Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 tsamba 3
  • Zimene Zimalepheretsa Ena Kukonda Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zimalepheretsa Ena Kukonda Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Choonadi Chingakumasuleni
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Bodza Lachiwiri: Mulungu ndi Wosamvetsetseka
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Bodza Lachitatu: Mulungu ndi Wankhanza
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kondani Mulungu Amene Amakukondani
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 11/1 tsamba 3
[Chithunzi patsamba 3]

NKHANI YA PACHIKUTO | MABODZA OMWE AMALEPHERETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU

Zimene Zimalepheretsa Ena Kukonda Mulungu

“‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba.”—Ananena mawu amenewa ndi Yesu Khristu, mu 33 C.E.a

Anthu ena zimawavuta kukonda Mulungu chifukwa amaona kuti ndi wosamvetsetseka, wankhanza komanso sakhudzidwa ndi mavuto a anthu. Taonani zimene ena ananena:

  • “Ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize. Koma pa nthawi yomweyonso ndinkaona kuti iye sakhudzidwa ndi mavuto a anthu ndipo sangamve mapemphero anga. Ndinkaona kuti Mulungu si weniweni.”—Marco, Italy.

  • “Ndinkafuna kutumikira Mulungu, koma ndinkaona kuti saganizira n’komwe za ine. Ndinkaonanso kuti iye ndi Mulungu wankhanza amene amangofuna kutilanga basi. Ndinkaganiza kuti alibe chikondi.”—Rosa, Guatemala.

  • “Ndili mwana, ndinkakhulupirira kuti Mulungu amangofufuza zolakwa zathu n’cholinga choti atilange. Kenako ndinayamba kumuona kuti ndi wapamwamba kwambiri moti sindingakhale naye pa ubwenzi. Ndinkaona kuti Mulungu ali ngati pulezidenti amene amalowerera nkhani za anthu amene amawalamulira, koma alibe nawo chidwi chenicheni.”—Raymonde, Canada.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi Mulungu ndi wopanda chikondi? Akhristu akhala akudzifunsa funso limeneli kwa zaka zambirimbiri. Ndipotu m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500 anthu ambiri a m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu sankapemphera kwa Mulungu Wamphamvuyonse chifukwa ankachita naye mantha kwambiri. Wolemba mbiri wina, dzina lake Will Durant, analemba kuti: “Zingatheke bwanji kuti munthu wochimwa alimbe mtima kupemphera kwa Mulungu, yemwe ndi woopsa komanso ali kutali kwambiri ndi anthu?”

Koma kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthu aziona kuti Mulungu ndi ‘woopsa komanso ali nawo kutali kwambiri?’ Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani zokhudza Mulungu? Nanga kodi kuphunzira zoona zokhudza Mulungu kungakuthandizeni kuti muzimukonda kwambiri?

a Mateyu 22:37, 38.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena