Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 11/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Achibale Anu Ndi Anzanu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Chiukiriro—Cha Yani, ndipo Kuti?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 11/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi n’zoona kuti Yesu anaukitsa anthu?

Yesu akuitana Lazaro, yemwe anali atamwalira, kuti atuluke m’manda

Yesu anaukitsa Lazaro, yemwe anali atakhala m’manda masiku 4

M’Baibulo muli nkhani zonena kuti Yesu anaukitsa anthu. Nkhani zimenezi si nthano chabe chifukwa zinachitika pamalo komanso nthawi yodziwika bwino. Mwachitsanzo, m’chaka cha 31 C.E., Yesu ndi anthu ena ankachokera ku Kaperenao kupita ku Naini. Atafika ku Naini, anakumana ndi gulu la anthu litanyamula maliro ndipo Yesu anaukitsa womwalirayo. Nkhani imeneyi si yokayikitsa, chifukwa inalembedwa m’Baibulo komanso anthu ambiri anaona zimenezi zikuchitika.—Werengani Luka 7:11-15.

Yesu anaukitsanso Lazaro, yemwe anali mnzake. Lazaroyo anali atakhala m’manda masiku 4. Nkhani imeneyinso si yokayikitsa chifukwa pamene zimenezi zinkachitika, panali anthu ambiri amene anaona.—Werengani Yohane 11:39-45.

N’chifukwa chiyani Yesu ankaukitsa anthu?

Yesu ankaukitsa anthu chifukwa anali wachifundo. Ankachitanso zimenezi pofuna kusonyeza kuti Atate wake, yemwe ndi Mlengi, anamupatsa mphamvu zoukitsira akufa.—Werengani Yohane 5:21, 28, 29.

Tikamawerenga nkhani zokhudza anthu amene Yesu anawaukitsa, zimatithandiza kukhulupirira kuti zimene iye analonjeza zidzachitikadi. Iye adzaukitsa anthu ambirimbiri, kuphatikizapo amene anamwalira asakudziwa Mulungu. Anthuwa adzapatsidwa mwayi wophunzira za Yehova yemwe ndi Mulungu wachikondi.—Werengani Machitidwe 24:15.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 7 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena