Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w04 5/15 tsamba 2-3
  • Zimene Anthu Achita Poyesa Kukondweretsa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Anthu Achita Poyesa Kukondweretsa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ziphunzitso Zoona Mungazipeze Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2000
  • N’chiyani Chimachitika pa Imfa?
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Mungathe Kukondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2004
w04 5/15 tsamba 2-3

Zimene Anthu Achita Poyesa Kukondweretsa Mulungu

“SIPANAKHALEPO gulu la anthu limene likamachita zinthu siliganizira n’komwe za Mulungu, koma nthaŵi zambiri amam’ganizira kuti Mulunguyo ndiye woyendetsa zinthu ndipo ndiye analenga zinthuzo. Izi zili choncho ngakhale pakati pa magulu a anthu amene safuna kulimbikitsa anthu kukhulupirira Mulungu.” Anatero John Bowker m’buku lake lakuti God​—A Brief History (Mbiri Yachidule ya Kukhulupirira Mulungu). Nthaŵi zonse anthu akhala akuyesayesa kuti azindikire Mulungu ndi kumukondweretsa, ndipo akhala akuchita zimenezi m’njira zosiyanasiyana. Anthu ambiri padziko lonse amafuna ndi mtima wonse kukondweretsa Mulungu. Ndipo ndi zoona kuti iwo akuchita izi mosiyanasiyana malinga ndi zikhulupiriro zawo.

Anthu ena amakhulupirira kuti chinthu chofunika kuti munthu akondweretse Mulungu ndicho kukhala ndi makhalidwe abwino basi. Enanso amaganiza kuti amakondweretsa Mulungu mwa kuchitira osauka zinthu zachifundo. Palinso anthu ambiri amene amaona miyambo ya chipembedzo kukhala yofunika kwambiri.

Ndiyeno pali anthu ena amene amakhulupirira kuti Mulungu n’ngosatheka kum’dziŵa kapena n’ngotanganidwa kwambiri ndi zinthu zina moti sangapeze nthaŵi yoganizira anthu wamba. Epicurus wa ku Greece wakale, amene anaphunzira kwambiri nzeru za anthu, akuti ankakhulupirira kuti ‘milungu sikhudzidwa ndi zimene anthu amachita ndipo singathandize kapena kuvulaza munthu m’njira iliyonse.’ Komabe, anthu ambiri amaganizo ameneŵa ndi opembedza. Ndipo ena amafika mpaka popereka nsembe ndiponso kuchita miyambo ina n’cholinga chokondweretsa makolo awo amene anafa.

Kodi inu maganizo anu ndi otani? Kodi Mulungu amaonadi zimene tikuyesetsa kuchita pofuna kuti tim’kondweretse? Kodi n’zotheka kuti tichite zinthu zom’khudza mtima Mulungu ndi kum’kondweretsa?

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Courtesy of ROE/​Anglo-Australian Observatory, photograph by David Malin

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena