Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 6/1 tsamba 6-7
  • Sayansi Singatithandize Kudziwa Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sayansi Singatithandize Kudziwa Zonse
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Chilengedwe Chonsechi Ndiponso Zamoyozi Zinakhalako Bwanji?
    Galamukani!—2002
  • Kugwirizanitsa Sayansi ndi Chipembedzo
    Galamukani!—2002
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaona Bwanji Sayansi?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 6/1 tsamba 6-7
Wasayansi ali mu labotale

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SAYANSI INGALOWE M’MALO MWA BAIBULO?

Sayansi Singatithandize Kudziwa Zonse

Zaka zapitazi, anthu alemba mabuku ambiri ofotokoza zimene anthu omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu ananena. Anthu ambiri amachita chidwi ndi zimene mabukuwa amanena moti amayamba kukhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani yoti kuli Mulungu kapena ayi. Wasayansi wina dzina lake David Eagleman analemba kuti: “Anthu ena akawerenga mabukuwa . . . amaganiza kuti asayansi amadziwa zonse moti amakhulupirira kuti zimene asayansiwa anganene pa nkhani yoti kulibe Mulungu, zikhoza kukhala zoona. Koma asayansi enieni amadziwa kuti pali zinthu zambiri zomwe sanazidziwebe ndipo zimenezi zimaonekera bwino akatulukira chinthu chatsopano.”

Katswiri wa zakuthambo akugwiritsa ntchito chipangizo choonera kutali

Kuyambira kale kwambiri, akatswiri a sayansi akhala akufufuza kuti adziwe zambiri zokhudza chilengedwechi ndipo adabwa kwambiri ndi zimene apeza. Komabe nthawi zina zimene apeza sizikhala zolondola. Mwachitsanzo wasayansi wina, dzina lake Isaac Newton yemwe anatulukira zinthu zambiri, ankaphunzitsa kuti mphamvu yokoka imachititsa kuti mapulaneti, nyenyezi komanso magulu a nyenyezi zizikhala mwadongosolo m’mlengalenga. Anayambitsanso njira ina yosovera masamu yomwe masiku ano amagwiritsa ntchito popanga makompyuta. Asayansi amagwiritsanso ntchito masamuwa kuti adziwe mmene angayendere kupita kumapulaneti ena komanso popanga zinthu monga mabomba, magetsi ndi zina zomwe zimapangidwa pogwiritsa ntchito mphamvu ya nyukiliya. Komabe, zinthu zina zomwe Newton ankakhulupirira zinali zabodza. Mwachitsanzo ankakhulupirira kuti akhoza kugwiritsa ntchito njira zamatsenga kuti asinthe zitsulo kukhala golide.

Zaka 1,500 Newton asanapeze zimenezi, munthu wina wa ku Greece, yemwenso anali katswiri wolemba mapu, dzina lake Ptolemy, ankafufuza zinthu za m’mlengalenga ndi maso ake. Ankachita zimenezi usiku kuti aone mapulaneti omwe ali m’mlengalenga. Ptolemy ankakhulupirira kuti dzikoli ndiye pakati pa chilengedwe chonse. Komabe wasayansi wina dzina lake Carl Sagan analemba kuti: “Anthu anakhala akukhulupirira zimene Ptolemy ankanenazi kwa zaka zoposa 1,500 koma sankadziwa kuti n’zabodza. Zimenezi zikusonyeza kuti wasayansi, ngakhale wanzeru kwambiri akhoza kupeza zinthu zomwe si zolondola.”

Wasayansi akuwerenga Baibulo

Masiku anonso, asayansi amalephera kudziwa bwinobwino zinthu zina zokhudza chilengedwechi ndipo amapangitsa anthu kuganiza zolakwika. N’zoona kuti masiku ano sayansi yapita patsogolo kwambiri ndipo zimene asayansi apeza zikuthandiza anthu. Komatu ndi bwino kudziwa kuti asayansi sangatithandize kudziwa zonse. Wasayansi wina dzina lake Paul Davies, anati: “Takhala tikufufuza kuti tidziwe mmene zinthu zina m’chilengedwechi zimachitikira. Koma kunena zoona zinthu zambiri n’zozunguza mutu ndipo sitingathe kufotokoza bwinobwino mmene zinthuzi zimagwirira ntchito.” Apatu mfundo ndi yakuti, anthufe sitingakwanitse kudziwa zonse zokhudza chilengedwechi. Choncho anthu ena akamati sayansi ingatithandize kudziwa zonse, si bwino kufulumira kukhulupirira zimenezo.

Baibulo ndi lothandiza kwambiri kuposa sayansi

Pali zinthu zambiri zimene anthufe sitingazimvetse komanso kuzidziwa. Ponena za chilengedwechi, Baibulo limati: “Zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita [za Mulungu], ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Izi zikusonyeza kuti zimene Paulo analemba zaka 2,000 zapitazo n’zoona. Iye anati: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?”—Aroma 11:33.

Malangizo Amene Asayansi Sangapereke

N’zoona kuti asayansi amatithandiza kudziwa zambiri. Koma Baibulo lili ndi mfundo komanso malangizo omwe angatithandize kuti tizikhala osangalala komanso kuti tizikhala bwino ndi anthu. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

  • Dzanja

    Kupewa Kuphwanya Malamulo

    Kuona kuti moyo ndi wofunika

    “Usaphe munthu.”—Ekisodo 20:13.

    “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu.”—1 Yohane 3:15.

    Kukhala mwamtendere ndi anthu

    “Patukani pa zinthu zoipa ndipo chitani zabwino. Funafunani mtendere ndi kuusunga.”—Salimo 34:14.

    “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.”—Yakobo 3:18.

    Kupewa zachiwawa

    “Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe, ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Salimo 11:5.

    “Usasirire munthu wachiwawa, kapena kusankha njira zake. Pakuti munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye.”—Miyambo 3:31, 32.

  • Banja

    Malangizo Othandiza Mabanja

    Ana azimvera makolo awo

    “Ananu, muzimvera makolo anu mwa Ambuye, pakuti kuchita zimenezi n’chilungamo. ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,’ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo: ‘Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’”—Aefeso 6:1-3.

    Makolo aziphunzitsa bwino ana awo

    “Inunso abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”—Aefeso 6:4.

    “Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”—Akolose 3:21.

    Muzikondana ndi kulemekezana m’banja

    “Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.

  • Mtengo

    Kusamala Zachilengedwe

    Kale anthu ena a ku Isiraeli ankawononga zinthu zosiyanasiyana. Ponena za anthu amenewa Baibulo linati: “Dzikolo laipitsidwa ndi anthu okhalamo . . . anthu okhala m’dzikolo apezeka ndi mlandu.” (Yesaya 24:5, 6) Mulungu adzaimba mlandu anthu onse amene amawononga zinthu zachilengedwe. Baibulo limati Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Anthuwa sadzathawa ndipo adzalandira chilango cha zochita zawozo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena