Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 12/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ndi anthu otani amene Mulungu amafuna kuti akhale anzake?
  • Kodi Choonadi Ndi Chofunikabe Masiku Ano?
    Nkhani Zina
  • Akristu Amalambira Mumzimu ndi M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kutsanzira Mulungu wa Choonadi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 12/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi n’zotheka kumudziwadi Mulungu?

Wa Mboni akulalikira munthu wina ku paki

N’chifukwa chiyani mulungu amafuna kuti timudziwe bwino? werengani Yohane 17:3

Mulungu amafuna kuti timudziwe. N’chifukwa chake anagwiritsa ntchito mphamvu yake ya mzimu woyera pothandiza anthu kuti alembe Baibulo. (2 Petulo 1:20, 21) Choncho tikhoza kumudziwa bwino Mulungu tikamawerenga Baibulo.—Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16.

Baibulo limatithandiza kudziwa makhalidwe a Mulungu komanso zimene amafuna. Limafotokoza chifukwa chimene Mulungu anatilengera, zimene wakonza kuti adzatichitire mtsogolomu komanso zimene amafuna kuti tizichita. (Machitidwe 17:24-27) Choncho tinganene kuti Yehova Mulungu amafuna kuti timudziwe bwino.—Werengani 1 Timoteyo 2:3, 4.

Kodi ndi anthu otani amene Mulungu amafuna kuti akhale anzake?

Yehova amafuna kuti anthu amudziwe bwino ndipo n’chifukwa chake anatumiza Mwana wake kuti adzaphunzitse anthu zokhudza iyeyo. Choncho amathandiza anthu amene amafunitsitsa kudziwa zolondola kuti akhale otsatira a Yesu. (Yohane 18:37) Ndipo amafuna kuti anthu oterewa akhale anzake komanso azimulambira.—Werengani Yohane 4:23, 24.

Satana Mdyerekezi amaphimba anthu m’maso kuti asamudziwe bwino Mulungu. Amachita zimenezi pofalitsa mabodza. (2 Akorinto 4:3, 4) Anthu amene safuna kudziwa zolondola zokhudza Mulungu, amakhulupirira mabodza amenewa. (Aroma 1:25) Komabe pali anthu ena ambiri omwe amaphunzira Baibulo ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asapusitsidwe ndi mabodza a Satana.—Werengani Machitidwe 17:11.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 1 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena