Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 7/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Yesu Atiphunzitsa Ife Kupemphera
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 7/1 tsamba 16
Bambo wachikulire akupemphera

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera?

Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye momasuka komanso nthawi zonse, n’kumuuza mavuto athu. (Luka 18:1-7) Tikamapemphera amamvetsera chifukwa amatidera nkhawa. Ndiye popeza Atate wathu wakumwamba amatilimbikitsa kuti tizimuuza mavuto athu, tiyeneradi kumapemphera kwa iye.—Werengani Afilipi 4:6.

Sikuti tiyenera kupemphera pa nthawi yokha imene tikufuna kuti Mulungu atithandize zinazake. Tizidziwanso kuti pemphero limatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Salimo 8:3, 4) Tikamauza Yehova zakukhosi kwathu nthawi zonse, timayamba kumuona kuti ndi mnzathu wapamtima.—Werengani Yakobo 4:8.

Kodi tizipemphera bwanji?

Mulungu safuna kuti tikamapemphera tizinena mawu odzionetsera kapena kunena mapemphero oloweza. Safunanso kuti tizichita kukhala mwa njira inayake tikamapemphera. Chofunika kwambiri kwa iye n’choti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima. (Mateyu 6:7) Mwachitsanzo, Hana yemwe ankakhala ku Isiraeli wakale, pa nthawi ina anapemphera zokhudza mavuto a m’banja lake. Yehova atayankha pemphero lake, iye anasangalala kwambiri ndipo anapempheranso kwa Mulungu n’kumuthokoza kuchokera pansi pa mtima.—Werengani 1 Samueli 1:10, 12, 13, 26, 27; 2:1.

Tilitu ndi mwayi waukulu woti tingathe kupemphera kwa Mlengi wathu n’kumuuza zimene zikutidetsa nkhawa. Tingathenso kumutamanda ndi kumuthokoza pa zabwino zimene amachita. Choncho tiyenera kupemphera nthawi zonse posonyeza kuti timayamikira mwayi umenewu.—Werengani Salimo 145:14-16.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku ili lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena