Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 12/1 tsamba 3
  • Kodi kudziwa zimene Baibulo limanena kungakuthandizeni bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi kudziwa zimene Baibulo limanena kungakuthandizeni bwanji?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Baibulo Ndi Buku Lomveka Bwino
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Tingawathandize Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 12/1 tsamba 3

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMANENA?

Baibulo Ndi Buku Lothandiza Kwambiri

Mayi wina wa ku China, dzina lake Lin anati: “Ndimadziwa ndithu kuti Baibulo ndi buku limene anthu ambiri opemphera amaligwiritsa ntchito koma ndimaona kuti ndi lothandiza m’mayiko ena osati ku China kuno.”

Bambo wina wa ku India, dzina lake Amit, ananena kuti: “Ngati ndimalephera kumvetsa mabuku a chipembedzo changa chachihindu, ndiye kuli bwanji Baibulo?”

Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Yumiko anati: “Ndimangomva zoti Baibulo ndi buku lakale komanso kuti anthu ambiri ali nalo. Koma chibadwire sindinalionepo.”

Padzikoli anthu ambiri ali ndi Baibulo ndipo amaona kuti ndi lofunika. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri a m’mayiko a ku Asia amadziwa zochepa kwambiri ndipo ena sadziwa n’komwe zimene Baibulo limanena. Ndipo n’zodabwitsanso kwambiri kuti m’mayiko omwe Baibulo ndi buku lofala kwambiri, anthu owerengeka chabe ndi amene amadziwa zimene limanena.

Mayi akuwerenga Baibulo

Ndiye mwina mungafunse kuti, ‘Kodi kudziwa zimene Baibulo limanena kungandithandize bwanji?’ Kumvetsa zimene Baibulo limanena kungakuthandizeni:

  • Kudziwa zimene mungachite kuti muzisangalala

  • Kukhala ndi banja losangalala

  • Kuti musakhale ndi nkhawa

  • Kuti muzigwirizana ndi anthu ena

  • Kuti muzitha kugwiritsa ntchito bwino ndalama

Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Yoshiko, ankafuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo anaganiza zongoliwerenga yekha. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yoshiko anati: “Baibulo landithandiza kudziwa chifukwa chake Mulungu anatilenga komanso zimene tikuyembekezera kutsogoloku. Zimenezi zandithandiza kuti ndizisangalala.” Nayenso Amit amene tamutchula poyamba uja anawerenga Baibulo payekha ndipo ananena kuti: “Nditawerenga Baibulo ndinadabwa nditadziwa kuti ndi buku lothandiza wina aliyense.”

Baibulo lathandiza anthu mamiliyoni ambiri. Inunso lingakuthandizeni ngati mutaliwerenga ndi kumvetsa zimene limanena.

Moyo Wokhutiritsa Mmene Mungaupezere

Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene Baibulo lingakuthandizireni, werengani kabuku kakuti, Moyo Wokhutiritsa Mmene Mungaupezere, kofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Kabukuka kakupezekanso pa webusaiti ya www.jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena