Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 9/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu Ukulamulira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Muziphunzira Maulosi a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 7
    Galamukani!—2012
  • Maulosi Amene Anakwaniritsidwa
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 9/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

N’chifukwa chiyani m’Baibulo mumapezeka maulosi?

Yesu akulankhula ndi ena mwa atumwi ake paphiri la Maolivi

N’chifukwa chiyani Baibulo linafotokoza zinthu zomwe zikuchitika masiku ano?—Luka 21:10, 11.

M’Baibulo muli maulosi ambiri onena mwatsatanetsatane zimene zidzachitike m’tsogolo. Palibe munthu amene angafotokoze zinthu zam’tsogolo ngati mmene Baibulo limachitira. Choncho kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kumatitsimikizira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.—Werengani Yoswa 23:14; 2 Petulo 1:20, 21.

Maulosi amene anakwaniritsidwa kale amatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu. (Aheberi 11:1) Amatitsimikiziranso kuti zimene Mulungu analonjeza zoti dzikoli lidzakhala paradaiso zidzakwaniritsidwa. Zimenezi zimatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.—Werengani Salimo 37:29; Aroma 15:4.

Kodi maulosi a m’Baibulo amatithandiza bwanji?

Maulosi ena amanenedwa n’cholinga chothandiza atumiki a Mulungu kudziwa zochita, ulosiwo ukamadzakwaniritsidwa. Mwachitsanzo, Akhristu oyambirira ataona zinthu zina zimene ulosi unanena zikuchitika, anathawa mu Yerusalemu. Ndiyeno pamene mzindawu unkawonongedwa chifukwa choti anthu ambiri anakana kukhulupirira Yesu, Akhristu omwe anathawa aja anapulumuka.—Werengani Luka 21:20-22.

Maulosi amene akukwaniritsidwa masiku ano amatitsimikizira kuti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uwononga maboma onse a anthu. (Danieli 2:44; Luka 21:31) Choncho m’pofunika kuti aliyense azichita zinthu zosonyeza kuti ali kumbali ya Yesu Khristu, amene anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale Mfumu.—Werengani Luka 21:34-36.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena