Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 8/1 tsamba 3-7
  • Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi zolaula zimakhudza bwanji woonerayo?
  • Kodi zolaula zimakhudza bwanji banja la munthuyo?
  • Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya zolaula
  • Kodi Ndingapewe Bwanji Kuona Zithunzi Zolaula?
    Galamukani!—2007
  • Zithunzi Zolaula N’zowononga
    Galamukani!—2003
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuona Zithunzi Zolaula?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuonerera Zolaula?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 8/1 tsamba 3-7

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?

Masiku ano zolaula zili paliponse.a Zimapezeka m’mafilimu, m’nyimbo, m’magazini, m’masewera a pakompyuta, pa TV, m’mafoni komanso pa Intaneti. Masiku ano anthu ambiri akumaonera zolaula kuposa kale ndipo akuona kuti palibe vuto lililonse kuchita zimenezi.—Onani bokosi lakuti, “Anthu Ambiri Akumaonera Zolaula.”

Komanso zolaula zimene anthu ankaonera m’mbuyomu zikusiyana ndi zimene anthu akumaonera masiku ano. Pulofesa wina, dzina lake Gail Dines, analemba kuti: “Masiku ano anthu akumaonera zithunzi zimene poyamba anthu ankaziona kuti n’zoipa kwambiri kapena n’zosayenera.”

Kodi inuyo mumaganiza bwanji pa nkhani imeneyi? Kodi mumaona kuti kuonera zolaula kuli ndi vuto lililonse? Yesu ananena kuti: “Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.” (Mateyu 7:17) Kodi munthu amene amaonera zolaula amakumana ndi mavuto otani? Kuti tipeze yankho la funso limeneli, choyamba tiyeni tiyankhe kaye mafunso ena okhudza zolaula.

Kodi zolaula zimakhudza bwanji woonerayo?

ZIMENE AKATSWIRI ENA AMANENA: Munthu akayamba kuonera zolaula samafuna kusiya. Anthu ena amene anachita kafukufuku anapeza kuti munthu amene amaonera zolaula amakhala ndi chibaba ngati munthu wosuta fodya.

Brian,b yemwe anazolowera kuonera zolaula pa Intaneti, ananena kuti: “Ndinkalephera kusiya. Ndinkaona kuti palibe chilichonse chomwe ndingachite kuti ndisiye kuonera zolaula. Ndinkati ndikapanda kuonera zolaula, ndinkanjenjemera ndipo mutu unkandipweteka. Ndinkayesetsa kuti ndisiye koma ndinkalephera.”

Nthawi zambiri anthu amene amaonera zolaula amachita zimenezi mobisa komanso amakonda kunama. N’chifukwa chake ambiri amasowa ocheza nawo, amachita manyazi, amakhala ndi nkhawa, amavutika maganizo komanso amakhala okwiya. Nthawi zina amafunanso kudzipha. Serge, yemwe ankapanga dawunilodi zolaula pa foni yake tsiku lililonse, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkangokhala wolusa komanso sindinkaganizira anthu ena. Ndinkadziona kuti ndine munthu wopanda pake, ndinkadziimba mlandu komanso ndinkaona kuti sindingathe kusiya. Ndinkachita mantha komanso manyazi kuti ndiuze anthu ena.”

Kuonera zolaula n’koopsa kwambiri ngakhale munthu atangoonera pang’ono kapena atangoziona mwangozi. Mzimayi wina amene anatsogolera pa kafukufuku wokhudza zolaula, dzina lake Judith Reisman, ananena kuti: “Munthu akamaonera zolaula, ubongo wake umasokonezeka komanso umasunga zimene waonazo moti zimavuta kuti aziiwale.” Mtsikana wina wazaka 19, yemwe ankakonda kuonera zolaula pa Intaneti, dzina lake Susan, ananena kuti: “Sindimaiwala zithunzi zimene ndinkaonera. Nthawi zina zimangopezeka kuti zangobwera m’maganizo mwanga. Ndimaona kuti sindidzakwanitsa kuchotseratu zithunzi zimenezi m’maganizo mwanga.”

MFUNDO YOFUNIKA KUIKUMBUKIRA: Anthu amene amaonera zolaula amakhala ngati kapolo komanso amavutika kwambiri.—2 Petulo 2:19.

Kodi zolaula zimakhudza bwanji banja la munthuyo?

ZIMENE AKATSWIRI ENA AMANENA: “Banja likhoza kutha ngati mwamuna kapena mkazi amaonera zolaula.”—Linatero buku lakuti, The Porn Trap, lomwe Wendy komanso Larry Maltz analemba.

Kuonera zolaula kumasokoneza banja chifukwa

  • kumapangitsa kuti mwamuna ndi mkazi asamakhulupirirane komanso kuti asamakondane.—Miyambo 2:12-17.

  • kumapangitsa kuti woonera zolaulayo azidzikonda komanso kuti asamasangalale ndi mwamuna kapena mkazi wake.—Aefeso 5:28, 29.

  • kumalimbikitsa zilakolako zoipa zogonana.—2 Petulo 2:14.

  • woonerayo amakakamiza mwamuna kapena mkazi wake kuti azigonana potengera zimene waonerazo.—Aefeso 5:3, 4.

  • kumapangitsa kuti munthu azingoganiza zogonana komanso akhoza kuchita chigololo.—Mateyu 5:28.

Baibulo limanena kuti anthu okwatirana asamachitirane “zachinyengo.” (Malaki 2:16) Munthu akachita chigololo amakhala kuti wamuchitira mnzakeyo zachinyengo, zomwe zimasokoneza banja ndipo zingapangitse kuti okwatiranawo apatukane kapena banjalo lithe. Kupatukana komanso kutha kwa banja kumasokonezanso ana a m’banjamo.

Komanso zolaula pazokha zimasokoneza ana. Mwachitsanzo, Brian, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Tsiku lina ndikusewera chibisalirano ndinaona magazini a bambo anga a zithunzi zolaula. Pa nthawi imeneyi n’kuti ndili ndi zaka 10. Ndinayamba kumaziona mobisa koma sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani ndinkakopeka nazo. Kuyambira nthawi imeneyo ndinangozolowera kuonera zolaula.” Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata akamaonera zolaula amayamba kugonana adakali aang’ono, amagonana ndi anthu osiyanasiyana komanso amasokonezeka maganizo.

MFUNDO YOFUNIKA KUIKUMBUKIRA: Kuonera zolaula kumasokoneza banja komanso ana ndipo kumabweretsa mavuto aakulu.—Miyambo 6:27.

Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya zolaula

BAIBULO LIMATI: “Chititsani ziwalo za thupi lanu . . . kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.”—Akolose 3:5.

Kunena mwachidule, Yehovac Mulungu amadana ndi zolaula. Sikuti Mulungu amaletsa zolaula chifukwa chodana ndi zoti anthu azigonana. Tikutero chifukwa Mulungu anatilenga kuti tizikhala ndi chilakolako chogonana n’cholinga choti anthu okwatirana azisangalala, azikondana komanso kuti azibereka ana.—Yakobo 1:17.

Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu amadana kwambiri ndi zolaula? Taonani zifukwa zina:

  • Amadziwa kuti kuonera zolaula kumabweretsa mavuto aakulu.—Aefeso 4:17-19.

  • Amatikonda choncho amafuna kutiteteza kuti tisakumane ndi mavuto.—Yesaya 48:17, 18.

  • Yehova amafuna kuti mabanja komanso ana asasokonekere.—Mateyu 19:4-6.

  • Amafuna kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso kuti tizichita zinthu zolemekeza ufulu wa anthu ena.—1 Atesalonika 4:3-6.

  • Amafuna kuti tizilemekeza komanso kugwiritsa bwino ntchito mphatso yogonana.—Aheberi 13:4.

  • Yehova amadziwa kuti kuonera zolaula kumapangitsa anthu kukhala odzikonda komanso kukhala ndi maganizo olakwika omwe Satana amalimbikitsa pa nkhani ya kugonana.—Genesis 6:2; Yuda 6, 7.

MFUNDO YOFUNIKA KUIKUMBUKIRA: Munthu amene amaonera zolaula amawononga ubwenzi wake ndi Mulungu.—Aroma 1:24.

Komabe, Yehova amafunitsitsa kuthandiza anthu amene akufuna kusiya kuonera zolaula. Baibulo limati: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:8, 14) Yehova akufuna kuti anthu onse odzichepetsa omwe akufuna kusiya kuonera zolaula ‘awachitire chifundo ndi kuwasonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene akufunika thandizo.’—Aheberi 4:16; onani bokosi lakuti, “Zimene Munthu Angachite Kuti Asiye Kuonera Zolaula.”

Anthu ambiri akwanitsa kusiya kuonera zolaula chifukwa analola kuti Mulungu awathandize. Ponena za anthu ena amene anasiya makhalidwe awo oipa, Baibulo limati: “Koma mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa, mwayesedwa olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:11) Anthu amenewa amanena mawu ofanana ndi amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

Susan, yemwe anakwanitsa kusiya kuonera zolaula, ananena kuti: “Ndi Yehova yekha amene angathandize munthu kusiyiratu kuonera zolaula. Ngati mutamupempha kuti akuthandizeni, n’kumatsatira malangizo ake mukhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi iye. Musakayikire kuti Yehova akhoza kukuthandizani.”

Zimene Munthu Angachite Kuti Asiye Kuonera Zolaula

Kodi mukudziwa munthu wina aliyense amene akuyesetsa kuti asiye kuonera zolaula? Onani zimene anthu ena anachita kuti asiye kuonera zolaula.

1. Kupemphera kwa Mulungu.

“Chinthu chofunika kwambiri chimene munthu angachite kuti asiye kuonera zolaula ndi kupempha kwa Yehova kuti amuthandize.”—Anatero Franz.

Yehova amapereka mzimu woyera kwa munthu amene wamupempha thandizo ndipo mzimuwo ‘umalimbitsa zolakalaka zake kuti achite zinthu zonse zimene [Mulungu] amakonda.’ (Afilipi 2:13) Munthuyo akalola kuti mzimuwo uzimutsogolera, umamuthandiza kuti athetse “zikhumbo zake ndi zilakolako zake” zoipa.—Agalatiya 5:16, 24.

2. Kupempha nzeru kwa anthu ena.

“Munthu ukazolowera kuonera zolaula sufuna ena adziwe ndipo umachita manyazi moti sungauze anthu ena kuti akuthandize. Umaganiza kuti ukhoza kuthana nazo wekha. Koma zoona zake n’zakuti umafunika anthu ena akuthandize. Choncho, ineyo ndinadzichepetsa n’kumuuza mkazi wanga za vutolo. Ndinamuuzanso mnzanga yemwe ndinkamukhulupirira kuti andithandize. Zinali zovuta kuuza anthu ena koma zinandithandiza kwambiri.”—Anatero Yoshi.

Pamafunika kulimba mtima kuti munthu auze anthu ena za vuto limeneli. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri kuti munthu asiye kuonera zolaula komanso kuti ayambirenso kugwirizana ndi achibale komanso anzake. Susan, yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Nditauza anthu ena, mtima wanga unakhala m’malo. N’zoona kuti zinali zovuta kuuza anthu, koma nditawauza ndinapeza mtendere wamumtima ndipo ndinayambiranso kusangalala.”—Yakobo 5:16.

3. Kudziwa komanso kupewa zimene zingakuchititseni kuonera zolaula.

Munthu afunika kudziwa malo komanso zinthu zimene zingamuchititse kuyamba kuganiza zinthu zolakwika. Mwachitsanzo, kodi amayamba kuganiza zolakwika akakhala pa Intaneti? Akamaonera TV usiku? Akamawerenga magazini? Akapita kunyanja? Kapena amaganiza zolakwika akakhala ndi njala, akakwiya, akakhala yekha kapena akatopa? Sven ananena kuti: “Muyenera kudziwa zinthu zimene zingakupangitseni kufuna kuonera zolaula. Mukazidziwa muzizipewa.” Yesu ananena kuti: “Ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.”—Mateyu 5:29.

Franz ananena kuti: “Ndikaona kuti ndayamba kuyang’anitsitsa mzimayi momusirira ndimapemphera kwa Yehova. Ndikatero ndimayesetsa kuyang’ana kumbali.” Yobu, yemwe anali wokhulupirika ananena kuti: “Ndachita pangano ndi maso anga. Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?’’—Yobu 31:1.

4. Kukonda Mulungu

Franz ananenanso kuti: “Muzikonda kuganizira zinthu zabwino komanso muzitanganidwa ndi kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu.”

Baibulo limati: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi . . .  ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.”—Afilipi 4:8, 9.

a Mawu akuti “zolaula” amatanthauza zinthu zokhudza kugonana zimene zimapangidwa n’cholinga choti munthu amene akuonera, kumvetsera kapena kuwerengayo akhale ndi maganizo ofuna kugonana. Zolaula zimatha kupezekanso m’mabuku, m’magazini, m’nyimbo komanso m’zithunzi.

b Mayina asinthidwa.

c Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.

ANTHU AMBIRI AKUONERA ZOLAULA

PA SEKONDI ILIYONSE: Anthu pafupifupi 30,000 amaonera zolaula pa Intaneti.

PA MPHINDI ILIYONSE: Anthu amatumiza ma imelo okhala ndi zolaula oposa 1.7 MILIYONI.

PA OLA LILILONSE: Ku United States kumatulutsidwa mavidiyo AWIRI oonetsa zolaula zoipa komanso zankhanza kwambiri.

TSIKU LILILONSE: Ku United States kokha anthu amabwereka mafilimu oonetsa zolaula pafupifupi 2 MILIYONI.

MWEZI ULIWONSE: Ku United States, anyamata 9 pa 10 alionse komanso atsikana atatu pa 10 alionse amaonera zolaula.

CHAKA CHILICHONSE: Padziko lonse makampani opanga mafilimu kapena zinthu zolaula amapeza ndalama pafupifupi madola 100 BILIYONI.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena