Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 3/1 tsamba 12-14
  • Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Amakhulupirira Kuti Achita Mphumi
  • Kodi Mphoto Yake Imachokera Kuti?
  • “Msampha” Umene Tifunika Kuupewa
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Kutchova Juga
    Galamukani!—2015
  • Peŵani Msampha wa Kutchova Njuga
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 3/1 tsamba 12-14

Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?

MAFILIMU otchuka ndiponso mapulogalamu a pa TV amakonda kuonetsa anthu okongola, olemera, ndiponso otchuka akutchova juga. Zimenezi zimachititsa kuti anthu aziona kutchova juga ngati chinthu chosiririka. N’zoona kuti anthu amene amaonera zimenezi amadziwa kuti ndi za mufilimu basi.

Komabe, masiku ano kuli juga zosiyanasiyana monga lotale, kubetcha pa masewera osiyanasiyana ndiponso juga yosewera pa Intaneti. Anthu ambiri amakopeka ndi zimenezi. Buku lina linanena kuti kutchova juga “ndi khalidwe loipa limene anthu akuchita pafupifupi kulikonse padziko lapansi ndipo likufalikira mofulumira kwambiri.” (Internet Gambling) Mwachitsanzo, masiku ano pa TV kapena pa Intaneti amakonda kuonetsa anthu akutchova juga ya makadi. Nyuzipepala ina inanena kuti anthu ofufuza anapeza kuti ku United States, chiwerengero cha anthu otchova juga ya makadi chawonjezeka kawiri pa miyezi 18 yokha yapitayi.

Mawu akuti juga akutanthauza masewera alionse amene anthu amabetcherana ndalama ngakhale kuti sakudziwa kuti zotsatira zake zikhala zotani. Koma ena amaona kuti kutchova juga sikulakwa ngati ndalama zimene munthu akuchitira jugazo ndi zakedi komanso ngati samangokhalira kutchova juga nthawi zonse. Buku lina la Akatolika limanena kuti kutchova juga “si tchimo ngati munthu sakuiwala udindo wake pa zinthu zofunika.” (New Catholic Encyclopedia) Koma palibe vesi lililonse la m’Baibulo limene limasonyeza kuti zimenezi ndi zoona. Ndiyeno kodi Mkhristu ayenera kuiona bwanji nkhani imeneyi? Kodi Baibulo limalola kapena kuletsa juga?

M’Malemba Oyera mulibe mawu akuti juga. Komabe Malemba angatithandize kudziwa ngati juga ndi yabwino kapena yoipa. M’malo mokhazikitsa malamulo pa nkhani ina iliyonse, Baibulo limatilimbikitsa ‘kupitiriza kuzindikira chifuniro cha Yehova.’ (Aefeso 5:17) Katswiri wina wa Baibulo, dzina lake E. W. Bullinger, ananena kuti mawu a m’Chigiriki amene anawamasulira kuti “kuzindikira” pavesili amatanthauza kusonkhanitsa mfundo zonse zokhudza nkhani inayake “n’kuidziwa bwino chifukwa choiganizira mofatsa.” Choncho Mkhristu angazindikire chifuniro cha Mulungu pa nkhani ya juga mwa kusonkhanitsa mfundo zonse za m’Baibulo zokhudza nkhaniyi, n’kuziganizira mofatsa. Mukamawerenga malemba amene ali mu nkhaniyi, dzifunseni kuti: ‘Kodi kutchova juga ndi kogwirizana ndi zimene lembali likunena? Kodi Baibulo likusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti tizichita chiyani pa nkhaniyi?’

Amakhulupirira Kuti Achita Mphumi

Anthu amene amachita juga amabetcherana zinthu zimene sakudziwa kuti awine ndani. Choncho iwo amadalira mphumi kapena kuti mphamvu inayake imene amakhulupirira kuti ingawathandize kuti achite mwayi. Iwo amakhulupirira kwambiri mphamvu imeneyi makamaka akakhala kuti zimene abetcheranazo ndi ndalama. Mwachitsanzo, polemba matikiti a lotale, anthu amasankha manambala amene amati ndi manambala amwayi. Anthu okhulupirira mphamvu zamizimu amati pali mawu ena amene munthu sayenera kutchula pochita masewera enaake a ku China otchedwa mah-jongg. Komanso pochita maere, munthu amayamba kaye wauzira mpweya pamaerewo asanawaponye. Kodi n’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Otchova juga amenewa amakhulupirira kuti mphamvu inayake ingawathandize kuti achite mphumi.

Kodi kudalira mphamvu inayake imene ingachititse munthu kuchita mphumi kulibe vuto lililonse? Kale anthu ena ku Isiraeli ankakhulupirira zimenezo. Iwo ankaganiza kuti pali mphamvu inayake imene ingawapatse mwayi woti alemere. Koma kodi Yehova Mulungu anamva bwanji ndi zimenezo? Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Mulungu anawauza kuti: “Anthu inu mwamusiya Yehova. Mwaiwala phiri langa loyera. Inu mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi. Mumadzaza chikho ndi vinyo wosakaniza n’kupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.” (Yesaya 65:11) Mulungu amaona kuti kukhulupirira kuti mphamvu inayake ingatipatse mwayi n’chimodzimodzi kulambira mafano ndipo kuchita zimenezi ndi kosagwirizana ndi kulambira koona. Anthu amene amakhulupirira mphamvu zopatsa mwayi amasonyeza kuti amadalira mphamvu zinazake m’malo modalira Mulungu woona. Palibe chifukwa chilichonse chokhulupirira kuti Mulungu anasintha maganizo ake pa nkhani imeneyi.

Kodi Mphoto Yake Imachokera Kuti?

Kaya ndi juga ya pa Intaneti, lotale, kubetcherana pa masewero kapena kuchita juga kumalo otchovera juga, anthu ochita juga nthawi zambiri saganizira kwambiri za kumene mphoto imene akufuna kuwinayo ichokere. Kutchova juga kumasiyana ndi kuchita malonda ovomerezeka kapena kugula katundu, chifukwa ndalama zimene munthu wotchova juga amawina zimakhala zimene anthu ena aluza.a Bungwe lina loona za mankhwala osokoneza bongo ndi matenda a m’maganizo la ku Canada linanena kuti: “Munthu akawina ndalama zambiri za lotale, ndiye kuti anthu mamiliyoni ambiri aluza ndalama zawo.” Ndiye kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingathandize Mkhristu kuzindikira mmene Mulungu amaonera nkhaniyi?

Lamulo lomaliza pa malamulo 10 amene Mulungu anapatsa Aisiraeli limati: “Usalakelake mkazi wa mnzako, kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake, bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” (Ekisodo 20:17) Kulakalaka chuma, ndalama, kapena chinthu chilichonse cha munthu wina linali tchimo lalikulu lofanana ndi kulakalaka mkazi wake. Patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo anabwerezanso lamulo limeneli kwa Akhristu. Iye anawauza kuti: “Usasirire mwansanje.” (Aroma 7:7) Ngati Mkhristu akufuna kuwina ndalama zimene munthu wina waluza, kodi kumeneku si kusirira kwa nsanje?

“Munthu wina wolemba nkhani m’magazini, dzina lake J. Phillip Vogel ananena kuti: “Kaya anthu [ochita juga] avomereze kapena ayi, zoona ndi zakuti asanayambe kutchova juga, mumtima mwawo amalakalaka kuti ndalama imene abetchayo, ngakhale itakhala yochepa bwanji, isanduke ndalama zankhaninkhani.” Anthu amenewa amalakalaka atalemera m’kanthawi kochepa. Zimenezitu ndi zosiyana ndi zimene Baibulo limalangiza Akhristu. Limati Mkhristu ayenera ‘kugwira ntchito molimbikira. Kugwira ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.’ (Aefeso 4:28) Komanso mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.” Iye ananenanso kuti: “Adye chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.” (2 Atesalonika 3:10, 12) Komano kodi juga ndi ntchito yovomerezeka?

Ngakhale kuti nthawi zina juga ingakhale ntchito yokhetsa thukuta, ndalama zimene munthu amapeza zimakhala zoti wangowina, osati malipiro a ntchito imene wagwira. Pochita juga munthu amabetcha ndalama zake n’kumadikirira kuti awina. Mumtima mwake amangofunitsitsa atachita mwayi basi. M’mawu ena, munthu wotchova juga amafuna kukolola pomwe sanalime. Mosiyana ndi zimenezi, Akhristu oona amalangizidwa kuti azigwira ntchito kuti apeze ndalama mwachilungamo. Mfumu Solomo analemba kuti: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.” Kenako iye ananenanso kuti: “Zimenezinso n’zochokera m’dzanja la Mulungu woona.” (Mlaliki 2:24) Choncho, atumiki a Mulungu sayembekezera kuti alemere mwachinyengo, m’malomwake amadalira Mulungu kuti ndi amene angawadalitse komanso kuwathandiza kuti azikhala osangalala.

“Msampha” Umene Tifunika Kuupewa

Ngakhale munthu wotchova juga atawinadi, angachite bwino kuganizira, osati za ndalama zimene wawinazo, koma mmene kutchova juga kungakhudzire moyo wake. Lemba la Miyambo 20:21 limati: “Cholowa chopezedwa mwadyera poyamba, tsogolo lake silidzadalitsidwa.” Anthu ambiri amene anawinapo ndalama pa juga akazindikira kuti ndalama zimene apeza sizinawathandize kukhala osangalala amanong’oneza bondo. Choncho tingachite bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti tisamadalire ‘chuma chosadalirika, koma tizidalira Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.’​—1 Timoteyo 6:17.

Monga taonera, kuwina kapena kuluza ndalama pa juga kuli ndi mavuto ake. Komabe palinso vuto lina. Mawu a Mulungu amati: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru. Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.” (1 Timoteyo 6:9) Munthu wopanga msampha amaupanga moti ukakola chinthu chisathawe. Anthu amene poyamba ankafuna kutchova juga ndi ndalama zochepa kapena ankafuna kutchova juga kwa nthawi yochepa, panopa anayamba kuikonda kwambiri moti zimawakanika kusiya. Kutchova juga kumachititsa kuti munthu achotsedwe ntchito, akhumudwitse anthu amene amawakonda ndiponso kuti banja lake lisokonekere.

Ndiyeno popeza takambirana malemba ambiri onena za kutchova juga, kodi mwazindikira mmene Mulungu amaonera nkhaniyi? Mtumwi Paulo analangiza Akhristu anzake kuti: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Pa nkhani iliyonse, Mkhristu ayenera kutsatira chifuniro cha Mulungu, osati kuyendera maganizo amene anthu ambiri ali nawo masiku ano. Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe,” ndipo amafuna kuti tizisangalala. Choncho iye safuna kuti tizikumana ndi mavuto amene anthu otchova juga amakumana nawo.​—1 Timoteyo 1:11.

[Mawu a M’munsi]

a Magazini yachingerezi ya Galamukani! ya October 8, 2000, tsamba 25 mpaka 27 inafotokoza kusiyana kwa juga ndi kugula kapena kugulitsa masheya a kampani. Magaziniyi ndi yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Atumiki a Mulungu amagwira ntchito kuti apeze ndalama mwachilungamo

[Bokosi patsamba 13]

Chisangalalo Chimene Munthu Amakhala Nacho Akawina

Kodi ndi zoona kuti munthu akayamba kutchova juga, sachedwa kuyamba kuikonda kwambiri moti zimamuvuta kusiya? Atachita kafukufuku pa zimene anthu amachita akawina kapena kuluza ndalama pa juga, Dr. Hans Breiter ananena kuti: “Zimene zimachitika mu ubongo wa munthu wotchova juga akawina ndalama, ndi zofanana ndi zimene zimachitika mu ubongo wa munthu wokonda kumwa mankhwala osokoneza bongo akamwa mankhwalawo.”

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi ndalama zimene anthu otchova juga amayembekezera kuwina zimakhala za ndani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena