Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 10/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Zimene Ena Achita Pofuna Kuthetsa Umphawi
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
    Galamukani!—1998
  • Nkhani Yabwino kwa Osauka
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 10/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi umphawi ungadzathedi padzikoli?

Amayi akumbatira mwana kwinaku atanyamula mbale yopanda kanthu

Kodi Mulungu Adzachita Zotani Kuti Anthu Asamadzavutikenso Ndi Umphawi?​—Mateyu 6:9, 10.

Chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri amafa ndi njala komanso matenda omwe amabwera chifukwa cha umphawi. Ngakhale kuti pali mayiko ena omwe ndi olemera, zikuoneka kuti anthu ambiri akuvutika ndi umphawi. Baibulo limanena kuti anthu akhala akuvutika ndi umphawi kuyambira kalekale.—Werengani Yohane 12:8.

Kuti umphawi udzathe, pakufunika boma lolamulira dziko lonse lapansi limene lizidzapatsa anthu zimene akufunika mosakondera. Boma limeneli lidzafunikanso kuthetsa nkhondo zomwe zimachititsa kuti anthu ambiri akhale mu umphawi. Mulungu watilonjeza kuti adzabweretsa boma lotereli.—Werengani Danieli 2:44.

Kodi ndani adzathetse umphawi?

Mulungu anasankha Yesu kuti adzalamulire dzikoli. (Salimo 2:4-8) Yesu akadzakhala mfumu, adzathandiza anthu osauka omwe amaponderezedwa komanso kuzunzidwa.—Werengani Salimo 72:8, 12-14.

Baibulo linaneneratu kuti popeza Yesu ndi “Kalonga Wamtendere” adzakhazikitsa mtendere komanso chitetezo padziko lonse. Kenako aliyense adzakhala ndi nyumba yakeyake komanso chakudya chokwanira. Anthu adzakhalanso ndi mwayi wogwira ntchito yakumtima kwawo.—Werengani Yesaya 9:6, 7; 65:21-23.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 8 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena