Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 8/1 tsamba 3
  • Kodi Ana Ayenera Kuphunzitsidwa za Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ana Ayenera Kuphunzitsidwa za Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kuphunzitsa Ana Zachipembedzo Kumawasokoneza?
  • Kodi Chinsinsi Chake Chagona Pati?
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 8/1 tsamba 3

Kodi Ana Ayenera Kuphunzitsidwa za Mulungu?

“Zimene chipembedzo chimatiphunzitsa sizitithandiza kukondana, zimangotidanitsa.”​—JONATHAN SWIFT, WOLEMBA MABUKU WA KU BRITAIN.

SWIFT ananena zimenezi m’zaka za m’ma 1700, koma anthu ambiri masiku ano angagwirizane ndi mawu akewa. Ndipotu anthu ena amakhulupirira kuti makolo sayenera kuphunzitsa ana awo zinthu zokhudza Mulungu. Iwo amaona kuti ana amene akulira m’banja lopembedza amamanidwa ufulu wochita zinthu zina.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Pa mfundo zimene zili m’munsizi, ndi iti imene mukuona kuti ndi yomveka?

● Makolo sayenera kuloledwa kuti aziphunzitsa ana awo zinthu zokhudza Mulungu.

● Makolo sayenera kuphunzitsa ana aang’ono nkhani zachipembedzo, koma ayenera kudikira mpaka anawo atakula.

● Pamene ana adakali aang’ono, makolo ayenera kuwaphunzitsa zimene iwowo amakhulupirira ponena za Mulungu. Koma anawo akamakula, makolo ayenera kuwalimbikitsa kufufuza kuti atsimikize ngati zimene anawaphunzitsazo zili zoona.

● Ana ayenera kungotengera zikhulupiriro za makolo awo popanda kufufuza ngati zili zoona kapena ayi.

Kodi Kuphunzitsa Ana Zachipembedzo Kumawasokoneza?

Palibe kholo lachikondi limene limafuna kuti mwana wake asokonezeke. Koma kodi pali umboni wosonyeza kuti ndibwino kuti makolo asamaphunzitse ana awo za Mulungu? Kwa zaka zochuluka, akatswiri akhala akufufuza zambiri zokhudza mmene zikhulupiriro zachipembedzo cha makolo zimakhudzira ana. Kodi iwo apeza zotani?

Akatswiriwa anapeza kuti chipembedzo sichisokoneza ana koma chimawathandiza kuti akule bwino. Mu 2008, nkhani imene inalembedwa m’magazini inayake inati: “Kafukufuku wasonyeza kuti kuphunzitsa mwana zachipembedzo kumathandiza kuti mwanayo azikondana kwambiri ndi mayi ake komanso bambo ake.”a (Social Science Research) Nkhani imeneyi inanenanso kuti: “Zikuoneka kuti chipembedzo komanso moyo wauzimu zathandiza ana ambiri ndipo zathandizanso kuti anthu azigwirizana m’banja.” Zimene apezazi ndi zogwirizana ndi zimene Yesu Khristu ananena. Iye anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”​—Mateyu 5:3.

Nanga bwanji mfundo yoti ana ayenera kukula kaye asanayambe kuphunzitsidwa nkhani zokhudza Mulungu ndiponso zachipembedzo? Anthu amene amakhala ndi maganizo amenewa amaiwala mfundo iyi: Mwana akangobadwa, ubongo wake umakhala ngati chitini chopanda kanthu. Ndiyeno makolo ayenera kusankha zoti zilowe m’chitini chimenechi. Angasankhe kuti aphunzitse mwana wawoyo mfundo za makhalidwe abwino ndiponso zikhulupiriro zimene akuona kuti ndi zoyenera, kapena angasankhe kuti mwanayo aphunzire zinthu zilizonse zimene amamva kwa anthu.

Kodi Chinsinsi Chake Chagona Pati?

Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti anthu amagwiritsa ntchito mfundo zachipembedzo pofuna kulimbikitsa tsankho komanso chidani. Ndiyeno kodi makolo angatani kuti zimene ananena Jonathan Swift zija zisachitikire ana awo? Kodi angaphunzitse bwanji ana awo mfundo zimene zingawathandize kuti azikonda anthu ena?

Chinsinsi chake chagona pa kudziwa mayankho a mafunso awa: (1) Kodi ana ayenera kuphunzira chiyani? (2) Ndani ayenera kuwaphunzitsa? (3) Kodi njira zabwino kwambiri zophunzitsira ana ndi ziti?

[Mawu a M’munsi]

a Mfundo za munkhani imeneyi zinachokera pa zotsatira za kafukufuku amene anachitidwa kwa ana oposa 21,000 a ku United States, komanso kwa aziphunzitsi awo ndi makolo a anawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena