Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w10 4/1 tsamba 4
  • Uthenga wa Yesu Khristu Ndi Wamphamvu Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uthenga wa Yesu Khristu Ndi Wamphamvu Kwambiri
  • Nsanja ya Olonda—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Akuchita Mawu, Osati Akumva Okha
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mungakhale ndi Khalidwe Labwino mwa Kutsatira Zimene Yesu Anaphunzitsa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyu N’kale Lonse”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • Kodi Mapemphero Anu Amagwirizana ndi Zimene Yesu Anaphunzitsa?
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2010
w10 4/1 tsamba 4

Uthenga wa Yesu Khristu Ndi Wamphamvu Kwambiri

“Umboni wosatsutsika wosonyeza kuti munthu wina wa ku Kaperenao anali wanzeru kwambiri, ndi uthenga womwe ankalalikira chifukwa ukupitirizabe kukhudza mitima ya anthu ambiri.”a​—Anatero munthu wina wolemba mabuku dzina lake GREGG EASTERBROOK.

MAWU ali ndi mphamvu ndipo mawu anzeru komanso osankhidwa bwino angathandize anthu kukhala ndi chiyembekezo komanso angawasinthe mitima. Palibe munthu amene analalikira uthenga wa wamphamvu kwambiri kuposa wa Yesu Khristu. Munthu wina amene anamvetsera Yesu akulalikira uthenga umene masiku ano umatchedwa ulaliki wa paphiri, analemba kuti: “Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.”​—Mateyo 7:28.

Mpaka pano, uthenga umene Yesu anaphunzitsa ndi wodziwika kwa anthu ambiri padziko lonse. Taonani chitsanzo cha mfundo zina zothandiza zimene iye anaphunzitsa.

“Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Mateyo 6:24.

“Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”​—Mateyo 7:12.

“Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”​—Mateyo 22:21.

“Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Komabe uthenga wa Yesu sikuti unangokhala wosaiwalika, koma uli ndi mphamvu chifukwa umathandiza anthu kudziwa choonadi chonena za Mulungu, uli ndi mfundo zothandiza anthu kukhala ndi moyo wabwino ndipo umawathandiza kudziwa Ufumu wa Mulungu womwe udzathetse mavuto onse a anthu. Tikamakambirana za uthenga wa Yesu m’nkhani zotsatirazi, tiona chifukwa chake uthenga wake ukupitirizabe kukhudza mitima ya anthu ambiri.

[Mawu a M’munsi]

a Kaperenao unali mzinda wa ku Galileya, kwawo kwa Yesu.​—Maliko 2:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena