Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Yesaya chaputala 53 ali ndi ulosi wotchuka wamesiya. Vesi 10 limati: “Kunakomera Yehova kumutundudza; anamumvetsa zoŵaŵa.” Kodi zimenezi zimatanthauzanji?
M’posavuta kuona chifukwa chimene funso likubwerera lokhudzana ndi Yesaya 53:10. Akristu oona saganiza kuti kungakomere Mulungu wathu wachifundo ndi wachikondi kutundudza kapena kudwalitsa wina aliyense. Baibulo limatipatsa maziko odalirika akuti Mulungu sasangalatsidwa ndi kuvutitsa anthu osalakwa. (Deuteronomo 32:4; Yeremiya 7:30, 31) Kwa zaka mazana ambiri Yehova nthaŵi zina wakhala akulola kuvutika pa zifukwa zogwirizana ndi nzeru ndi chikondi chake. Koma ndithudi sanachititse Mwana wake wokondedwa, Yesu, kuti avutike. Nanga kodi lembali likunenanji kwenikweni?
Chabwino, tingathandizidwe kuzindikira tanthauzo lake ngati tilingalira vesi lonseli, ndi kuona mawu aŵiri ogwiritsidwa ntchito m’lembali akuti, “kunakomera” ndi “chomukondweretsa.” Pa Yesaya 53:10 timaŵerenga kuti: “Kunakomera Yehova kumutundudza; anamumvetsa zoŵaŵa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, iye adzaona mbewu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomukondweretsa Yehova chidzakula m’manja mwake.”
Uthenga wonse wa m’Baibulo ukusonyeza kuti “chomukondweretsa Yehova” chili pa kuchita chifuno chake pogwiritsa ntchito Ufumu. Pochita zimenezi Yehova adzatsimikizitsa ufumu wake ndipo adzatheketsa kuti tchimo lotengera kwa makolo lichotsedwe kwa anthu omvera, machimo athu. (1 Mbiri 29:11; Salmo 83:18; Machitidwe 4:24; Ahebri 2:14, 15; 1 Yohane 3:8) Njira yochitira zimenezi ndi yakuti, Mwana wa Mulungu anayenera kukhala munthu ndi kupereka nsembe ya dipo. Monga tikudziŵa, pochita zimenezi Yesu anavutika. Baibulo limatiuza kuti ‘anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuŵaŵa nazo.’ Motero Yesu analandira mphoto chifukwa cha kuvutika kumeneku.—Ahebri 5:7-9.
Yesu anadziŵiratu kuti njira yabwino imene akatenga ikaphatikizapo kuvutika. Zimenezo n’zoonekeratu m’mawu ake opezeka pa Yohane 12:23, 24 pamene timaŵerenga kuti: “Yafika nthaŵi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, ngati mbewu ya tirigu siigwa m’nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.” Inde, Yesu ankadziŵa kuti adzafunika kusunga umphumphu wake ngakhale pophedwa. Nkhaniyi imapitiriza kuti: “Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine ku nthaŵi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthaŵi iyi. Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mawu ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.”—Yohane 12:27, 28; Mateyu 26:38, 39.
Ndi m’nkhani imeneyi pamene tingamvetse Yesaya 53:10. Yehova ankadziŵa bwino kuti zimene Mwana wake akakumana nazo zikaphatikizapo kutundudzidwa m’lingaliro limeneli. Komabe poganizira kulemekezeka ndi ubwino waukulu umene ukatsatira, zinakomera Yehova zimene Yesu akakumana nazo. M’lingaliro limeneli “kunakomera Yehova kumutundudza,” kapena kutundudzidwa kwa, Mesiya. Ndipo Yesu nayenso zinamukomera zimene akatha kuchita ndiponso zimene anakwanitsa kuchita. Ndithudi, Yesaya 53:10 amamaliza ndikuti, ‘chomukondweretsa Yehova chinakula m’manja mwake.’