Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w10 11/15 tsamba 20-21
  • ‘Aliyense Apereke Chopereka kwa Yehova’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Aliyense Apereke Chopereka kwa Yehova’
  • Nsanja ya Olonda—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Kutumikira Mulungu ndi “Mtima Umodzi ndi Maganizo Amodzi”
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kupereka Mokondwera Kuchokera Pansi pa Mtima
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Mumasangalala ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • “Madalitso a Yehova Alemeretsa”
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2010
w10 11/15 tsamba 20-21

‘Aliyense Apereke Chopereka kwa Yehova’

KODI munthu wina akakuchitirani zabwino mumachita chiyani pofuna kuyamikira? Tiyeni tione zimene akuluakulu a asilikali a Isiraeli anachita poyamikira atapambana pa nkhondo yomenyana ndi Amidiyani. Nkhondoyi inamenyedwa Aisiraeli atachimwa chifukwa cholambira Baala wa ku Peori. Mulungu anathandiza anthu ake kuti apambane ndipo zinthu zimene analanda anazipereka kwa asilikali 12,000 ndiponso kwa Aisiraeli ena onse. Malinga ndi malangizo amene Yehova anawapatsa, asilikaliwo anapereka zina mwa zinthu zimene analandirazo kwa ansembe. Aisiraeli ena onse anaperekanso zina mwa zinthu zimene analandira kwa anzawo a fuko la Levi ndipo zinthu zimenezi zinali zochuluka mofanana ndi zimene asilikali anapereka kwa ansembe.​—Num. 31:1-5, 25-30.

Koma akuluakulu a asilikali ankafuna kuchitanso zinthu zina. Iwo anauza Mose kuti: “Atumiki anufe tawerenga amuna onse ankhondo amene tikuwayang’anira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene akusowapo.” Iwo anaganiza zoti apereke kwa Yehova golide ndi zinthu zina zokongoletsera. Zinthu zokongoletsera zimene anapereka zinali zolemera makilogalamu 190.​—Num. 31:49-54.

Masiku anonso anthu ambiri ali ndi mtima wofuna kuyamikira Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene wawachitira. Ndipotu si atumiki a Mulungu okha amene ali ndi mtima woyamikira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi dalaivala wa basi amene anatenga anthu popita ndiponso pobwera ku msonkhano wa mayiko ku Bologna m’dziko la Italy mu 2009. Chifukwa chakuti ankayendetsa basi mosamala ndipo anali wofatsa, anthu amene anakwera basiyo anaganiza zomulembera kalata yoyamikira komanso kumupatsa ndalama ndi buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Koma dalaivalayo anati: “Ndayamikira kwambiri kalatayi ndi buku lomwe mwandipatsa. Koma tengani ndalamazi. Ndikufuna kuti ndalama zimenezi zithandize pa ntchito yanu. Ngakhale kuti sindine wa Mboni za Yehova, ndikufuna kupereka ndalama zimenezi chifukwa ndaona kuti mumachita zinthu chifukwa cha chikondi.”

Njira imodzi imene mungasonyezere kuyamikira zimene Yehova wakuchitirani ndi mwa kupereka zopereka zothandiza pa ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova. (Mat. 24:24) Bokosi limene lili m’munsimu likusonyeza njira zimene ena amaperekera.

NJIRA ZIMENE ENA AMAPEREKERA

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amachita bajeti, kapena kuti amaika padera ndalama zoti aziponya m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Ntchito ya Padziko Lonse.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha ndalama zimene mukufuna ku Accounting Office, Watch Tower Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite ku “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso basi.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, pali njira zinanso zoperekera zinthu popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi:

Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.

Maakaunti Akubanki:

Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya:

Mungapereke masheya amene muli nawo m’kampani ku Watch Tower Society monga mphatso basi.

Malo ndi Nyumba:

Mungapereke mphatso monga malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.

Chuma Chamasiye:

Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapenanso mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Society

P. O. Box 30749

Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01 762 111

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena