Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 7/15 tsamba 26
  • M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Abale Atsopano a M’bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mamembala Atsopano a Bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda—2000
  • M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Msonkhano Wapadera Komanso Wosaiwalika
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 7/15 tsamba 26

M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira

Tsiku Lachitatu m’mawa pa September 5, 2012, analengeza ku banja la Beteli ku United States ndi ku Canada kuti pali m’bale watsopano m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. M’bale Mark Sanderson anayamba kutumikira m’bungweli pa September 1, 2012.

M’bale Sanderson analeredwa ndi makolo a Mboni za Yehova mumzinda wa San Diego ku California m’dziko la United States. Iye anabatizidwa pa February 9, 1975 ndipo anayamba kuchita upainiya kudera la Saskatchewan m’dziko la Canada pa September 1, 1983. Mu December 1990, anamaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki (yomwe panopa ikuchedwa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira) ku United States. M’bale Sanderson anaikidwa kukhala mpainiya wapadera pachilumba cha Newfoundland m’dziko la Canada mu April 1991. Kenako anadzakhala woyang’anira dera wogwirizira. Ndiyeno mu February 1997, anaitanidwa kuti azikatumikira ku Beteli ya ku Canada. Mu November 2000, anaitanidwa kuti azikatumikira ku nthambi ya ku United States. Kumeneko ankagwira ntchito mu Dipatimenti Yoyang’anira Zachipatala ndipo kenako anayamba kugwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki.

Mu September 2008, M’bale Sanderson analowa Sukulu ya Abale a M’komiti ya Nthambi. Kenako anatumizidwa kukatumikira m’Komiti ya Nthambi ku Philippines. Mu September 2010, anauzidwa kuti abwerere ku United States kuti azikathandizira m’Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira.

Abale Onse Amene Ali M’Bungwe Lolamulira Panopa

Oimirira kuchokera kumanzere: D. H. Splane, A. Morris III, D.  M. Sanderson, G. W. Jackson, M. S. Lett. Okhala pansi kuchokera kumanzere: S. F. Herd, G. Lösch, G. H. Pierce. Abale onse a m’Bungwe Lolamulira ndi Akhristu odzozedwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena