Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 9/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Angelo Ndi Otani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Zochita za Angelo Ndiponso Ziwanda Zimakhudza Bwanji Anthufe?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mmene Angelo Amatikhudzira
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 9/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi angelo amathandiza anthu masiku ano?

Danieli ali m’dzenje la mikango ndipo mngelo akumuteteza kuti mikangoyo isamudye

Angelo anathandiza Danieli yemwe anali mtumiki wa Yehova wokhulupirika. Masiku anonso angelo amathandiza anthu kuti amve uthenga wabwino

Yehova analenga angelo mamiliyoni ambirimbiri asanalenge anthu. (Yobu 38:4, 7) Angelo ndi amphamvu kwambiri ndipo amatumikira Mulungu. Nthawi zina Mulungu amawagwiritsa ntchito potsogolera komanso poteteza atumiki ake padziko lapansi. (Salimo 91:10, 11) Masiku ano, angelo amathandiza anthu kudziwa za uthenga wabwino umene otsatira a Yesu amalalikira.—Werengani Chivumbulutso 14:6, 7.

Kodi tiyenera kupemphera kwa angelo kuti atithandize? Ayi, chifukwa tikamapemphera timakhala kuti tikulambira ndipo Yehova yekha ndi amene tiyenera kumulambira. (Chivumbulutso 19:10) Popeza angelo ndi atumiki a Mulungu, iwo amachita zinthu zimene Mulungu wawauza osati zimene anthu awapempha. Choncho, nthawi zonse tiyenera kupemphera kwa Mulungu kudzera mwa Yesu.—Werengani Salimo 103:20, 21; Mateyu 26:53.

Kodi pali angelo ena oipa?

Mofanana ndi anthu, angelo analengedwa ndi ufulu wosankha zochita, ndipo akhoza kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti angelo ena anasankha kusamvera Mulungu. (2 Petulo 2:4) Mngelo woyamba kusamvera anali Satana, ndipo kenako angelo enanso anamutsatira ndipo anakhala ziwanda. Patapita nthawi, Satana ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwamba n’kuponyedwa padziko lapansi.—Werengani Chivumbulutso 12:7-9.

Zinthu zoipa komanso zachiwawa zakhala zikuwonjezeka padzikoli kuyambira 1914. Zimenezi ndi umboni woti Mulungu awononga Satana ndi ziwanda zake posachedwapa.Kenako Mulungu adzakonzanso dzikoli n’kukhala paradaiso.—Werengani Chivumbulutso 12:12; 21:3, 4.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 10 wa m’buku ili lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena