Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w06 4/15 tsamba 13-16
  • Mungasankhe Bwanji Zinthu Mokondweretsa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungasankhe Bwanji Zinthu Mokondweretsa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—2006
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Njira Ndi Iyi”
  • Gwiritsani Ntchito Mfundo za M’Baibulo
  • Muziona Patali
  • Mmene Mungasankhire Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2006
w06 4/15 tsamba 13-16

Mungasankhe Bwanji Zinthu Mokondweretsa Mulungu?

MWAMUNA wina ku United States anapita ku banki ndi cheke cha ndalama zokwana madola 25,000. Iye ankafuna kuika ndalamazo mu akaunti yomwe siilola munthu kutapa ndalama nthawi yake isanakwane. Koma, wogwira ntchito m’bankimo analangiza mwamunayo kuti akaike ndalamazo pa msika wogulitsira makampani, n’kumuuza kuti ngakhale patadutsa nthawi yaitali motani, ndalama zomwe munthu waikako sizigwa mphamvu. Mwamunayo anaganiza zomvera malangizowo. Koma sipanapite nthawi yaitali, ndalama zakezo zinagwa mphamvu kwambiri.

Izi zikusonyeza kuti kusankha zochita mwanzeru n’kovuta. Nanga bwanji za zosankha zambirimbiri zomwe timafunika kupanga m’moyo? Zambiri mwa zosankha zimenezi n’zofunika kwambiri chifukwa zingathandize kuti zinthu zitiyendere bwino m’moyo kapena ayi, ndiponso m’kupita kwanthawi zingatanthauze moyo kapena imfa. Ndiyeno tingatani kuti tisakayikire kuti zimene tasankha ndi zanzeru?

“Njira Ndi Iyi”

Tsiku ndi tsiku, timasankha zoti tidye, tivale, koti tipite, ndiponso zinthu zina. Zosankha zina zingaoneke ngati zazing’ono, koma zotsatira zake zingakhale zoopsa kwambiri. Mwachitsanzo, kusankha kuti usute fodya kwanthawi yoyamba kungapangitse kuti munthu uzisuta fodya moyo wako wonse. Tisapeputse kufunika kwa zosankha zimene zikuoneka ngati zazing’ono.

Kodi ndani angatipatse malangizo posankha zochita, ngakhale pa zinthu zooneka ngati zazing’ono? Zingakhale zosangalatsa kwambiri kukhala ndi katswiri wodalirika wotipatsa malangizo pamene tikufunika kusankha zochita pankhani yovuta kwambiri! N’zotheka kuti mupeze mlangizi woteroyo. Buku lakale kwambiri lomwe lili ndi uthenga wogwira ntchito masiku ano likunena izi: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Kodi ndani akunena zimenezi? Ndipo mungatsimikize bwanji kuti malangizo ake ndi odalirika?

Lonjezo lomwe taonali likupezeka m’Baibulo, buku limene anthu ambiri aliphunzira ndipo azindikira kuti ndi louziridwa ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi. (2 Timoteo 3:16, 17) Yehova akudziwa mmene tinapangidwira, motero ndi iye amene angatipatse malangizo abwino kwambiri. Amathanso kuoneratu zam’tsogolo, popeza ‘amalalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale amanena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala.’ (Yesaya 46:10) Motero, wamasalmo anafotokoza chikhulupiriro chake m’Mawu a Yehova, kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Komano, kodi Yehova amatithandiza bwanji kukhala motetezeka m’dziko lamavuto la masiku anoli? Kodi tingasankhe bwanji zinthu mokondweretsa Mulungu?

Gwiritsani Ntchito Mfundo za M’Baibulo

Yehova Mulungu anapatsa Akristu mfundo zake n’cholinga choti azisankha zochita mwanzeru. Kuphunzira mfundo za m’Baibulo ndi kuzigwiritsa ntchito kuli ngati kuphunzira chinenero ndi kuchigwiritsa ntchito. Mukadziwa chinenerocho, mungadziwe ngati wina sanatsate malamulo ake chifukwa chakuti zomwe iye akunena sizikumveka bwino. N’kutheka kuti simungathe kutchula cholakwika chenicheni m’chiganizo chomwe munthuyo wanena, koma mumadziwa kuti penapake palakwika. Mukaphunzira mfundo za m’Baibulo mpaka kufika podziwa mmene mungazigwiritsire ntchito bwino pa moyo wanu, nthawi zonse mungathe kudziwa ngati chinthu china chomwe mwasankha kuchita n’cholakwika, chosagwirizana ndi mfundo za Mulungu.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene mnyamata angafunike kusankha pankhani yokonza tsitsi lake. M’Baibulo mulibe lamulo lililonse lomwe limatsutsa mwachindunji kakonzedwe kenakake ka tsitsi. Koma, taonani mfundo iyi ya m’Baibulo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndifunanso kuti akazi azivala moyenera, mwaulemu ndi modzichepetsa. Kudzikongoletsa kwawo kusakhale pakulukaluka tsitsi, kapena pakuvala zagolide, kapena mikanda yamtengo wapatali, kapena zovala zamtengo wapatali. Makamaka adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati n’ngopembedza Mulungu.” (1 Timoteo 2:9, 10, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Pano, Paulo anali kulemba zokhudza akazi, koma mfundo yake ikugwira ntchito kwa amuna ndi akazi. Kodi mfundo yake ndi yotani? Maonekedwe athu akhale aulemu ndi odzichepetsa. Motero, mnyamatayu angadzifunse kuti, ‘Kodi kakonzedwe ka tsitsi langa kakhala kaulemu koyenera Mkristu?’

Ndipo kodi ndi mfundo yothandiza iti yomwe mnyamata angatole m’mawu otsatirawa a wophunzira Yakobo? “Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Akristu amadana ndi kukhala mabwenzi a dzikoli, lomwe lili paudani ndi Mulungu. Ngati iye atatengera mmene achinyamata anzake amakonzera tsitsi lawo, kodi zingapangitse kuti azioneka ngati bwenzi la Mulungu kapena bwenzi la dziko? Mnyamata amene akuganizira za kakonzedwe ka tsitsi lake angagwiritse ntchito mfundo za m’Baibulo ngati zimenezi posankha mwanzeru zoti achite. Zoonadi, mfundo za Mulungu zimatithandiza posankha zochita. Ndipo tikazolowera kusankha zochita zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, kusankha mwanzeru zochita zimene sizikhala ndi zotsatirapo zoopsa sikuvuta.

M’Mawu a Mulungu tingapezemo mfundo zambiri. Inde, n’kutheka kuti sitingapeze lemba lomwe likugwirizana ndendende ndi vuto lathu. Komabe, tingawerenge zimene ena anachita pomvera malangizo a Mulungu ndi mmene ena ananyalanyazira machenjezo a Mulungu. (Genesis 4:6, 7, 13-16; Deuteronomo 30:15-20; 1 Akorinto 10:11) Mwa kuwerenga nkhani zotere ndi kusinkhasinkha zotsatirapo zake, tingaone mfundo za Mulungu zomwe zingatithandize kusankha zochita zokondweretsa Mulungu.

Taganizirani mwachitsanzo zimene Yesu anakambirana mwachidule ndi mtumwi wake, Petro. Anthu otolera ndalama za msonkho anali atafunsa Petro kuti: “Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?” Petro anali atayankha kuti: “Apereka.” Posapita nthawi, Yesu anafunsa Petro kuti: “Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana awo kodi, kapena kwa akunja?” Petro atayankha kuti: “Kwa akunja,” Yesu anamuuza kuti: “Chifukwa chake anawo ali aufulu. Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine.” (Mateyu 17:24-27) Kodi ndi mfundo zotani zomwe tingapeze m’nkhaniyi?

Mwa kum’funsa mafunso angapo, Yesu anathandiza Petro kuganiza kuti: Popeza anali Mwana wa Mulungu, Yesu sanayenere kukhoma msonkho. Ngakhale kuti Petro poyamba analephera kumvetsa mfundo imeneyi, Yesu anam’thandiza mokoma mtima kutero. Ena akalakwitsa, mwina tingasankhe kuwakomera mtima, potsanzira Yesu, m’malo mowasonyeza mwaukali zolakwa zawozo kapena kuwadzudzula.

Atatero, Petro anatha kuona chifukwa chokhomera msonkho, chomwe chinali kusafuna kukhumudwitsa ena. Nayi mfundo ina yomwe tingapeze m’nkhaniyi. Kuganizira chikumbumtima cha ena n’kofunika kwambiri m’malo moumirira pa ufulu wathu.

Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kusankha zochita zosonyeza kuti tikulemekeza chikumbumtima cha ena? Kukonda anzathu. Yesu Kristu anaphunzitsa kuti kukonda anzathu monga timadzikondera ife eni ndiko lamulo lachiwiri lofunika kwambiri ndipo loyamba ndi lokonda Mulungu ndi moyo wathu wonse. (Mateyu 22:39) Koma tikukhala m’dziko limene limalimbikitsa dyera, ndiponso mtima wathu wochimwa umatilimbikitsa kukhala wadyera. Motero, kuti munthu akonde anzake monga mmene amadzikondera mwini, ayenera kusintha maganizo ake.​—Aroma 12:2.

Anthu ambiri asintha maganizo awo, ndipo akamasankha zochita amaganizira ena, kaya ndi pankhani zazikulu kapena zazing’ono. Paulo analemba kuti: “Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nawo ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwa chikondi chitiranani ukapolo.” (Agalatiya 5:13) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Taganizirani za mtsikana wina amene anasamukira kumudzi pofuna kukathandiza anthu kuphunzira za Mawu a Mulungu. Pamene anali kulankhula ndi anthu, anazindikira kuti zovala zake, ngakhale kuti zinali zaulemu malinga ndi mavalidwe a m’tawuni, zinakhala nkhani imene inali m’kamwam’kamwa. Kuvala ndi kudzikongoletsa kwake kunali kwaulemu, koma anaganiza zoti azivala zovala zosaonekera kwambiri “kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.”​—Tito 2:5.

Kodi inu mukanatani mukanafunika kusankha zochita pankhani ya zovala kapena nkhani ina yoti munthu n’kudzisankhira yekha zochita? Musakayikire kuti Yehova angasangalale kwambiri ngati zosankha zanuzo zikusonyeza kuti mukuganizira chikumbumtima cha anthu ena.

Muziona Patali

Kupatula pa mfundo za m’Baibulo ndi chikumbumtima cha anthu ena, kodi tingaganizire za chiyani tikamasankha zochita? Ngakhale kuti moyo wachikristu ndi wovuta, mofanana ndi kuyenda m’njira ya miyala ndi yopapatiza, Mulungu amapatsa Akristuwo ufulu wochuluka m’kati mwa malire amene iye anaika. (Mateyu 7:13, 14) Tikufunika kuganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire moyo wathu wauzimu, maganizo athu, ndiponso mmene zidzakhudzire umoyo wathu m’tsogolo.

Tiyerekeze kuti mukuganizira zolowa ntchito inayake. N’kutheka kuti palibe cholakwika chilichonse kapena chosayenera pantchitoyo. Mudzatha kupita ku misonkhano ya mpingo ndiponso ikuluikulu. Malipiro ake ndi okwera kusiyana ndi mmene munali kuganizirira. Bwana wanu akuona kuti ndinu katswiri pantchitoyo ndipo akufuna kuti mupindulitse kwambiri kampani yake. Kuwonjezera apo, mumaikonda ntchitoyo. Kodi pali chilichonse chomwe chingakulepheretseni kulowa ntchitoyo? Bwanji ngati mukuona kuti m’tsogolo mudzapanikizika chifukwa cha kuikonda kwambiri ntchitoyo? Akukuuzani kuti sadzakukakamizani kugwira ovataimu. Koma kuti mumalize ntchito inayake, kodi mungakonde kuti muzidzadzipanikiza? Kodi maovataimu oterowo n’kutheka kuti angadzayambe kuchuluka? Kodi zimenezo zingadzayambe kukulepheretsani kukhala ndi banja lanu ndipo kenaka pang’ono ndi pang’ono n’kumakulepheretsani kuchita zinthu zauzimu zomwe simufunika kuphonya m’pang’ono pomwe?

Taonani mmene Jim anapangira chosankha chachikulu chokhudza ntchito yake. Anagwira ntchito mwakhama n’kupatsidwa udindo waukulu kuntchito. Kenako anakhala bwana wamkulu pa kampani yawo m’dera lonse la Kum’mawa, anakhalanso mkulu wa nthambi ya kampani yawoyo ku United States, ndiponso mmodzi wa akuluakulu a kampaniyo ku Ulaya. Koma, kutabuka mavuto a zachuma ku Japan, iye anazindikira kuti kufunafuna chuma ndi udindo n’kopanda pake. Chuma chomwe anavutikira kuchipeza chinatha mofulumira. Moyo wake unasokonezeka. ‘Kodi m’zaka khumi zikubwerazi ndizidzachita chiyani?’ anadzifunsa motero. Kenako anazindikira kuti mkazi ndi ana ake anali kuchita zinthu zatanthauzo kwambiri m’moyo. Iwo anakhala akusonkhana ndi Mboni za Yehova kwa zaka zambiri. Jim anafuna kuti nayenso akhale ndi chimwemwe komanso wokhutira monga mmene banja lake linalili. Motero anayamba kuphunzira Baibulo.

Posapita nthawi, Jim anayamba kuona kuti moyo wake unali kumulepheretsa kukhala ndi moyo watanthauzo monga Mkristu. Popeza ankakhalira kuyendayenda pakati pa Asia, United States, ndi Ulaya, iye analibe nthawi yokwanira yophunzira Baibulo ndi kusonkhana ndi okhulupirira anzake. Anafunika kupanga chosankha: ‘Kodi ndipitirize kukhala moyo womwe ndakhala nawo kwa zaka 50 zapitazi, kapena ndiyambe moyo watsopano?’ Anapemphera, kenako n’kuganizira mofatsa za mmene chosankha chakecho chidzakhudzire zinthu m’tsogolo ndipo anaganiza zoti asiye ntchito zina zonse kusiyapo imodzi yokha n’cholinga choti azikhala ndi nthawi yochita zinthu zauzimu. (1 Timoteo 6:6-8) Zomwe anasankha kuchitazo zinam’thandiza kukhala munthu wosangalala kwambiri, ndipo zinam’patsa mpata wochita nawo kwambiri ntchito zachikristu.

Zosankha zanu ndi zofunika, kaya zikhale zazikulu kapena zazing’ono. Zimene mungasankhe kuchita lero, zingathandize kuti zinthu zikuyendereni bwino m’moyo kapena ayi, ndiponso zingadzatanthauze moyo kapena imfa m’tsogolo. Mungasankhe zinthu mwanzeru ngati muganizira mfundo za m’Baibulo, chikumbumtima cha anthu ena, ndiponso mmene zosankha zanuzo zidzakukhudzireni kwa nthawi yaitali m’tsogolo. Sankhani kuchita zinthu mokondweretsa Mulungu.

[Chithunzi patsamba 13]

Zosankha zooneka ngati zazing’ono zingakhale ndi zotsatirapo zoopsa kwambiri

[Chithunzi patsamba 14]

Kodi mfundo za m’Baibulo zingamuthandize bwanji kusankha mwanzeru?

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu analankhula mokoma mtima ndi Petro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena