Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?
YESU nthawi ina anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi alipo tate pakati panu kapena, amene mwana wake atam’pempha nsomba angam’patse njoka m’malo mwa nsomba? Kapena atam’pempha dzira iye n’kum’patsa chinkhanira?” (Luka 11:11, 12) M’nthawi ya Yesu, ana a ku Galileya ankasangalala kudya mazira ndi nsomba. N’chifukwa chake ankakonda kupempha bambo awo kuti awagulire zakudya zimenezi.
Yesu ananena kuti tiyenera kupitiriza kupempha mzimu woyera, monga mmene mwana amene ali ndi njala amapemphera chakudya. (Luka 11:9, 13) Kumvetsa kuti mzimu woyera n’chiyani, kungatithandize kudziwa kufunika kwake pamoyo wathu. Choncho, tiyeni tikambirane kaye zimene Baibulo limanena pankhani ya mzimu woyera.
“Mphamvu ya Wam’mwambamwamba”
Malemba amasonyeza bwino kuti mzimu woyera ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito pokwaniritsa zofuna zake. Mngelo Gabiriele pouza Mariya kuti adzakhala ndi mwana ngakhale kuti anali namwali, anati: “Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Malinga ndi zimene Gabiriele ananena, pali kugwirizana pakati pa mzimu woyera ndi “mphamvu ya Wam’mwambamwamba.”
Mfundo yofanana ndi imeneyi imapezekanso m’mavesi ena m’Baibulo. Mwachitsanzo, mneneri Mika ananena kuti: “Ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova.” (Mika 3:8) Yesu analonjeza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu pamene mzimu woyera udzafika pa inu.” (Machitidwe 1:8) Nayenso mtumwi Paulo ananena za “mphamvu ya mzimu woyera.”—Aroma 15:13, 19.
Choncho, kodi tinganene kuti tikuphunzirapo chiyani pa Malemba amenewa? Mzimu woyera ndi wogwirizana kwambiri ndi mphamvu ya Mulungu. Choncho mzimu woyera ndi njira imene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu yake. Mwachidule, tingati mzimu woyera ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito. Ndipotu mphamvu imeneyi ndi yosayerekezereka ngakhale pang’ono. Komanso sitingamvetsetse kuchuluka kwa mphamvu imene inafunika polenga chilengedwe chonsechi. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anasonyeza kuti tiyenera kuganiza mozama tikamaona chilengedwe. Iye anati: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.”—Yesaya 40:26.
Choncho Baibulo limasonyeza kuti chilengedwe chonsechi chinakhalapo chifukwa cha ‘mphamvu zazikulu’ za Mulungu Wamphamvuyonse. Ndithudi, mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu ndi yochuluka kwambiri, ndipo ngakhale moyo wathu umadalira mphamvu imeneyi.—Onani bokosi lakuti, “Zimene Mzimu Woyera Unachita.”
Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake woyera pochita zinthu zikuluzikulu, mofanana ndi mmene anachitira polenga zinthu zonse. Akhozanso kugwiritsa ntchito mzimuwo pothandiza anthu. M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza mmene mzimu woyera wa Mulungu unathandizira atumiki a Mulungu a padziko lapansi.
“Mzimu wa Yehova Uli pa Ine”
Zimene Yesu anachita pa utumiki wake zimatithandiza kuona pang’ono chabe mmene mzimu woyera wa Mulungu umathandizira atumiki ake. Yesu anauza anthu a ku Nazarete kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine.” (Luka 4:18) Kodi Yesu anakwanitsa kuchita chiyani mwa “mphamvu ya mzimu”? (Luka 4:14) Iye anachiritsa anthu odwala matenda osiyanasiyana, analetsa namondwe, anadyetsa anthu ambirimbiri ndi timikate komanso tinsomba tochepa, ndiponso anaukitsa akufa. Mtumwi Petulo ananena kuti Yesu anali “munthu amene Mulungu anamuonetsera poyera kwa inu . . . mwa ntchito zamphamvu, mwa zodabwitsa ndi zizindikiro, zimene Mulunguyo anachita pakati panu kudzera mwa iye.”—Machitidwe 2:22.
Masiku ano, mzimu woyera suthandiza anthu kuchita zozizwitsa ngati zimenezi. Komabe, ungatichitire zinthu zodabwitsa. Yehova amapereka mofunitsitsa mzimu wake woyera kwa anthu amene amamulambira, monga mmene Yesu anatsimikizira ophunzira ake. (Luka 11:13) N’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Kodi mzimu woyera ungakuchitireni zimenezi pamoyo wanu? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
Chifukwa chake tinganene kuti mzimu woyera si munthu
Baibulo limayerekezera mzimu woyera ndi madzi. Ponena za madalitso amene adzachitire anthu ake, Mulungu anati: “Ndidzathira madzi pa dziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbewu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako.”—Yesaya 44:3.
Mulungu akathira mzimu wake pa atumiki ake, iwo ‘amadzazidwa ndi mzimu woyera.’ Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Yesu, Yohane Mbatizi, Petulo, Paulo, Baranaba, ndiponso ophunzira amene anasonkhana pa Pentekosite mu 33 C.E., anadzazidwa ndi mzimu woyera.—Luka 1:15; 4:1; Machitidwe 4:8; 9:17; 11:22, 24; 13:9.
Ndiyeno, ganizirani izi: Ngati mzimu woyera ndi munthu, kodi zikanatheka kuti ‘athiridwe’ pa anthu osiyanasiyana? Kodi mukuganiza kuti munthu mmodzi ‘angadzaze’ mwa anthu ambirimbiri? Zimenezo n’zosatheka. Baibulo limatchula anthu amene anadzazidwa ndi nzeru, kuzindikira, kapenanso kudziwa zinthu molondola. Koma silitchula munthu aliyense kuti anadzazidwapo ndi munthu wina.—Eksodo 28:3; 1 Mafumu 7:14; Luka 2:40; Akolose 1:9.
Mawu achigiriki omasuliridwa kuti “mzimu” ndi penevuma, amenenso amatanthauza mphamvu yosaoneka. Malinga ndi buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo, mawu akuti penevuma “kwenikweni amatanthauza mphepo . . . ndiponso mpweya; komanso makamaka mzimu, umene mofanana ndi mphepo, ndi wosaoneka, sitingaugwire ndiponso ndi wamphamvu.”—Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words.
Choncho, n’zoonekeratu kuti mzimu woyera si munthu.a
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri pankhaniyi, onani mutu wakuti, “Zoona Zenizeni za Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera,” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 201 mpaka 204. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu a Chithunzi]
Photodisc/SuperStock