake akuyerekezedwa ndi angelo (amithenga) ndi nyenyezi. (Chivumbulutso 1:20)a Ponena za iyemwini, Kristu anauza Yohane kulemba kuti: “Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m’dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zagolidi.” (Chivumbulutso 2:1) Mauthenga asanu ndi aŵiri otumizidwa kumipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asia akusonyeza kuti m’zaka zana loyamba C.E., mipingoyo ndi akulu ake anali ndi mbali zomwe ankachita bwino ndi zina zomwe sanali kukhoza. N’chimodzimodzinso lerolino. Chotero, tidzakhala achimwemwe kwambiri ngati tikumbukirabe kuti Kristu, Mutu wathu, ali pakati pa mipingo. Akudziŵa bwino lomwe zomwe zikuchitika. Mophiphiritsa, oyang’anira ali “m’dzanja lake lamanja,” kunena kuti, akulamulidwa ndi kutsogozedwa ndi iye ndipo adzafunsidwa mmene akuŵetera mipingo.​—Machitidwe 20:28; Ahebri 13:17.

6. N’chiyani chikusonyeza kuti si oyang’anira okha amene adzafunsidwa ndi Kristu?

6 Komabe, kungakhale kudzinyenga kulingalira kuti ndi oyang’anira okha amene adzafunsidwa za ntchito zawo ndi Kristu. Mu uthenga wake wina, Kristu anati: “Idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.” (Chivumbulutso 2:23) Mawuwo ndi chenjezo komanso ndi chilimbikitso. Ndi chenjezo lakuti Kristu amadziŵa zolinga zathu za pansi pa mtima, ndi chilimbikitso chifukwa chakuti amatsimikizira kuti Kristu akudziŵa zoyesayesa zathu ndipo adzatidalitsa ngati tichita zonse zomwe tingathe.​—Marko 14:6-9; Luka 21:3, 4.

7. Ndi motani mmene Akristu a ku Filadelfeya ‘anasungira mawu a chipiriro cha Yesu’?

7 Uthenga wa Kristu ku mpingo wa mumzinda wa Filadelfeya, ku Lidiya ulibe chidzudzulo chilichonse, koma uli ndi pangano loyenera kutichititsa chidwi kwambiri. “Popeza unasunga mawu a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthaŵi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.” (Chivumbulutso 3:10) Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “unasunga mawu a chipiriro changa” angatanthauzenso “unasunga zimene ndinanena ponena za chipiriro.” Vesi 8 likusonyeza kuti Akristu a ku Filadelfeya sanangolabadira malamulo a Kristu koma anatsatiranso uphungu wake wakuti iwowo apirire mokhulupirika.​—Mateyu 10:22; Luka 21:19.

8. (a) Kodi Yesu analonjezanji kwa Akristu a ku Filadelfeya? (b) Kodi ndani lerolino amene akukhudzidwa ndi “nthaŵi ya kuyesedwa”?

8 Yesu ananenanso kuti adzawalanditsa mu “nthaŵi ya kuyesedwa.” Sitikudziŵa kuti mawuŵa anatanthauzanji kwa Akristu akalewo. Ngakhale kuti Domitian atamwalira mu 96 C.E. chizunzo chinadzalekeza kwakanthaŵi, funde lina lachizunzo linayambiranso mu ulamuliro wa Trajan (98-117 C.E.), limene mosakayikira linadzetsa ziyeso zowonjezeka. Koma “nthaŵi ya kuyesedwa” yaikulu ilipo mu “tsiku la Ambuye” mu “nthaŵi ya chimaliziro,” imene tikukhalamoyi. (Chivumbulutso 1:10; Danieli 12:4) Akristu odzozedwa ndi mzimu anali panthaŵi yeniyeni yakuyesedwa m’kati mwa nkhondo yoyamba ya dziko lonse ndi m’nyengo yotsatira nkhondoyo. Komabe, “nthaŵi ya kuyesedwa” idakapitirirabe. Ikukhudza “dziko lonse lapansi,” kuphatikizapo mamiliyoni a mu khamu lalikulu, amene akuyembekeza kupulumuka chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 3:10; 7:9, 14) Tidzakhalatu achimwemwe ngati ‘tisunga zimene Yesu ananena ponena za chipiriro,’ kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”​—Mateyu 24:13.

Kugonjera Uchifumu wa Yehova Mwachimwemwe

9, 10. (a) Kodi masomphenya a mpando wachifumu wa Yehova ayenera kutikhudza motani? (b) Kodi kuŵerenga kwathu Chivumbulutso kungatithandize motani kukhala achimwemwe?

9 Masomphenya operekedwa m’chaputala 4 ndi 5 a Chivumbulutso osonyeza mpando wachifumu wa Yehova ndi mabwalo ake akumwamba ayenera kutichititsa nthumanzi. Tiyenera kuchita chidwi ndi zitamando zochokera pansi pa mtima zonenedwa ndi zolengedwa zamphamvu zakumwamba pamene zikugonjera uchifumu wolungama wa Yehova mwachimwemwe. (Chivumbulutso 4:8-11) Mawu athu ayenera kumveka pakati pa awo amene akunena kuti: “Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa, zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthaŵi za nthaŵi.”​—Chivumbulutso 5:13.

10 Kwenikweni, zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kukhala ogonjera chifuniro cha Yehova mwachimwemwe pazinthu zonse. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilichonse mukachichita m’mawu kapena muntchito, chitani zonse m’dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.” (Akolose 3:17) Kuŵerenga kwathu Chivumbulutso kudzatipangitsa kukhaladi achimwemwe ngatidi m’maganizo mwathu ndi pansi pa mtima tivomereza uchifumu wa Yehova ndi kuganizira chifuniro chake pochita china chilichonse m’moyo wathu.

11, 12. (a) Kodi dongosolo la Satana lapadziko lapansi lidzagwedezedwa ndi kuwonongedwa motani? (b) Malinga n’kunena kwa Chivumbulutso 7, kodi ndani ‘adzakhoza kuima’ panthaŵiyo?

11 Kugonjera uchifumu wa Yehova mwachimwemwe ndiko maziko a chimwemwe cha munthu aliyense payekha ndi chilengedwe chonse. Posachedwapa chivomezi chachikulu chophiphiritsa chidzagwedeza dongosolo ladziko la Satana ndi maziko ake omwe ndi kuliwononga. Anthu amene amakana kugonjera boma la Ufumu wakumwamba la Kristu, lomwe likuimira ulamuliro woyenerera wa Mulungu, sadzapulumuka. Ulosiwo umati: “Mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri; nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa; chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wawo, ndipo akhoza kuima ndani?”​—Chivumbulutso 6:12, 15-17.

12 Pa funso limenelo, m’chaputala chotsatira, mtumwi Yohane akufotokoza awo amene akupanga khamu lalikulu, amene akutuluka m’chisautso chachikulu, kuti “akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 14, 15) Kuimirira ku mpando wachifumu wa Mulungu kukusonyeza kuti iwo akuzindikira mpandowo ndipo akugonjera uchifumu wa Yehova ndi mtima wonse. Choncho ali ovomerezeka.

13. (a) Kodi anthu ambiri padziko lapansi akulambira chiyani, ndipo kodi chizindikiro cha pamphumi pawo kapena padzanja lawo chikuphiphiritsa chiyani? (b) Nangano n’chifukwa chiyani padzafunikira kupirira?

13 Kwinakunso, chaputala 13 chikusonyeza okhala padziko otsalawo kuti akulambira dongosolo landale la Satana, lophiphiritsidwa ndi chilombo. Iwo akulandira chizindikiro “pamphumi” pawo kapena “padzanja” lawo, kusonyeza kuti amachirikiza dongosolo limenelo m’maganizo komanso ndi mphamvu zawo. (Chivumbulutso 13:1-8, 16, 17) Ndiyeno chaputala 14 chikuwonjezera kuti: “Ngati wina alambira chilombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pamphumi pake, kapena padzanja lake, iyenso adzamwako ku vinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m’chikho cha mkwiyo wake; . . . pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.” (Chivumbulutso 14:9, 10, 12) M’kupita kwa nthaŵi, funso lalikulu lidzakhala lakuti: Kodi muli kumbali ya yani? Kumbali ya Yehova ndi uchifumu wake kapena kumbali ya dongosolo landale losaopa Mulungu lophiphiritsidwa ndi chilombo? Achimwemwe adzakhala awo amene akupeŵa kulandira nawo chizindikiro cha chilombo ndipo amene akupirira mokhulupirika mogonjera uchifumu wa Yehova.

14, 15. Ndi uthenga wotani umene ukudukiza mafotokozedwe a m’Chivumbulutso a Armagedo, ndipo uli ndi tanthauzo lotani kwa ife?

14 Olamulira a “dziko lonse” ali pangozi yoyang’anizana ndi Yehova pankhani ya uchifumu. Mapeto a nkhaniyo adzakhala Armagedo, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Mawu owonjezera ochititsa chidwi akuonekera pakatikati pa nkhani yonena za kusonkhanitsa mafumu a dziko lapansi kuti achite nkhondo ndi Yehova. Yesu iye mwini akudukiza masomphenyawo ndi kunena kuti: “(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)” (Chivumbulutso 16:15) Mwina mawuŵa akunenedwa malinga ndi zimene zinkachitika kwa Alevi amene anali alonda a pakachisi amene anali kuvulidwa zovala ndi kuchititsidwa manyazi poyera ngati anapezeka akugona pantchito yawo yaulondayo.

15 Uthengawo n’ngwomveka: Ngati tikufuna kupulumuka Armagedo, tiyenera kukhalabe atcheru mwauzimu ndi kusunga zovala zauzimu zosonyeza kuti ndife Mboni zokhulupirika za Yehova Mulungu. Tidzakhala achimwemwe ngati tipeŵa kuwodzera kwauzimu ndi kupitirizabe mosaleka pofalitsa nawo mwachangu “Uthenga Wabwino wosatha” wa Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu.​—Chivumbulutso 14:6.

‘Wodala Iye Amene Asunga Mawu Aŵa’

16. N’chifukwa chiyani machaputala omalizira a Chivumbulutso makamaka alili opatsa chimwemwe?

16 Oŵerenga achimwemwe a buku la Chivumbulutso amasangalala kwabasi pamene aŵerenga machaputala omalizira amene amafotokoza chiyembekezo chathu chaulemerero cha kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene zikutanthauza boma lakumwamba lolungama la Ufumu lolamulira anthu atsopano, oyeretsedwa, zonse zodzetsa chitamando kwa “Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 21:22) Pamene masomphenya osangalatsa osiyanasiyanawo anali kutha, mngelo wamithengayo anati kwa Yohane: “Mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga. Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mawu a chinenero cha buku ili.”​—Chivumbulutso 22:6, 7.

17. (a) Kodi ndi chitsimikizo chotani chimene chikuperekedwa pa Chivumbulutso 22:6? (b) Kodi tiyenera kukhala atcheru kuti tipeŵe chiyani?

17 Oŵerenga Chivumbulutso achimwemwe akukumbukira bwino lomwe kuti kuchiyambi kwa “buku” limenelo kulinso mawu onga ameneŵa. (Chivumbulutso 1:1, 3) Mawu ameneŵa akutitsimikizira kuti zonse zoloseredwa m’buku lomalizirali la Baibulo ‘zidzachitika posachedwapa.’ Tili m’kati mwenimweni mwa nthaŵi yamapeto moti zochitika zazikulu zoloseredwa m’Chivumbulutso ziyenera kuchitikadi motsatizana kwambiri. Chotero, bata lomwe lingaonekere m’dongosolo la Satana siliyenera kutigonetsa tulo. Woŵerenga watcheru adzakumbukira machenjezo operekedwa m’mauthenga otumizidwa kumipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asia ndipo adzapeŵa misampha ya kukonda chuma, kulambira mafano, chisembwere, kufunda, ndi mpatuko.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ayenera kudzabe, ndipo n’chiyembekezo chotani chomwe Yohane anasonyeza chomwe ifenso tili nacho? (b) Kodi Yehova ‘azadzabe’ ndi cholinga chotani?

18 Nthaŵi zingapo, Yesu akulengeza m’buku la Chivumbulutso kuti: ‘Ndidza msanga.’ (Chivumbulutso 2:16; 3:11; 22:7, 20a) Ayenera kudzabe kudzaweruza Babulo Wamkulu, dongosolo landale la Satana, ndi anthu onse amene akukana kugonjera uchifumu wa Yehova, umene tsopano ukuchitidwa mwa Ufumu Waumesiya. Tikugwirizana ndi mtumwi Yohane ponena kuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.”​—Chivumbulutso 22:20b.

19 Yehova iyemwini akuti: “Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake.” (Chivumbulutso 22:12) Podikira mphotho yaulemerero ya moyo wosatha kaya monga mbali ya “m’mwamba mwatsopano” kapena “dziko latsopano,” tiyeni tonse tigwirizane mwachangu popereka chiitanochi kwa anthu onse oona mtima chakuti: “Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Iwonso akhale oŵerenga achimwemwe a buku louziridwa ndi lolimbikitsa la Chivumbulutso!

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku la Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, masamba 28-9, 136 (mawu amtsinde).

Mfundo Zobwereza

◻ Kodi Yehova anagwiritsa ntchito njira iti popereka Chivumbulutso, ndipo tingaphunzireponji pamenepa?

◻ N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala achimwemwe poŵerenga mauthenga otumizidwa ku mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asia?

◻ Kodi tingakhale motani otetezeka mu “nthaŵi ya kuyesedwa”?

◻ Kodi tidzakhala ndi chimwemwe chotani ngati tisunga mawu a m’buku lomwe lili ndi Chivumbulutso?

[Chithunzi patsamba 15]

Achimwemwe ndi awo ozindikira Gwero la nkhani zosangalatsa

[Chithunzi patsamba 18]

Wachimwemwe ndi munthu amene akhalabe maso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena