Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 11/1 tsamba 8
  • Bodza Lachisanu: Mariya Ndi Amayi a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bodza Lachisanu: Mariya Ndi Amayi a Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mariya Ndi Amayi a Mulungu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Lambirani Mlengi, Osati Chilengedwe
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mariya (Amayi ŵa Yesu)
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Kulambira Mulungu Mayi Kudakalipo?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2009
w09 11/1 tsamba 8

Bodza Lachisanu: Mariya Ndi Amayi a Mulungu

Kodi bodzali linayamba bwanji?

Buku lina limati: “Kulambira amayi a Mulungu kunayamba kufala kwambiri pamene . . . anthu ambiri akunja anayamba kulowa Chikhristu. . . . Anthuwa anali atayamba kale kwambiri kulambira ‘mayi wolemekezeka’ ndiponso ‘namwali woyera.’”​—The New Encyclopædia Britannica (1988), Voliyumu 16, tsamba 326 ndi 327.

Kodi Baibulo limati chiyani?

Limanena kuti: “Udzakhala ndi pathupi nudzabereka mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu nadzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. . . . Pachifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”​—Luka 1:31-35.

Lembali likusonyeza kuti Mariya anali amayi a “Mwana wa Mulungu,” osati amayi a Mulungu. Ndiponso kodi zikanatheka bwanji kuti Mariya atenge pathupi pa amene ‘m’mwamba mumachepa kumulandira’? (1 Mafumu 8:27) Komanso Mariya sananene kuti anali amayi a Mulungu. Chiphunzitso chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi n’chimene chinachititsa kuti anthu azikhulupirira kuti Mariya ndi amayi a Mulungu. Chifukwa chonena kuti Mariya ndi Theotokos (mawu achigiriki otanthauza “wobereka Mulungu”), kapena kuti “Amayi a Mulungu,” msonkhano umene unachitikira ku Efeso, mu 431 C.E., unachititsa kuti anthu azilambira Mariya. Anthu a mumzinda wa Efeso, kumene kunachitikira msonkhano wa tchalitchi umenewu, kwanthawi yaitali ankakonda kulambira fano la mulungu wamkazi wotchedwa Atemi amene iwo ankakhulupirira kuti amathandiza anthu ndiponso zinthu zina kuti zizibereka bwino.

Choncho, polambira Mariya, anthu anayambanso kuchita zinthu zina monga kuguba, zimene anthu ankachitika polambira Atemi, amene ankakhulupirira kuti ‘anagwa kuchokera kumwamba.’ (Machitidwe 19:35) Ndipo chinthu china chimene Akhristu anayambanso kuchita ndicho kugwiritsa ntchito mafano a Mariya ndiponso a anthu ena polambira.

Yerekezani ndi mavesi awa: Mateyo 13:53-56; Maliko 3:31-35; Luka 11:27, 28

ZOONA N’ZAKUTI:

Mariya anali amayi a Mwana wa Mulungu, osati amayi a Mulungu. Bodza lakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi linachititsa kuti anthu azilambira Mariya ngati Amayi a Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena