Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w02 3/1 tsamba 30
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—2002
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Atate Wanu Ndi Wachifundo’
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Timatumikira Mulungu “Wachifundo Chochuluka”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2002
w02 3/1 tsamba 30

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’kolondola kunena kuti chifundo cha Yehova chimachepetsa chilungamo chake?

Ngakhale kuti mawu ameneŵa akhala akugwiritsidwa ntchito, ndi bwino kuwapewa chifukwa amasonyeza kuti chifundo cha Yehova chimafeŵetsa kapena kuletsa chilungamo chake, ngati kuti khalidwe lake la chifundo n’lalikulu kwambiri kuposa khalidwe lake lokhwimirapo la chilungamo. Zimenezi si zoona.

Liwu la Chihebri la “chilungamo” lingatanthauzenso “chiweruzo.” N’zoona kuti chilungamo cha Yehova chingaphatikizepo kulanga olakwa, koma chimaphatikizaponso kupulumutsa anthu amene akufunika kupulumutsidwa. (Genesis 18:20-32; Yesaya 56:1; Malaki 4:2) Motero, chilungamo cha Yehova tisamachione ngati chokhwima kapena chofunika kuchifeŵetsa.

Liwu la Chihebri la “chifundo” lingatanthauze kuchepetsa chilango. Lingatanthauzenso kusonyeza chifundo, kuwapatsa mpumulo anthu ovutika.​—Deuteronomo 10:18; Luka 10:29-37.

Yehova ali Mulungu wa chilungamo ndiponso wachifundo. (Eksodo 34:6, 7; Deuteronomo 32:4; Salmo 145:9) Chilungamo chake ndiponso chifundo chake zonse n’zangwiro ndipo zimagwira ntchito pamodzi mogwirizana. (Salmo 116:5; Hoseya 2:19) Makhalidwe onse aŵiriŵa amayendera limodzi kapena kuthandizana. Motero, ngati titanena kuti chifundo cha Yehova chimachepetsa chilungamo chake, ndiye kuti tingafunikenso kunena kuti chilungamo chake chimachepetsa chifundo chake.

Yesaya analosera kuti: “Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro [“chilungamo,” The New English Bible].” (Yesaya 30:18) Yesaya pano akusonyeza kuti chilungamo cha Yehova chimam’chititsa kusonyeza chifundo, osati kuti chifundo chake chimafeŵetsa kapena kuchepetsa chilungamo chake. Yehova amasonyeza chifundo chifukwa chakuti iye ndi wachilungamo ndiponso chifukwa chakuti ndi wachikondi.

N’zoona kuti wolemba Baibulo Yakobo analemba kuti: “Chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.” (Yakobo 2:13b) Komabe m’nkhaniyo, Yakobo sakunena za Yehova koma za Akristu amene amasonyeza chifundo​—mwachitsanzo, kuchitira chifundo ovutika kapena osauka. (Yakobo 1:27; 2:1-9) Anthu achifundo amenewo akamaŵeruzidwa, Yehova amaganizira khalidwe lawo ndipo amawakhululukira mwachifundo pamaziko a nsembe ya Mwana wake. Motero, khalidwe lawo lachifundo limapambana chilango chimene akanayenera kulandira.​—Miyambo 14:21; Mateyu 5:7; 6:12; 7:2.

Motero, n’kulakwitsa kunena kuti chiweruzo cha Yehova chimachepetsedwa ndi chifundo chake m’ganizo lakuti chilungamo chake chimafunika kufeŵetsedwa ndi chifundo. Kwa Yehova, makhalidwe aŵiri onseŵa ndi ofanana. Amafanana monga mmene makhalidwe ena a Yehova monga chikondi ndi nzeru amafananira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena