Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 1 tsamba 4-5
  • Kodi Chinyengo N’choopsa Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chinyengo N’choopsa Bwanji?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ANTHU AMASIYA KUKUKHULUPIRIRA
  • CHINYENGO CHILI NGATI MATENDA OPATSIRANA
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachinyengo?
    Galamukani!—2012
  • Kodi Ubwino Wopewa Chinyengo Ndi Wotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Mukufunitsitsa Kuyang’anizana ndi Chowonadi m’Moyo Wanu?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Mmene Mungayang’anizirane ndi Chitokoso Chamakhalidwe a Kukhala Waumphaŵi
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 1 tsamba 4-5
Amayi awiri akukambirana

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUCHITA ZINTHU MOONA MTIMA?

Kodi Chinyengo N’choopsa Bwanji?

Mayi wina wa ku South Africa, dzina lake Samantha, anati: “Mavuto ena angathe ngati utangochitako kachinyengo pang’ono.”

Kodi mukugwirizana ndi zimene mayiyu ananena? N’zoona kuti munthu aliyense amakumana ndi mavuto amene angamuchititse kuganiza zochita chinyengo. Komano zimene timachita tikakumana ndi mavuto oterowo zimasonyeza zomwe zili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, munthu akhoza kulolera kuchita chinyengo n’cholinga choti asagwidwe komanso asachite manyazi. Koma zoona zake zikadziwika, munthuyo amakumana ndi mavuto aakulu. Tiyeni tione mavuto amene amabwera chifukwa cha chinyengo.

ANTHU AMASIYA KUKUKHULUPIRIRA

Anthu akamakhulupirirana m’pamene amagwirizana kwambiri. Koma sikuti zimenezi zimangochitika lero ndi lero. Anthu amayamba kukhulupirirana akamacheza nthawi zonse n’kumauzana zakukhosi komanso kuchita zinthu moganizirana. Komabe wina akachita zachinyengo ngakhale kamodzi kokha, mnzakeyo amasiya kumukhulupirira. Ndipotu zimakhala zovuta kuti ayambirenso kukhulupirirana.

Kodi munayamba mwanamizidwapo ndi munthu amene munkaona kuti ndi mnzanu wapamtima? Ngati ndi choncho, n’zosakayikitsa kuti munakhumudwa kwambiri. Kunena zoona chinyengo chimasokoneza mgwirizano ndiponso chibale.

CHINYENGO CHILI NGATI MATENDA OPATSIRANA

Pulofesa wa pa yunivesite ya California, dzina lake Robert Innes, anachita kafukufuku wina ndipo anapeza kuti “chinyengo chili ngati matenda opatsirana.” Choncho zimakhala zosavuta kuti munthu ayambe kuchita chinyengo ngati amakonda kuchita zinthu ndi munthu wachinyengo.

Kodi mungatani kuti musamachite nawo zinthu zachinyengo? Werengani mfundo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni.

Zimene Anthu Achinyengo Amachita

Amanena Bodza

Bambo wina akuvula mphete ya ukwati

KODI MUNTHU WABODZA AMATANI? Munthu wabodza amauza munthu wina zinthu zomwe si zoona. Nthawi zina amatha kusintha nkhani, kubisa mfundo zina, kapena kuikokomeza kwambiri.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Pakuti munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) “Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnzake.”—Aefeso 4:25.

Amanena Miseche

Abambo awiri akunong’onezana pamene bambo wina akulowa

KODI MUNTHU WAMISECHE AMATANI? Amanena zinthu zabodza komanso zoipa zokhudza munthu wina n’cholinga chomuipitsira mbiri.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Kazitape amangokhalira kuyambitsa mikangano, ndipo wonenera anzake zoipa amalekanitsa mabwenzi apamtima.” (Miyambo 16:28) “Popanda nkhuni moto umazima, ndipo popanda munthu wonenera anzake zoipa mikangano imazilala.”—Miyambo 26:20.

Amaba Mwachinyengo

Munthu akuloza wotchi yomwe wabisa m’jekete

KODI MUNTHU WAKUBA MWACHINYENGO AMATANI? Munthu wakuba mwachinyengo amanyengerera kapena kupusitsa munthu wina n’cholinga choti amubere.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Usachitire chinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubera.” (Deuteronomo 24:14, 15) “Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga, koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.”—Miyambo 14:31.

Amaba

Munthu akuba kachikwama ka ndalama m’chikwama cha munthu wina

KODI MUNTHU WAKUBA AMATANI? Munthu wakuba amatenga katundu, ndalama kapena zinthu zina zomwe si zake popanda chilolezo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.” (Aefeso 4:28) “Musasocheretsedwe. . . . Akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena