Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 10/1 tsamba 3-4
  • Wolamulira Wachuma Sanasankhe Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wolamulira Wachuma Sanasankhe Bwino
  • Nsanja ya Olonda—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu ndi Wolamulira Wachichepere Wachuma
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yesu ndi Woweruza Wachichepere Wachuma
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Anayankha Wolamulira Wachinyamata Amene Anali Wolemera
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti ‘Ukhale Wotsatira Wanga’?
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2007
w07 10/1 tsamba 3-4

Wolamulira Wachuma Sanasankhe Bwino

WOLAMULIRA wachuma wachinyamata anali wokonda chilungamo, womvera malamulo, ndiponso wokonda kupembedza. Iye atabwera kwa Yesu, anagwada pansi n’kufunsa kuti: “Mphunzitsi wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”

Poyankha, Yesu anauza mnyamatayo kuti afunikira kutsatira malamulo a Mulungu ngati akufuna moyo wosatha. Atafunsa kuti malamulo ake ndi ati, Yesu anati: “Usaphe munthu, Usachite chigololo, Usabe, Usapereke umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amayi wako, komanso, Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” Amenewa anali malamulo akuluakulu a m’Chilamulo cha Mose. Kenako mnyamatayo anati: “Ndakhala ndikuzitsatira zonsezi; n’chiyaninso chimene ndikupereweza?”​—Mateyo 19:16-20.

Yesu “anam’konda” mnyamatayo ndipo anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita, kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndi kupatsa ndalamazo osauka, pamenepo chuma udzakhala nacho kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”​—Maliko 10:17-21.

Yesu anamusiya mnyamatayo ndi ntchito yaikulu kwambiri yosankha chochita. Kodi iye anatani? Kodi anapereka chuma chake n’kukhala wotsatira wa Yesu, kapena anakakamirabe chuma chake? Kodi anasankha chuma cha padziko lapansi kapena chuma chakumwamba? Sizinali zophweka kuti asankhe chimodzi. N’zowonekeratu kuti mnyamatayu ankakonda zinthu zauzimu, chifukwa ankatsatira Chilamulo ndipo anafunsa mafunso ofuna kudziwa zimene angachite kuti Mulungu am’konde. Ndiyeno kodi anasankha chiyani? Iye “anachoka ali wachisoni, pakuti anali ndi katundu wochuluka.”​—Maliko 10:22.

Wolamulira wachinyamata ameneyu sanasankhe bwino. Akanakhala wotsatira wa Yesu wokhulupirika, akanapeza moyo wosatha umene iye ankafuna. Baibulo silifotokoza zimene kenako zinachitikira mnyamatayu. Koma zimene tikudziwa n’zakuti, patatha zaka pafupifupi 40, asilikali Achiroma anawononga Yerusalemu ndi madera ambiri a Yudeya. Panthawi imeneyi, Ayuda ambiri anataya chuma ndiponso moyo wawo.

Mosiyana ndi wolamulira wachinyamatayu, mtumwi Petulo ndi ophunzira ena anasankha mwanzeru. Iwo ‘anasiya zinthu zonse’ ndi kutsatira Yesu. Anasankha bwino kwambiri! Yesu anawauza kuti adzalandira zinthu zambiri kuposa zimene iwo anasiya. Koposa zonse, adzalandira moyo wosatha. Iwo sanasankhe molakwika moti n’kunong’oneza bondo.​—Mateyo 19:27-29.

Tonsefe timasankha zochita pamoyo wathu, zina zazing’ono, zina zazikulu. Kodi Yesu anatipatsa malangizo otani pankhani yosankha zochita? Kodi musankha kumvera malangizo ake? Ngati mutatero, mudzadalitsidwa kwambiri. Tiyeni tione mmene tingatsatirire Yesu ndiponso mmene tingapindulire ndi zimene iye ananena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena