Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 1 tsamba 15
  • Musamade Nkhawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musamade Nkhawa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Muziganiziranso za Mawa
    Nsanja ya Olonda—2007
  • N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Muzimutulira Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Nkhawa
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 1 tsamba 15

MFUNDO ZAKALE KOMA ZOTHANDIZABE MASIKU ANO

Musamade Nkhawa

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu.”—Mateyu 6:25.

Mayi akuyang’ana palisiti mosonyeza kuti ali ndi nkhawa

Kodi mfundoyi imatanthauza chiyani? Yesu anayankhula mawuwa pa ulaliki wina womwe unachitikira paphiri. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo, linanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kudera nkhawa,” angatanthauze “zimene munthu amachita akamakumana ndi mavuto monga umphawi komanso njala.” Kuwonjezera pamenepa nthawi zambiri anthu amada nkhawa akaganizira zimene zidzawachitikire m’tsogolo. N’zoona kuti si kulakwa kumaganizira kwambiri za achibale athu ndiponso mmene tingapezere ndalama zogulira zinthu zofunika. (Afilipi 2:20) Komabe, Yesu ananena mawu akuti “lekani kudera nkhawa,” chifukwa sankafuna kuti otsatira ake azida nkhawa ndi zinthu zomwe sizinachitike n’komwe kuopera kuti angamakhale osasangalala.—Mateyu 6:31, 34.

Kodi mfundoyi ndi yothandiza masiku ano? Malangizowa ndi othandiza kwambiri ngakhale masiku ano. Tikunena zimenezi chifukwa mabuku ena amanena kuti munthu amene amangokhalira kuda nkhawa amadwaladwala. Amadwala matenda monga “zilonda za m’mimba, matenda a mtima komanso chifuwa cha mphumu [kapena kuti asima].”

Yesu anatchula chifukwa chimene chingatithandize kuti tisamade nkhawa. Anasonyeza kuti kuda nkhawa sikungatithandize chilichonse. Iye anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” (Mateyu 6:27) Zimenezi n’zoona chifukwa zinthu zina zimene timada nazo nkhawa sizingachitike n’komwe. Katswiri wina wa maphunziro anati: “Kumangodera nkhawa zam’tsogolo n’kutaya nthawi. Mwina zimene tikudera nkhawazo sizichitika n’komwe.”

Mayi akuthyola ndiwo padimba

Kodi tingatani kuti tisamangokhalira kuda nkhawa? Choyamba, tiyenera kumadalira kwambiri Mulungu. Baibulo limanena kuti Mulungu amadyetsa mbalame komanso amaveka maluwa. Choncho sangalephere kuthandiza anthu amene amamulambira kuti azipeza zinthu zofunikira pa moyo. (Mateyu 6:25, 26, 28-30) Chachiwiri, ngati mwakumana ndi vuto linalake, musamakhale ndi nkhawa kuti vutolo lidzachitikanso mawa. Yesu anati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.” Mwina nanunso mumavomereza mfundo yakuti, “zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.

Choncho taona kuti kutsatira malangizo a Yesu kungatithandize kuti tisamadwaledwale chifukwa cha nkhawa. Kuwonjezera pamenepa timakhala ndi mtendere wa mumtima womwe Baibulo limautchula kuti “mtendere wa Mulungu.”—Afilipi 4:6, 7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena