Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 12/15 tsamba 14-19
  • Tisabwerere Kuloŵa Kuchitayiko!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tisabwerere Kuloŵa Kuchitayiko!
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko Kumatanthauza
  • Mmene Akristu Anapanikizidwira Kuti Abwerere
  • Chifukwa Chake Sayenera Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko
  • Chifukwa Chake Sitiyenera Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko
  • Tikhaletu iwo Achikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Musaleme Kuthamanga Makani a Moyo!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Chenjerani ndi Kusakhulupirira
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Muziyamikira Mwayi Wanu Wolambira M’kachisi Wauzimu wa Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 12/15 tsamba 14-19

Tisabwerere Kuloŵa Kuchitayiko!

“Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko.”​—AHEBRI 10:39.

1. Kodi ndi zochitika zotani zimene zinapangitsa mtumwi Petro kugwidwa ndi mantha?

ATUMWI ayenera kuti anadabwa kwambiri pamene Ambuye wawo wokondedwa, Yesu, anawauza kuti onse adzabalalika kum’siya. Kodi zimenezi zingatheke bwanji makamaka panthaŵi imene adzafunikira chichirikizo kwambiri ngati imeneyi? Petro ananena motsimikiza kuti: “Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iyayi.” Zoonadi, Petro anali mwamuna wolimba mtima. Koma pamene Yesu anaperekedwa ndi kumangidwa, atumwiwo, ndi Petro yemwe, anabalalika. Pambuyo pake, pomwe Yesu ankafunsidwa m’nyumba ya Kayafa Mkulu wa Ansembe, Petro sanachoke msanga ndipo anali m’bwalo la nyumbayo. Mkati mwa usiku wozizirawo, Petro ayenera kuti anayamba kuopa kuti Yesu ndi aliyense wogwirizana naye adzaphedwa. Pamene anthu ena amene anali pafupi anazindikira Petro kuti ndi mmodzi wa anzake a Yesu, mantha anam’gwira. Katatu konse anakana zoti ndi mnzake wa Yesu. Petro anakananso n’zoti amam’dziŵa n’komwe!​—Marko 14:27-31, 66-72.

2. (a) N’chifukwa chiyani mantha a Petro usiku womwe Yesu anamangidwa sanam’pangitse kukhala wa “iwo obwerera”? (b) Kodi tiyenera kutsimikizira m’mtima kuti chiyani?

2 Imeneyotu inali nthaŵi yomvetsa chisoni kwambiri m’moyo wa Petro, nthaŵi imene mosakayikira anachita chisoni poikumbukira m’moyo wake wonse. Koma kodi zimene Petro anachita usikuwo zinam’pangitsa kukhala munthu wamantha? Kodi zinam’panga kukhala mmodzi wa “iwo” amene mtumwi Paulo anadzafotokoza pamene analemba kuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”? (Ahebri 10:39) Ambiri a ife tingavomereze kuti mawu a Paulo sakukhudza Petro. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mantha a Petro anali akanthaŵi kochepa, kufooka kosakhalitsa kwa munthu wolimba mtima ndi wachikhulupiriro chabasi. Mofananamo, ambiri a ife tilinso ndi nthaŵi zina m’mbuyomu zimene timachitabe chisoni tikazikumbukira, nthaŵi pamene tinadzidzimuka, n’kugwidwa ndi mantha amene anatilepheretsa kuimira choonadi molimba mtima monga momwe tinafunira. (Yerekezani ndi Aroma 7:21-23.) Ndife otsimikiza kuti kulephera kwa kanthaŵi kochepa kumeneku sikumatipanga kukhala m’gulu lobwerera kuchitayiko. Komabe, tiyenera kutsimikizira m’mtima kuti sitidzakhala m’gulu limenelo. Chifukwa chiyani? Ndipo tingapeŵe motani kukhala munthu wotero?

Zimene Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko Kumatanthauza

3. Kodi aneneriwo Eliya ndi Yona anachita mantha motani?

3 Pamene Paulo analemba za “iwo akubwerera kuloŵa chitayiko,” sanali kunena za awo amene angagwidwe ndi mantha kwa kanthaŵi kochepa. Paulo analidi kudziŵa za nkhani ya Petroyo ndi nkhani zina zofanana nazo. Eliya, mneneri wolimba mtima ndiponso woyankhula mopanda mantha, anagwidwa ndi mantha panthaŵi inayake ndipo anathaŵa kuti apulumutse moyo wake chifukwa chakuti Mfumukazi Yezebeli woipayo anamuuza kuti adzamupha. (1 Mafumu 19:1-4) Mneneri Yona anachita mantha aakulu kwambiri. Yehova anamuuza kupita kumzinda wotchuka ndi chiwawa wa Nineve. Nthaŵi yomweyo Yona anakwera chombo chopita ku Tarisi​—mtunda wa makilomita 3,500 kuchokera ku Nineveko! (Yona 1:1-3) Komabe, aneneri okhulupirika ameneŵa ngakhalenso Petro sanganenedwe kuti ndi iwo obwerera m’mbuyo. Chifukwa chiyani?

4, 5. (a) Kodi nkhaniyi ikutithandiza motani kudziŵa zimene Paulo anatanthauza ponena kuti “chitayiko” pa Ahebri 10:39? (b) Kodi Paulo anatanthauzanji ponena kuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”?

4 Onani chiganizo chonse chimene mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito: ‘Koma ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko.’ Kodi anatanthauzanji ponena kuti “chitayiko”? Mawu achigiriki amene anagwiritsa ntchito, nthaŵi zina amatanthauza kuwonongedwa kwamuyaya. Tanthauzo limeneli likugwirizana ndi nkhaniyi. Paulo anali atangochenjeza kumene kuti: “Tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziŵitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuwononga otsutsana nawo.”​—Ahebri 10:26, 27.

5 Chotero pamene Paulo anali kunena kwa okhulupirira anzake kuti, “Si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko,” ankatanthauza kuti iyeyo ndi Akristu okhulupirika oŵerenga kalata yakeyo anali otsimikizira kuti sadzachoka kwa Yehova ndipo sadzasiya kum’tumikira. Kubwerera kuloŵa kuchitayiko kungatsogolere kuchiwonongeko chosatha. Yudasi Isikariote ndi mmodzi mwa amene anabwerera kuloŵa kuchitayiko choterocho, monganso anachitira adani ena a choonadi amene mochita kufuna ankatsutsana ndi mzimu wa Yehova. (Yohane 17:12; 2 Atesalonika 2:3) Anthu oterowo ndiwo ena mwa “amantha” amene adzawonongedwa kosatha m’nyanja ya moto yophiphiritsayo. (Chivumbulutso 21:8) Ndithudi, sitikufuna kukhala m’gulu limenelo!

6. Kodi Satana Mdyerekezi amafuna kuti titenge njira yotani?

6 Satana Mdyerekezi akufuna kuti tibwerere kuloŵa kuchitayiko. Pokhala katswiri wa “machenjerero,” amadziŵa kuti njira yoipa imeneyi nthaŵi zambiri imayamba pang’onopang’ono. (Aefeso 6:11) Ngati chizunzo sichinakwaniritse zolinga zake, amayesa kuwononga chikhulupiriro cha Akristu oona mwa njira zina zosaonekera msanga. Amafuna kuona Mboni za Yehova zolimba mtima ndi zachangu zitazizira. Tiyeni tione machenjera amene anagwiritsa ntchito pa Akristu achihebri amene Paulo anawalembera kalata.

Mmene Akristu Anapanikizidwira Kuti Abwerere

7. (a) Kodi mpingo wa ku Yerusalemu unali utaona zotani? (b) Kodi ena mwa oŵerenga kalata ya Paulo anali mumkhalidwe wotani wauzimu?

7 Umboni ukusonyeza kuti Paulo analembera Ahebri kalata yake cha mu 61 C.E. Mpingo wa ku Yerusalemu unali utakumana ndi zovuta zambiri. Pambuyo pa imfa ya Yesu, panabuka chizunzo choopsa, chimene chinakakamiza Akristu ochuluka mumzindawo kubalalika. Komabe panadzakhala nthaŵi inayake ya mtendere imene inalola Akristu kuwonjezeka. (Machitidwe 8:4; 9:31) M’kupita kwa zaka, zizunzo ndi mavuto ena zinkayamba ndi kutha. Zikuoneka kuti mmene Paulo ankalemba kalata yakeyo kwa Ahebri, mpingowo unalinso pamtendere. Komabe, panali ziyeso zina. Pafupifupi zaka makumi atatu zinali zitadutsa kuchokera pamene Yesu analosera kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Zikuoneka kuti panali ena amene anali kuona kuti mapeto achedwa mopitirira muyeso motinso mwina sadzadza iwo adakali amoyo. Ena, makamaka amene anali achatsopano m’chikhulupirirocho, anali asanayesedwebe ndi chizunzo chachikulu ndipo sanali kudziŵa kufunika kwenikweni kwa chipiriro poyesedwa. (Ahebri 12:4) Ndithudi Satana anayesetsa kupezerapo mpata pamikhalidwe imeneyo. Kodi ndi “machenjero” otani amene anagwiritsa ntchito?

8. Kodi Ayuda ambiri ankauona motani mpingo watsopano wachikristu?

8 Ayuda a m’Yerusalemu ndi m’Yudeya ankanyansidwa ndi mpingo wachikristu watsopanowo. Kungoona zimene Paulo analemba m’kalata yake, titha kudziŵa china mwa chitonzo chimene atsogoleri achipembedzo achiyuda amwanowo ndi otsatira awo ankanena kwa Akristu. Kwenikweni, ayenera kuti amati: ‘Ifeyo tili ndi kachisi wamkuluyo m’Yerusalemu, amene wakhalako zaka mazana! Tili ndi mkulu wa ansembe wolemekezeka kumeneko, limodzinso ndi ansembe ake aang’ono. Tsiku ndi tsiku nsembe zimaperekedwa. Tili ndi Chilamulo, chimene chinaperekedwa kwa Mose kudzera mwa angelo ndipo chinakhazikitsidwa ndi zizindikiro zazikulu pa Phiri la Sinai. Kagulu katsopanoka ka mpatuko, Akristuwa, amene apatuka ku Chiyuda, alibe zinthu ngati zimenezi!’ Kodi chitonzo chimenechi chinakwaniritsa zilizonse? Zikuoneka kuti Akristu ena achihebri anavutika maganizo ndi chitsutsocho. Kalata ya Paulo inawapatsa chichirikizo chapanthaŵi yake.

Chifukwa Chake Sayenera Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko

9. (a) Kodi nkhani yaikulu m’kalata ya Ahebri ndi yotani? (b) Kodi Akristu anali kutumikira m’kachisi wabwino kuposa wa m’Yerusalemu m’lingaliro lotani?

9 Tiyeni tipende zifukwa ziŵiri zimene Paulo anapatsa abale ndi alongo ake a ku Yudeyako zimene sayenera kubwererera kuloŵa kuchitayiko. Chifukwa choyamba, chimenenso chili nkhani yaikulu m’kalata yonseyo yopita kwa Ahebri, ndicho ukulu wa dongosolo lachikristu la kulambira. M’kalata yake yonseyo, Paulo anafotokoza nkhani imeneyi. Kachisi wa m’Yerusalemu anali chithunzi chabe cha kachisi wamkulu koposa, kachisi wauzimu wa Yehova, nyumba ‘yosamangika ndi manja.’ (Ahebri 9:11) Akristu amenewo anali ndi mwayi wotumikira m’makonzedwe auzimu amenewo a kulambira koona. Anatumikira m’pangano labwino koposa, pangano latsopano lolonjezedwa kalelo, limene Nkhoswe yake ndi winawake wamkulu kwa Mose, Yesu Kristu.​—Yeremiya 31:31-34.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani mzere wa Yesu wobadwiramo sunam’letse kutumikira monga Mkulu wa Ansembe m’kachisi wauzimu? (b) Kodi Yesu anali motani Mkulu wa Ansembe woposa amene anali kutumikira pakachisi m’Yerusalemu?

10 Akristu amenewo analinso ndi Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri, Yesu Kristu. Inde, sanali mbadwa ya Aroni. Mmalo mwake, anali Mkulu wa Ansembe “monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke.” (Salmo 110:4) Melikizedeke, amene mzere wake wobadwiramo sunalembedwe, anali mfumu ya mzinda wakalewo wa Salemu komanso mkulu wa ansembe kumeneko. Chotero anali woyenerera kuphiphiritsa Yesu mwaulosi, amene unsembe wake sunadalire pa mzere uliwonse wobadwiramo wa anthu opanda ungwiro, koma pa chinachake chachikulu koposa​—lumbiro la Yehova Mulungu iye mwini. Monga Melikizedeke, Yesu sakungotumikira monga Mkulu wa Ansembe komanso monga Mfumu, mfumu imene sidzafa.​—Ahebri 7:11-21.

11 Komanso, mosiyana ndi mkulu wa ansembe wa pakachisi ku Yerusalemu, Yesu sanafunikire kupereka nsembe chaka ndi chaka. Nsembe yake inali moyo wake wangwirowo, umene anaupereka kamodzi, kwatha. (Ahebri 7:27) Nsembe zonsezo zoperekedwa pakachisi zinali mithunzi, zithunzi za zimene Yesu anapereka. Nsembe yake yangwiro inatheketsa kukhulukidwa kwenikweni kwa machimo a anthu onse amene anasonyeza chikhulupiriro. Mawunso a Paulo ndi osangalatsa popeza akusonyeza kuti Mkulu wa Ansembe ndiye Yesu mmodzimodziyo wosasintha amene Akristu a mu Yerusalemu anam’dziŵa. Anali wodzichepetsa, wokoma mtima, amenenso ‘amamva chifundo ndi zofooka zathu.’ (Ahebri 4:15; 13:8) Akristu odzozedwawo anali ndi chiyembekezo chotumikira monga ansembe aang’ono a Kristu! Akanaganiza bwanji zobwerera ku “miyambo yofooka ndi yaumphaŵi” ya Chiyuda chowonongekacho?​—Agalatiya 4:9.

12, 13. (a) Kodi Paulo anapereka chifukwa chachiŵiri chotani chomwe sayenera kubwererera? (b) N’chifukwa chiyani mbiri yawo yakale ya kupirira ikanalimbikitsa Akristu achihebri kusabwerera kuloŵa kuchitayiko?

12 Ngati kuti chifukwacho sichinali chokwanira, Paulo anapatsa Ahebri chifukwa chachiŵiri chimene sayenera kubwererera kuchitayiko​—mbiri yawo ya chipiriro. Iye analemba kuti: “Tadzikumbutsani masiku akale, mmenemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zoŵaŵa.” Paulo anawakumbutsa kuti iwo anali “chinthu chooneredwa” potonzedwa ndi kusautsidwa. Ena anaponyedwa m’ndende; ena anasonyeza chifundo ndi kuchirikiza a m’ndendewo. Inde, anasonyeza chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro ndi kulimbikira. (Ahebri 10:32-34) Nangano n’chifukwa chiyani Paulo anawapempha ‘kukumbukira’ zokumana nazo zoŵaŵa ngati zimenezo? Kodi zimenezo sizikanawafooketsa?

13 Iyayi, ‘kukumbukira masiku akale’ kukanakumbutsa Ahebri za mmene Yehova anawachirikizira m’mayesero awo. Ndi thandizo limeneli, iwo anali atalaka kale ziukiro zambiri za Satana. Paulo analemba kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Inde, Yehova anakumbukira ntchito zawo zonse zokhulupirikazo, kuwasunga m’chikumbumtima chake chosaiŵalacho. Zikutikumbutsa malangizo a Yesu akuti tizisungira chuma kumwamba. Palibe wakuba amene angabe chuma chimenechi; njenjete ndi dzimbiri sizingachiwononge. (Mateyu 6:19-21) Kwenikweni, chuma chimenechi chimawonongeka pokhapokha Mkristu atabwerera kuloŵa kuchitayiko. Kumenekotu kungawonongetse chuma chilichonse chimene anasungira kumwamba. N’chifukwatu champhamvu kwambiri chimene Paulo anapatsa Akristu achihebri chimene sanayenere kutenga njira imeneyo! N’kuwonongeranji zaka zonsezo za utumiki wokhulupirika? Kupitirizabe kupirira kungakhale koyenerera ndiponso kwabwino kwambiri.

Chifukwa Chake Sitiyenera Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko

14. Ndi zovuta zotani zimene tikuyang’anizana nazo lerolino zofanana ndi zimene Akristu a m’zaka zana loyamba anakumana nazo?

14 Akristu oona lerolino alinso ndi zifukwa zamphamvu zimene sayenera kubwererera. Choyamba, tiyeni tione dalitso limene tili nalo pa kulambira koyera kumene Yehova watipatsa. Mofanana ndi Akristu a m’zaka zana loyamba, tikukhala panthaŵi imene anthu a m’zipembedzo zotchuka kwambiri amatinyogodola ndi kutitonza, ponyadira matchalitchi awo a mtengo wapatali ndi miyambo yawo yomwe inayamba kalekale. Komano Yehova akutitsimikizira kuti akuvomereza mtundu wathu wa kulambira. Kwenikweni, tili ndi madalitso lerolino amene Akristu a m’zaka zana loyamba analibe. Mungadabwe kuti, ‘Zingatheke bwanji?’ Iwotu analiko pamene kachisi wauzimu anali atangoyamba kumene. Kristu anakhala Mkulu wa Ansembe m’kachisiyo atangobatizidwa mu 29 C.E. Ena mwa Akristuwo anaona Mwana wa Mulungu wochita zozizwitsayo. Ngakhale pambuyo pa imfa yake, zozizwitsa zinanso zinkachitikabe. Koma monga momwe zinanenedweratu, mphatso zimenezo zinatha m’kupita kwa nthaŵi.​—1 Akorinto 13:8.

15. Kodi Akristu oona lerolino akukhala m’nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa ulosi uti, ndipo zimenezo zimatanthauzanji kwa ife?

15 Komabe, tikukhala m’nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwapadera kwa ulosi wa kachisi wamkuluyo wa Ezekieli m’machaputala 40-48.a Chotero, taona kukonzedwanso kwa kulambira koona kwa Mulungu. Kachisi wauzimu ameneyo wayeretsedwa, zoipitsa zonse zachipembedzo ndi kupembedza mafano zachotsedwamo. (Ezekieli 43:9; Malaki 3:1-5) Talingalirani za mapindu amene kuyeretsaku kwatipatsa.

16. Kodi Akristu a m’zaka zana loyamba anakumana ndi chokhumudwitsa chotani?

16 M’zaka zana loyamba, tsogolo la mpingo wachikristu wolinganizidwawo silinali kuoneka bwino. Yesu anali ataneneratu kuti zidzakhala monga kuti m’munda momwe mwangodzalidwa kumene tirigu mwadzalidwanso namsongole, kupangitsa tirigu kukhala wovuta kum’siyanitsa ndi namsongoleyo . (Mateyu 13:24-30) Ndipo zinaterodi. Podzafika kumapeto kwa zaka zana loyamba, pamene mtumwi Yohane wokalambayo anali yekhayo woti n’kuletsa zoipitsa, mpatuko unali utayamba kale. (2 Atesalonika 2:6; 1 Yohane 2:18) Mosakhalitsa atumwi atamwalira, gulu lina la atsogoleri achipembedzo linabadwa, lopondereza nkhosa ndiponso lovala zovala zachilendo. Mpatukowo unafala ngati mpweya woipa. Zimenezo zinali zokhumudwitsa kwambiri kwa Akristu okhulupirika! Iwo anaona kulambira koyera kokhazikitsidwa chatsopanoko kukuloŵedwa m’malo ndi kulambira koipa. Zimenezi zinayamba zaka zana limodzi zisanathe kuchokera pamene Kristu anakhazikitsa mpingo.

17. Kodi mpingo wamakono wachikristu wakhala motani kwanthaŵi yaitali kuposa wa m’zaka zana loyamba?

17 Tsopano, naku kusiyana kwake. Lerolino, kulambira koyera kwakhalapo kale kwanthaŵi yaitali kuposa mmene kunakhalirapo m’nthaŵi yonseyo kufikira atumwi anamwalira. Kuchokera pamene kope loyamba la magazini ino linafalitsidwa kalelo mu 1879, Yehova watidalitsa ndi kulambira komwe kukumkabe kukhala koyera. Yehova ndi Kristu Yesu analoŵa m’kachisi wauzimu mu 1918 kuti ayeretsemo. (Malaki 3:1-5) Chiyambire 1919, kulambira Yehova Mulungu kwakhala kukuyeretsedwa mopita patsogolo. Tikumvetsetsa kwambiri maulosi a Baibulo ndi mfundo zake zachikhalidwe. (Miyambo 4:18) Kodi tiyenera kuthokoza ndani? Osati anthu wamba opanda ungwiro. Yehova yekha, pamodzi ndi Mwana wake monga Mutu wa mpingo, ndiwo amene angateteze anthu Ake kuti asaipitsidwe m’nthaŵi zoipa zino. Chotero tisalephere konse kuthokoza Yehova potilola kutengamo mbali m’kulambira koyera lerolino. Ndipo tikhale otsimikiza m’mtima zolimba kuti sitidzabwerera kuloŵa kuchitayiko!

18. Kodi tili ndi chifukwa chotani chosabwererera kuloŵa kuchitayiko?

18 Mofanana ndi Akristu achihebriwo, tili ndi chifukwa chachiŵiri chokanira kuchita mantha ndi kubwerera. Ndicho mbiri yathu yachipiriro. Kaya sitinathe zaka zambiri tikutumikira Yehova kapena takhala tikum’tumikira mokhulupirika zaka zambirimbiri, tadzipangira mbiri ya ntchito zachikristu. Ambiri a ife tazunzidwa, kaya mwa kuponyedwa m’ndende, kutsekedwa kwa ntchito yathu, nkhanza, kapena kulandidwa katundu. Ambiri takhala tikutsutsidwa ndi achibale athu, kunyozedwa, ndi kunyalanyazidwa. Tonsefe tapirira, kupitirizabe utumiki wathu wokhulupirika kwa Yehova mosasamala kanthu za mavuto ndi mayesero a m’moyo. Mwa kutero, tapanga mbiri ya kulimbikira imene Yehova sadzaiŵala, nkhokwe ya chuma chosungidwa kumwamba. Chotero, inoyi si nthaŵinso yobwerera kudongosolo loipa lakaleli limene tinasiya kumbuyo! N’kuwonongeranji ntchito yathu yaikuluyo? Zimenezi zilidi motero makamaka lerolino, pamene kwatsala “kanthaŵi kakang’onong’ono” kuti mapeto afike.​—Ahebri 10:37.

19. Kodi n’chiyani chidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira?

19 Inde, tiyeni tikhale otsimikiza m’mtima kuti “ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”! M’malo mwake, tiyeni tikhale “iwo a chikhulupiriro.” (Ahebri 10:39) Nanga tingatsimikizire motani kuti ndifedi otero, ndipo tingawathandize motani Akristu anzathu kuchita chimodzimodzi? Nkhani yotsatira idzafotokoza mfundo imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda, March 1, 1999, masamba 8-23.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi kubwerera kuloŵa kuchitayiko kumatanthauza chiyani?

◻ Kodi ndi ziyeso zotani zimene Akristu achihebri amene Paulo analembera kalata anali kukumana nazo?

◻ Ndi zifukwa zotani zosabwererera kuloŵa kuchitayiko zimene Paulo anapatsa Ahebri?

◻ Kodi tili ndi zifukwa zotani zokhalira otsimikiza mtima kuti sitidzabwerera kuloŵa kuchitayiko?

[Zithunzi patsamba 15]

Kuchita mantha kwa Petro kwa kanthaŵi kochepa sikunam’pange kukhala wa “iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena