Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w01 5/1 tsamba 3
  • Mmene Umasiye Unakhudzira Akazi Aŵiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Umasiye Unakhudzira Akazi Aŵiri
  • Nsanja ya Olonda—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Asanaphunzire ndi Ataphunzira—Anapeza Mphamvu Kuti Asinthe
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Anapatsa Agalu Anga Mabisiketi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kuthandiza Akazi Amasiye M’mayesero Awo
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Amuna ndi Akazi Amasiye Amafunikira Chiyani? Nanga Mungawathandize Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2001
w01 5/1 tsamba 3

Mmene Umasiye Unakhudzira Akazi Aŵiri

SANDRA ndi mkazi wamasiye amene akukhala m’dziko la Australia. Mwamuna wake atamwalira, Sandra anasokonezeka maganizo ndipo sanakhulupirire. “Kudziŵa kuti mwamuna wanga wokondedwa wamwalira mwadzidzidzi, kunandisokoneza maganizo kwambiri. Sindikukumbukira mmene ndinayendera kuchoka kuchipatala kufika kunyumba kapena zomwe ndinachita tsikulo. M’milungu ingapo yotsatira, mantha anga anayambitsa kupweteka m’thupi kosalekeza.”

Mnzake wa Sandra dzina lake Elaine nayenso wakhala wamasiye kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Elaine anadwazika mwamuna wake, David, kwa miyezi isanu ndi umodzi mwamunayo asanamwalire ndi matenda a kansa. Iye anali ndi chisoni kwambiri moti mpaka anasiya kuona kwakanthaŵi ndithu. Patatha zaka ziŵiri, iye anakomoka pamaso pa anthu. Dokotala wake sanam’peze ndi matenda alionse. Komabe, dokotalayo anazindikira kuti Elaine wakhala akusunga chisoni m’mtima mwake. Choncho, anamuuza kuti apite kunyumba ndipo akadzikakamize kulira. “Zinanditengera nthaŵi yaitali ndithu kuti ndithetse chisoni changa,” anavomereza motero Elaine. Ndipo anawonjezera kuti, ndikasungulumwa “ndinkakonda kupita ku chipinda chogona n’kukafunda zovala za mwamuna wanga David.”

Inde, anthu angachite zinthu zosiyanasiyana mwamuna kapena mkazi wawo wapamtima akamwalira. Kwa akazi amasiye, imfa ya mwamuna imaphatikizapo zambiri kuposa kungokhala wopanda mwamuna. Mwachitsanzo, Sandra kwakanthaŵi ndithu, ankadziona kuti si mmene analili kale. Mofanana ndi akazi ambiri amene amuna awo amwalira posachedwapa, Sandra nayenso ankadziona kuti sali wotetezedwa. Iye anakumbukira kuti: “Popeza kuti mwamuna wanga ndiye anali kusankha zochita, kumwalira kwake kwadzidzidzi kunachititsa kuti ndizisankha ndekha zochita zoterozo. Ndinali kulephera kugona. Ndinali kutopa ndiponso kufooka. Ngakhale kudziŵa kokha zofunika kuchita kunali kovuta kwabasi.”

Nkhani zofanana ndi ya Sandra ndi Elaine zikuchitika tsiku n’tsiku padziko lonse. Matenda, ngozi, nkhondo zapachiweniweni, ndiponso ziwawa zikuthandiza kuwonjezera chiŵerengero cha akazi amasiye.a Ambiri mwa akazi ameneŵa amavutika ndi chisoni m’mtima mwawo. Sadziŵa kuti kaya agwira mtengo wanji. Kodi mabwenzi ndi achibale angatani kuti athandize akazi amasiye? Nkhani yotsatirayi ili ndi malangizo amene angathandize kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

a Akazi ena ali ngati amasiye chifukwa chakuti amuna awo anawachokera. Ngakhale kuti kupatukana m’banja ndiponso kusudzulana kumabweretsa mavuto ena apadera, mfundo zina zomwe zili m’nkhani yotsatirayi zingathandizenso akazi otereŵa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena