Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 3/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Anatumiza Yesu Padziko Lapansi?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Yesu ndi ndani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Yesu Analidi Mwana wa Mulungu?
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 3/1 tsamba 16
[Chithunzi patsamba 16]

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa Mwana wa Mulungu?

Mulungu alibe mkazi weniweni amene anabereka naye ana. Iye ndi Mlengi wa zamoyo zonse. Anthu analengedwa mwanjira yakuti azitha kutengera makhalidwe a Mulungu. N’chifukwa chake Adamu, munthu woyamba kulengedwa, amatchedwa “mwana wa Mulungu.” Yesu amatchedwanso “Mwana wa Mulungu,” chifukwa analengedwa ndi makhalidwe ofanana ndi a Atate wake.—Werengani Luka 3:38; Yohane 1:14, 49.

Kodi Yesu analengedwa liti?

Mulungu analenga Yesu asanalenge Adamu. Ndipo Mulungu atalenga Yesu anamugwiritsira ntchito kulenga zinthu zina zonse kuphatikizapo angelo. N’chifukwa chake Baibulo limati Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Werengani Akolose 1:15, 16.

Asanabadwe ku Betelehemu, Yesu anali kumwamba monga cholengedwa chauzimu. Nthawi itakwana, Mulungu anasamutsira moyo wa Yesu m’mimba mwa Mariya n’cholinga choti Yesuyo abadwe monga munthu.—Werengani Luka 1:30-32; Yohane 6:38; 8:23.

N’chifukwa chiyani Mulungu anakonza zoti Yesu abadwe padziko lapansi? Nanga Yesu anakwaniritsa udindo wotani? Mayankho a mafunso amenewa mungawapeze m’Baibulo. Mayankhowo adzakuthandizani kumvetsa bwino komanso kuyamikira zimene Mulungu ndi Yesu anakuchitirani.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 4 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena