Khirisimasi—N’chifukwa Chiyani Imachitikanso M’mayiko a Kummaŵa?
CHIKHULUPIRIRO chakale cha Kummaŵa chimatikumbutsa za Santa Claus wa Khirisimasi. Tikunena za chikhulupiriro cha ku Korea mwa winawake wotchedwa Chowangshin, ndipo china chofananacho tingachipeze pakati pa anthu ena a ku China ndi ku Japan.
Chowangshin ankati ndi mulungu woyang’anira za kukhichini, mulungu wamoto yemwenso ankalambiridwa nawo polambira moto mu Korea wakale. (M’nthaŵi zakale, anthu a ku Korea ankanyamula makala onyeka mosamala kwambiri, ndi kuonetsetsa kuti sakuzirala.) Ankakhulupirira kuti mulungu ameneyu anali kuyang’anira khalidwe la a m’banja kwa chaka chathunthu, ndipo pambuyo pake amapita kumwamba potulukira m’chitofu ndi m’chumuni cha m’khichini.
Akuti Chowangshin amakaonekera kwa mfumu ya kumwamba patsiku la 23 la mwezi wa December. Ankayembekezereka kubwerera kumapeto a chakacho akumadutsiranso pa chumuni ndi pa chitofu pomwepaja, atatenga mphatso ndi ziweruzo za wina aliyense mogwirizana ndi khalidwe lake. Tsiku la kubwerera kwake litafika, a m’banjamo anali kuyatsa makandulo m’khichini ndi pena paliponse m’nyumbamo. Zithunzi za mulungu wam’khichini ameneyo zili ndi chinachake chofanananso ndi zithunzi za Santa Claus, anam’jambula atavala zofiira! Mwambo wa ku Korea unali wakuti mpongozi amayenera kuluka masokosi aŵiri a mapangidwe a ku Koreako, ndi kuwapereka kwa apongozi ake aakazi pa nyengo ya chisanu. Ankachita zimenezo posonyeza kuti akufunira apongozi akewo moyo wautali, popeza kuti pambuyo pa deti limenelo masiku amakhala ataliatali.
Kodi simukuona kufanana kulikonse pakati pa mfundo zomwe zatchulidwa pamwambazi ndi Khirisimasi? Nkhani ndi miyambo yake n’zofanana: chumuni, makandulo, kupereka mphatso, masokosi, mwamuna wokalamba wovala zofiira, ndi tsiku laphwando. Komabe, kufanana koteroko sindiko kokha kumene kunachititsa kuti anthu alolere kumachita Khirisimasi m’Korea. Kukhulupirira Chowangshin kunali kutangotsala pang’ono kutheratu pamene kwanthaŵi yoyamba Khirisimasi imafika m’Korea. Ndithudi, anthu ambiri a ku Korea lerolino sadziŵa n’komwe kuti kunalinso chikhulupiriro choterocho.
Ngakhale zili choncho, izi zikusonyeza mmene miyambo yokhudza nyengo ya chisanu ndi kutha kwa chaka inafalira padziko lonse m’njira zosiyanasiyana. M’zaka zana lachinayi C.E., tchalitchi chomwe chinalipo panthaŵiyo mu Ufumu wa Roma chinasintha dzina la Saturnalia, madyerero akunja achiroma okondwerera kubadwa kwa mulungu dzuwa, n’kulipanga kukhala mbali ya Khirisimasi. Pa phwando la Khirisimasi m’pomwe ankasinthira miyambo yawo ndi kuipatsa dzina lina. Kodi zimenezo zinali zotheka motani?
Tanthauzo la Kupereka Mphatso
Kupereka mphatso ndi mwambo umodzi womwe sunazimirike. Kwanthaŵi yaitali, anthu a m’Korea apeza chimwemwe chochuluka m’kupereka ndi kulandira mphatso. Chimenechi chinali chifukwa chimodzi chotchukitsira phwando la Khirisimasi mu Korea.
Nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse itatha, asilikali a ku United States omwe ankakhala mu Korea ankafuna kulimbikitsa ubale wawo ndi anthu, chotero kwa iwo, matchalitchi anali malo okumanako ndi kugaŵa mphatso ndi zithandizo. Kwenikweni pa Tsiku la Khirisimasi m’pomwe zimenezi zinkachitika. Ana ambiri ankapita m’matchalitchi pongofuna kukaona zomwe zinali kuchitika, ndipo akafika kumeneko kwanthaŵi yoyamba anali kulandira mphatso za chokoleti. Monga mukudziŵa, ambiri a iwo anayamba kuyembekezera Khirisimasi ina mwachidwi.
Kwa ana oterowo, Santa Claus anali msilikali wachimereka wovala chipeŵa choluka chofiira kumutu kwake. Miyambo 19:6 amati: “Yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.” Inde, kupereka mphatso kunalidi kwabwino zedi. Koma monga momwe mungaonere m’vesilo, mphatso zoterozo sindizo zimene zimamanga ubwenzi wokhalitsa. Ngakhalenso mu Korea, muli anthu ambiri amene anayamba kupita kutchalitchi ali aang’ono kuti akangodya chokoleti basi. Komano, Khirisimasi sinaiŵalike. Pamene chuma chinali kupita patsogolo mofulumira m’Korea, amalonda nawo anachuluka, ndipo kupatsana mphatso za Khirisimasi inali njira yachidule yokopera makasitomala ambiri. Mabizinesi anapezerapo mwayi pa Khirisimasi wopeza mapindu ochuluka.
Zimenezi zakusonyezani chifukwa chake Khirisimasi imachitika lerolino m’mayiko a Kummaŵa. Zinthu zatsopano zimapangidwa ndi cholinga choti kugula katundu pa Khirisimasi kusadzadukize panjira. Kukonzekera kutsatsa malonda kumayamba m’kati mwa chilimwe. Katundu yemwe amagulitsidwa kumapeto kwa chaka amakhala wochuluka kwambiri chifukwa chakuti anthu amagula mphatso za Khirisimasi, makadi, ndi matepi anyimbo. Ndithudi, kutsatsa malonda kungasautse wachinyamata ngati iye wakhala panyumba ndipo sakulandira mphatso ina iliyonse usiku wotsatizana ndi tsiku la Khirisimasi!
Pamene Tsiku la Khirisimasi liyandikira, masitolo ndi malo azamalonda mu Seoul amadzaza ndi anthu ofuna kukagula mphatso, ndipotu zimenezi zikuchitika m’mizinda inanso ya m’mayiko a Kummaŵa. Magalimoto amachuluka kwambiri m’misewu. Mahotela, m’madera ochitira malonda, malesitilanti ndi malo osangalalira nthaŵi ya usiku amakhala odzaza ndi makasitomala. Phokoso la chikondwerero, kuimba mokweza, zimamveka. M’kati mwa usiku wotsatizana ndi tsiku la Khirisimasi, amuna ndi akazi oledzera amakhala akuyenda modzandira m’misewu yomwe imangokhala zinyalala zili mbwee.
Ndi mmenetu Khirisimasi imakhalira. Kummaŵa, Khirisimasi silinso tchuthi chotsogozedwa ndi odzinenera kukhala Akristu. N’chachidziŵikire kuti ku Korea, monganso kwina kulikonse, azamalonda ndiwo akupindula kwambiri ndi tchuthi cha Matchalitchi Achikristu chimenechi. Chotero, kodi azamalonda n’ngoyenera kuimbidwa mlandu woyambitsa Khirisimasi yomwe n’njolekana kotheratu ndi mzimu wa Kristu? Akristu oona afunikira kufufuza mwakuya nkhani yaikulu yoloŵetsedwamo.
Chiyambi cha Khirisimasi
Nyama yakuthengo yomwe yatsekeredwa mu mpanda kumalo osungirako nyama zakuthengo n’chilombo ndithu. Ndipotu kungakhale kuika moyo pangozi kukhulupirira kuti ingathe kukhalira limodzi ndi anthu kokha chifukwa chakuti yakhala mu mpandamo kwa kanthaŵi ndipo ikuoneka kuti ikusangalala ndi ana ake. Mwinatu inu munamvapo nkhani yakuti wogwira ntchito kumalo osungira nyama zakuthengo wavulazidwa ndi zinyamazo.
M’njira zina tinganene zambiri zofananazo zokhudza phwando la Khirisimasi. Poyambirira inali “chilombo” chokhala kunja kwa Chikristu. Buku lakuti The Christian Encyclopedia (la m’Chikoreya)a pamutu waung’ono wakuti “Relation to the Roman Saturnalia,” (Kugwirizana Kwake ndi Phwando Lachiroma la Saturnalia) likulongosola motere ponena za Khirisimasi:
“Mapwando achikunja a Saturnalia ndi Brumalia anali ozikika mwamphamvu pamwambo wotchuka kwambiri moti Akristu sanathe kuwanyalanyaza. Kuvomerezedwa kwa Sunday (tsiku la Phœbus ndi Mithras komanso Tsiku la Ambuye) ndi mfumu Constantine . . . kuyenera kuti n’komwe kunatsogolera Akristu a m’zaka zana lachinayi kulingalira kuti n’koyenerera kupanga tsiku la kubadwa kwa Mwana wa Mulungu ndi la kubadwa kwa dzuwa lenilenilo kukhala limodzi. Madyerero achikunja ndi chikondwerero chake chaphokoso lomkitsa ndi kusangalala zinali zofala zedi mwakuti Akristu anali okondwa kumva kuti ayenera kupitirizabe madyerero achikunjawo mwa kungowasintha pang’ono kaonedwe kapena kachitidwe kake.”
Kodi mukuganiza kuti zimenezo zinangochitika popanda kutsutsa kulikonse? Insaikulopediya imodzimodziyo inati: “Alaliki achikristu a Kumadzulo ndi a ku Nearer East anatsutsa chiphwete chosayenerera chomwe amasangalalira nacho phwando la tsiku lakubadwa kwa Kristu, pomwe Akristu a ku Mesopotamia anadzudzula abale awo a Kumadzulo chifukwa chopembedza mafano ndi kulambira dzuŵa popanga madyerero achikunja ameneŵa kukhala achikristu.” Ndithudi, chinachake chinalakwika kuchokera pachiyambi pomwe. “Komabe madyererowo anafala mwamsanga ndithu ndipo pambuyo pake anakhazikika mwakuti ngakhale mpatuko wa Apulotesitanti wa m’zaka zana la khumi ndi zisanu ndi chimodzi sunakhoze kuwathetsa,” inatero Insaikulopediyayo.
Inde, madyerero a mulungu dzuŵa, omwe sanali mbali ya Chikristu choona, analandiridwa m’tchalitchi chofala. Anawapatsa dzina lina, komabe zochitika zake zachikunjazo sizinasinthe. Ndipo anathandiza kuloŵetsa chikunja m’matchalitchi odzitcha achikristu ndi kuipitsa mikhalidwe yauzimu wa anthu. Mbiri yakale imatsimikizira kuti pamene Gawo la Matchalitchi Achikristu linali kukula, maganizo oyambirira akuti “kondanani nawo adani anu” analoŵedwa m’malo ndi makhalidwe oipa ndi nkhondo zoopsa.
Patapita nthaŵi, zinadziŵikiratu kuti mosasamala kanthu za dzina lake lachinyengolo, Khirisimasi imasonyezabe chiyambi chake chachikunja chodzala ndi chikondwerero chaphokoso, kumwa mopambanitsa, kuchita madyerero, kuvina, kupatsana mphatso, ndi kukongoletsa m’nyumba ndi mitengo yosayoyoka masamba. Pofuna kukwaniritsa cholinga chachikulu cha amalonda, chomwe ndi kugulitsa katundu wambiri, Khirisimasi aigwiritsa ntchito mulimonse mmene akanathera. Ofalitsa nkhani amaitamanda; anthu amasangalala zedi. M’chigawo chamalonda mumzinda wa Seoul, sitolo ina yomwe imagulitsa zovala zam’kati inaulutsa nkhani pawailesi yakanema mwa kungoonetsa m’mazenera ake mtengo wa Khirisimasi wokongoletsedwa ndi zovala zam’kati zokhazokha. Mzimu wa Khirisimasi unali kuonekera, komano chizindikiro cha kulandira Kristu sichinali kuoneka.
Kuona Khirisimasi Mwamalemba
Kodi tikuphunziranji pa mbiri ndi chiyambi choterocho? Ngati mabatani amalaya amangidwa mosemphanitsa poyamba penipeni, njira yokha yabwino yokonzeranso ndiyo kuyambiranso kumangako. Kodi sizoona zimenezo? Mosasamala kanthu kuti n’zoona, ena akunena kuti ngakhale kuli kwakuti maziko ake n’ngachikunja a kulambira dzuŵa, Khirisimasi yavomerezedwa ndi Matchalitchi Achikristu. Chotero amalingalira kuti tchuthi chimenecho anachidalitsa monga tsiku la kubadwa kwa Kristu ndi kuchipanga kukhala ndi tanthauzo latsopano.
Tingapeze phunziro lofunika kwambiri pachochitika chosaiŵalika chomwe chinachitika mu dziko la Yuda lakale. M’chaka cha 612 B.C.E., Ayuda anayambitsa kulambira kwachikunja kwa dzuŵa m’kachisi wa mu Yerusalemu. Kodi kulambira kwachikunja kumeneko kunayeretsedwa chifukwa choti anakuchitira m’malo opatulidwira kulambira koyera kwa Yehova Mulungu? Wolemba Baibulo Ezekieli analemba za kulambira dzuwa komwe kunali kuchitikira pakachisi wa ku Yerusalemu kuti: “Taonani, pa khomo la kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi aŵiri mphambu asanu . . . [a]kuyang’ana kummaŵa, napembedza dzuwa kummaŵa. Ndipo anati kwa ine, wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwawo.”—Ezekieli 8:16, 17.
Inde, m’malo moyeretsedwa, kulambira kwachikunja kumeneko kunaika kachisi yenseyo pangozi. Zochitika zoterezi zinafalikira m’Yuda ndi kupangitsa ziwawa ndi kuwonongeka kwa mikhalidwe yabwino m’dziko limenelo kuchuluka. Zilinso chimodzimodzi m’Gawo la Matchalitchi Achikristu, momwe mchitidwe umene unayamba ndi kulambira dzuŵa kwa Saturnalia umafika pachimake pa Khirisimasi. Chochititsa chidwi n’chakuti patangopita zaka zoŵerengeka Ezekieli ataonetsedwa masomphenya amenewo, Yerusalemu analandira chiweruzo cha Mulungu—anawonongedwa ndi Ababulo.—2 Mbiri 36:15-20.
Mwinamwake katswiri wamaphunziro wa ku Korea, wotchulidwa m’nkhani yoyamba uja, wakuseketsani ndi momwe wam’longosolera mwanayo Yesu. Koma zoona zake n’zakuti, popeza kuti walongosolayo ndi munthu wopanda chidziŵitso cholongosoka cha Kristu, kaonedwe kakeko n’koyenera kukaganizira ndithu. Zingapangitse anthu omwe amakondwerera Khirisimasi kuganiza mwakuya. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Khirisimasi imalephereratu kum’sonyeza Yesu molondola. Ndithudi, iyo siimasonyeza momwedi iye alili lerolino. Yesu saalinso mwana wogonekedwa m’chodyera cha ng’ombe.
Mobwerezabwereza, Baibulo limatsimikizira kuti Yesu tsopano ndi Mesiya, Mfumu yamphamvu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 11:15) Ali wokonzeka kuthetsa umphaŵi ndi mavuto zomwe sizinaiŵalike kwa anthu ena pomwe amapereka mphatso panyengo ya Khirisimasi ku mabungwe othandiza osoŵa.
Kunena zoona, Khirisimasi siinapindulitse mayiko amene ali m’Gawo la Matchalitchi Achikristu kapena mayiko ena alionse, kuphatikizanso a Kummaŵa. M’malo mwake, yachotsa chidwi mu uthenga woona wachikristu wonena za Ufumu wa Mulungu ndi mapeto a dongosolo loipa lamakono lino. (Mateyu 24:14) Tikukupemphani kufunsa Mboni za Yehova za momwe mapeto amenewo adzakhalira. Ndipo adzakuuzani za madalitso osatha omwe panthaŵiyo adzaperekedwa padziko lapansi, pansi pa chitsogozo cha Ufumu wa Mulungu ndi Mfumu yomwe ikulamulira, Yesu Kristu.—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
a Lozikidwa pa buku lakuti The New Schaff-Herzog Encyclopedia of Religious Knowledge.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Khirisimasi inathandiza kuloŵetsa miyambo yachikunja m’matchalitchi odzitcha achikristu
[Chithunzi patsamba 5]
Ana ambiri ankapita m’matchalitchi pongofuna kudziŵa chomwe chimachitika kumeneko ndi kukalandira mphatso za chokoleti. Ndiyeno anayamba kuyembekezera Khirisimasi inanso
[Chithunzi patsamba 7]
Usiku wotsatizana ndi tsiku la Khirisimasi mu mzinda wa Seoul, m’Korea
[Chithunzi patsamba 8]
Kristu salinso mwana koma tsopano ndi Mfumu yamphamvu ya Ufumu wa Mulungu