Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 3/1 tsamba 13-15
  • Mphatso Zoyenera Kupatsa Mfumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphatso Zoyenera Kupatsa Mfumu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ANKADUTSA NAZO M’CHIPULULU CHA ARABIA
  • “ANKASUNGA CHINSINSI”
  • Zodzoladzola Zimene Anthu Akale Ankagwiritsa Ntchito Podzikongoletsa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mafuta a Basamu wa ku Gileadi Ndi Ochiritsa
    Nsanja ya Olonda—2010
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 3/1 tsamba 13-15
Zinthu zonunkhira zosiyanasiyana

Mphatso Zoyenera Kupatsa Mfumu

“Okhulupirira nyenyezi ochokera kumadera a kum’mawa . . . anamasula chuma chawo ndi kupereka kwa mwanayo mphatso za golide, lubani ndi mule.”—Mateyu 2:1, 11.

MUTAKHALA kuti mukufuna kupereka mphatso kwa munthu yemwe mumamuona kuti ndi wofunika kwambiri, mungapereke mphatso yanji? Kale zinthu zonunkhira zinali zamtengo wapatali ngati golide ndipo ankaziona kuti ndi mphatso zoyenera kupereka kwa mfumu.a N’chifukwa chake mphatso zina zimene okhulupirira nyenyezi anapereka kwa “mfumu ya Ayuda,” zinali lubani ndi mule, zomwe ndi zinthu zonunkhira.—Mateyu 2:1, 2, 11.

Balsam oil

Mafuta a Basamu

Baibulo limanenanso kuti mfumukazi ya ku Sheba itapita kwa Mfumu Solomo, “inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente 120, mafuta a basamu ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali. Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo.”b (2 Mbiri 9:9) Mafumu enanso ankapereka kwa Solomo mafuta a basamu pomufunira zabwino.—2 Mbiri 9:23, 24.

N’chifukwa chiyani kale zinthu zonunkhira zimenezi zinali zamtengo wapatali komanso zodula? Chifukwa choti ankazigwiritsa ntchito akamachita miyambo yachipembedzo, poika maliro komanso ngati zodzoladzola. (Onani bokosi lakuti, “Kodi Kale Anthu Ankagwiritsa Ntchito Bwanji Zinthu Zonunkhira?”) Zinthuzi zinkadulanso chifukwa choti anthu ambiri ankazifuna, zinkachokera kutali komanso chifukwa choti pankalowa ndalama zambiri kuti munthu afike nazo pamsika.

ANKADUTSA NAZO M’CHIPULULU CHA ARABIA

Kasiya

Kasiya

Kale ku Isiraeli, mitengo ya zonunkhira inkapezeka m’chigwa cha Yorodano. Koma zonunkhira zina zinkachokera m’mayiko ena. Baibulo limatchula mayina a zonunkhira zosiyanasiyana. Zina mwa zinthu zimenezi ndi safironi, aloye, basamu, sinamoni, lubani ndi mule. Panalinso zonunkhira zina monga chitowe, minti ndi dilili zomwe ankazigwiritsa ntchito ngati zokometsera m’zakudya.

Kodi zonunkhira zomwe zinkachokera ku mayiko ena, zinkachokera mayiko ati? Aloye, kasiya ndi sinamoni ankachokera kudera lomwe masiku ano ndi China, India ndi Sri Lanka. Mule ndi lubani ankachokera m’dera lachipululu lomwe linkayambira kum’mwera kwa Arabia mpaka kukafika ku Somalia, komwe ndi ku Africa. Ndipo nado wambiri ankachokera ku India, kumapiri a Himalaya.

Safuroni

Safuroni

Kuti zonunkhirazi zikafike ku Isiraeli, nthawi zambiri zinkadutsa ku Arabia. Buku lina linati chifukwa cha izi, kuchokera mu 2000 B.C.E. mpaka mu 1000 B.C.E., ku Arabia “ndi komwe amalonda ambiri ankadutsa pochoka kum’mawa kupita kumadzulo.” (The Book of Spices) M’dera lina lotchedwa Negev lomwe lili kum’mwera kwa Israel anapezako matauni akale, mipanda komanso malo amene ankaimikamo makalavani, zomwe zikusonyeza kuti amalonda ogulitsa zinthu zonunkhira ankadutsa m’derali. Nthambi ina ya UNESCO yoona za zinthu zakale inati zinthu zomwe anapezazi, “zikusonyeza kuti anthu ankachita bizinezi yotentha, ya zonunkhira  . . . kuchokera ku Arabia kukafika kumadera ozungulira nyanja ya Mediterranean.”

“Ngakhale kakhungwa kakang’ono ka sinamoni kankadula kwambiri, chifukwa aliyense ankafuna kugula zinthu zonunkhira.”—The Book of Spices

Makalavani onyamula zinthu zonunkhira ankayenda ulendo wa makilomita 1,800 kudutsa ku Arabia. (Yobu 6:19) M’Baibulo muli nkhani ya Aisimaeli, amalonda omwe ananyamula zinthu zonunkhira monga mafuta a ‘labidanamu, a basamu komanso makungwa a utomoni wonunkhira.’ (Genesis 37:25) Amalondawa ankachokera ku Giliyadi kupita ku Iguputo. Ana aamuna a Yakobo anagulitsa Yosefe, yemwe anali mng’ono wawo, kwa amalondawa.

“ANKASUNGA CHINSINSI”

Dilili

Dilili

Kwa zaka zambiri, amalonda a ku Arabia ndi amene ankachita malonda ogulitsa zinthu zonunkhira. Amalondawa ndi amene ankagulitsa kasiya ndi sinamoni wambiri amene ankapezeka ku Asia. Pofuna kuti anthu a m’madera ozungulira nyanja ya Mediterranenean asamapite okha kum’mawa kukagula zinthu zonunkhira, anthu a ku Arabia anayamba kufalitsa bodza loti pankakhala matatalazi kuti munthu agule zinthu zonunkhirazo. Buku lija linanenanso kuti: “Amalonda a ku Arabia ankasunga chinsinsi kuti anthu asadziwe zoti zimene ankanenazi linali bodza lankunkhuniza.”

Chitowe

Chitowe

Kodi bodza lake linali lotani? Wolemba mbiri yakale wina wa zaka za m’ma 400 B.C.E., dzina lake Herodotus, ananena kuti amalonda a ku Arabia ankati kumene amapeza zonunkhira kunali mbalame zoopsa. Ankati mbalamezi zinkamanga zisa zamakungwa a mtengo wa sinamoni pamwamba pa phiri, poti munthu sangathe kufikapo. Ndiye kuti munthu apeze zonunkhirazi ankaika nyama yambiri pansi pa phirilo. Ndiyeno mbalame inkabwera kudzatenga nyamayo n’kukaiika m’chisa chake ndipo chisacho chinkagwa pansi chifukwa cholemedwa. Zikatere munthu ankathamanga n’kukatola chisacho, chomwe chinkakhala cha makungwa a sinamoni n’kugulitsa kwa amalonda aja. Buku lija linati nkhani zabodzazi zinafala kwambiri ndipo zinapangitsa kuti anthu aziganiza kuti sinamoni ndi wovuta kwambiri kum’peza. Izi zinapangitsa kuti sinamoni azigulitsidwa modula kwambiri.

Minti

Minti

Koma paja amati palibe chinsinsi. Choncho patapita nthawi, anthu anatulukira kuti amalonda a ku Arabia ankanama. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu enanso ayambe kuchita malondawa. Moti pofika zaka za pakati pa 1 ndi 99 B.C.E., mzinda wa Alexandria ku Iguputo unali chimake cha malonda a zinthu zonunkhira. Anthu oyendetsa sitima atajaira kudutsa panyanja ya India potengera mmene mphepo ikuyendera, sitima za Aroma zinayamba kumadutsa panyanjayi kuchoka ku Iguputo kupita ku India. Izi zinachititsa kuti zinthu zonunkhira zizipezeka paliponse ndipo zinayamba kutchipa.

Masiku ano anthu saona kuti zinthu zonunkhira ndi zamtengo wapatali ngati golide. Ndipo ndi ochepa amene angaganize kuti zinthuzi ndiye mphatso zoyenera kupatsa mfumu. Komabe anthu ambiri padziko lonse, amagwiritsabe ntchito zinthu zonunkhirazi ngati mankhwala, perefyumu komanso ngati zokometsera m’zakudya. Fungo lake labwino limapangitsa kuti anthu ambiri azizikonda ngati mmene zinalilinso zaka zambirimbiri kalelo.

Makungwa a Sinamoni

Sinamoni

a M’Baibulo mawu amene anawamasulira kuti “zinthu zonunkhira,” nthawi zambiri satanthauza zokometsera m’zakudya. Koma amatanthauza zinthu zonunkhira zochokera zomera.

b “Mafuta a basamu” anali mafuta onunkhira kapena utomoni wochokera ku mitengo komanso zitsamba.

Kale Zinthu Zonunkhira Zinkagwira Ntchito Zosiyanasiyana

Mafuta odzozera komanso zofukizira. Yehova anauza Mose mmene angapangire mafuta odzozera komanso zofukizira. Anafunika kupanga zinthuzi pogwiritsa ntchito zonunkhira 4 zosiyanasiyana. (Ekisodo 30:22-25, 34-38) Ansembe ena anali akatswiri popanga mafuta odzozerawa komanso ankaonetsetsa kuti mafutawa alipo okwanira nthawi zonse.—Numeri 4:16; 1 Mbiri 9:30.

Perefyumu komanso mankhwala. Anthu olemera ankagwiritsa ntchito zonunkhirazi kununkhiritsa m’nyumba zawo, zovala zawo, pabedi komanso ngati mafuta odzola. (Esitere 2:12; Miyambo 7:17; Nyimbo ya Solomo 3:6, 7; 4:13, 14) Mariya, mchemwali wake wa Lazaro, anathira tsitsi ndi miyendo ya Yesu “mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado weniweni,” ndipo anali odula kwambiri. Botolo laling’ono la “nado,” mtengo wake unali wofanana ndi malipiro a chaka chonse.—Maliko 14:3-5; Yohane 12:3-5.

Poika maliro. Nikodemo anabweretsa “mule wosakaniza ndi aloye,” kuti anthu apake thupi la Yesu pokonzekera kukaliika m’manda. (Yohane 19:39, 40) Komanso ophunzira ena a Yesu anatenga “zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira” n’kupita nazo kumanda a Yesu.—Luka 23:56–24:1.

Zokometsera m’zakudya. Aisiraeli ankaika zinthu zonunkhira mu nsomba komanso mu nyama monga zokometsera. Zokometsera zina ankazithira m’mowa kuti ukhale nthawi yaitali.—Nyimbo ya Solomo 8:2.

M’mene Ankapangira Lubani Ndi Mule

Lubani ankapangidwa kuchokera ku utomoni wa makungwa a mitengo ing’onoing’ono ndipo mule ankachokera ku zitsamba zaminga.

Mitengo ya lubani inkapezeka kum’mwera kwa Arabia m’mphepete mwa nyanja. Pomwe zitsamba za mule zinkapezeka kwambiri m’dera lachipululu lomwe pano ndi Somalia ndi Yemen. Lubani ndi mule zinali zinthu zamtengo wapatali chifukwa cha kununkhira kwake. Yehova anasankha kuti zinthu zimenezi zizigwiritsidwa ntchito polambira. Mule ankaikidwa m’mafuta odzozera ndipo lubani ankasakanizidwa ndi zinthu zina n’kupanga zofukizira. (Ekisodo 30:23-25, 34-37) Komabe lubani ndi mule ankazigwiridwa ntchito mosiyana.

Lubani ankafunika kumuwotcha kuti atulutse fungo labwino. Koma utomoni womwe ankauchotsa mu zitsamba za mule, ankaugwiritsa ntchito popanda kuuwotcha. Mule amatchulidwa katatu m’nkhani zonena za Yesu. Koyamba, okhulupirira nyenyezi anapatsa Yesu mule ngati mphatso ali mwana. (Mateyu 2:11) Kachiwiri, anthu anasakaniza mule ndi vinyo n’kupanga mankhwala ochepetsa ululu ndipo anamupatsa Yesu atapachikidwa, koma Yesu anakana. (Maliko 15:23) Kachitatu, mule anagwiritsidwa ntchito ngati zonunkhira pokonza thupi la Yesu kuti akaliike m’manda.—Yohane 19:39.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena