Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w04 9/15 tsamba 3-4
  • ‘Pempherani Chomwechi’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Pempherani Chomwechi’
  • Nsanja ya Olonda—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndizipemphera Bwanji?—Kodi Ndizigwiritsa Ntchito Pemphero la Ambuye?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mmene Muyenera Kulimvera Pemphero la Ambuye
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kwezani Manja Okhulupirika m’Pemphero
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Yandikirani kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2004
w04 9/15 tsamba 3-4

‘Pempherani Chomwechi’

KODI mumadziŵa zimene Pemphero la Ambuye limanena? Limeneli ndi pemphero lachitsanzo limene Yesu Kristu anaphunzitsa anthu. Yesu polankhula pa Ulaliki wotchuka wa pa Phiri anati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi.” (Mateyu 6:9) Nthaŵi zambiri pempheroli limatchedwa kuti Pemphero la Ambuye pakuti analiyambitsa ndi Yesu.​—M’Chilatini pempheroli amalitcha kuti Paternoster.

Padziko lonse pali anthu ambirimbiri amene analoweza Pemphero la Ambuye ndipo amalinena pamtima mobwerezabwereza, ena mwina tsiku lililonse. Kuyambira zaka zingapo zapitazo anthu ambiri akhala akunena pempheroli m’masukulu ndi m’malo osiyanasiyana amene kwasonkhana anthu. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amaona kuti Pemphero la Ambuye n’lofunika kwambiri?

Cyprian, yemwe anali katswiri wa maphunziro apamwamba a zaumulungu m’zaka za m’ma 200 analemba kuti: “Kodi ndi pemphero linanso liti limene lili ndi mfundo zauzimu zoposa mfundo za m’pemphero limene tinachita kupatsidwa ndi Kristu . . . ? Kodi pangapezekenso pemphero lina liti lopita kwa Atate lomwe lingakhale loona kuposa lomwe tinachita kupatsidwa ndi Mwana wawo, amene ali Choonadi?”​—Yohane 14:6.

Tchalitchi cha Roma Katolika chinalemba mu katekisima wake kuti Pemphero la Ambuye ndilo “pemphero lofunika kwambiri pa Chikristu.” Buku lotchedwa The World Book Encyclopedia linatchulapo za kufunika kwa pempheroli m’zipembedzo zonse zachikristu ndipo linati pempheroli “lili m’gulu la mawu otchuka kwambiri pa Chikristu.”

Komabe, tiyenera kudziŵa kuti anthu ambiri amene amatha kunena pamtima Pemphero la Ambuye salimvetsa bwinobwino. Nyuzipepala ina ya ku Canada, yotchedwa Ottawa Citizen inati: “Ngati Chikristu mukuchidziŵako n’zotheka kuti Pemphero la Ambuye mumatha kulilakatula pamtima mosapumira, koma mwina zingakuvuteni kulinena mofatsa ndiponso mozindikira zimene mukunena.”

Kodi m’pofunikadi kumvetsa bwino mapemphero athu opita kwa Mulungu? Kodi Yesu anatipatsiranji Pemphero la Ambuye? Kodi inuyo muyenera kulimva bwanji pempheroli? Tatiyeni tione bwinobwino mafunso ameneŵa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena