Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 2 tsamba 5-7
  • Nchifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIYANI CHINACHITIKA KUTI ANTHU AZIFA?
  • KODI MULUNGU ANACHITAPO CHIYANI?
  • N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANAVUTIKA MPAKA KUFA?
  • KODI INUYO MUNGAPINDULE BWANJI NDI IMFA YA YESU?
  • Kodi Yesu Amapulumutsa Motani?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • N’chifukwa chiyani Yesu Anafa?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • N’zotheka Ndithu Kuti Amene Ali Kumanda Adzakhalenso ndi Moyo
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 2 tsamba 5-7
Anthu a mitundu yosiyanasiyana akusangalala mu Paradaiso

NKHANI YA PACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?

‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 5:12

Adamu ndi Hava akuyang’ana chipatso choletsedwa; Adamu ndi Hava atakalamba; anthu anyamula bokosi lamaliro ndipo akupita nalo kumanda

Kodi mungayankhe bwanji ngati munthu atakufunsani kuti, “Kodi mukufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale?” Ambiri akhoza kuyankha kuti inde, koma amaona kuti n’zosatheka. Amanena kuti anthufe tinalengedwa kuti tizikhala ndi moyo kwa kanthawi kochepa n’kufa.

Nanga bwanji atakufunsani kuti, “Kodi mumafuna mutafa?” Ambiri angayankhe kuti ayi, chifukwa anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo kwa nthawi yaitali ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. Ndipo n’zimene Baibulo limanena, kuti Mulungu “anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Mlaliki 3:11.

Komatu anthufe sitikhala ndi moyo mpaka kalekale. Ndiye n’chiyani chinachitika kuti tizifa? Nanga Mulungu anachitapo chiyani pofuna kuthetsa vutoli? Baibulo limayankha mafunsowa komanso limafotokoza chifukwa chimene Yesu anavutikira mpaka kufa.

N’CHIYANI CHINACHITIKA KUTI ANTHU AZIFA?

Machaputala atatu oyambirira a buku la Genesis amatifotokozera kuti Mulungu analenga Adamu ndi Hava kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale. Anawapatsanso malamulo amene anayenera kutsatira kuti asafe. Koma Baibulo limafotokoza kuti anthuwa analephera kumvera malamulowo ndipo anataya mwayi wopitiriza kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Nkhaniyi inalembedwa mwachidule komanso m’njira yosavuta kumva, moti anthu ena amaganiza kuti ndi yongopeka. Koma mofanana ndi Mauthenga Abwino, buku la Genesis ndi lolondola komanso limafotokoza nkhaniyi momveka bwino.a

Kodi zotsatira za kusamvera kwa Adamu ndi zotani? Baibulo limanena kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Adamu anachimwa ndipo n’chifukwa chake anakhala ndi moyo kwa nthawi yochepa, kenako n’kufa. Ifeyo tinatengera uchimo wa Adamu chifukwa tinachokera kwa iyeyo. Zimenezi zinachititsa kuti tizidwala, tizikalamba ndiponso tizifa. Mfundo imeneyi imagwirizana ndi zimene asayansi anapeza zoti ana amatengera zinthu zina kuchokera kwa makolo awo. Koma kodi Mulungu anachitapo zotani kuti athetse mavuto amenewa?

KODI MULUNGU ANACHITAPO CHIYANI?

Adamu atachimwa anachititsa kuti ana ake onse asakhalenso ndi mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. Choncho Mulungu anakonza zoti awombole mtundu wa anthu kuti akhalenso ndi mwayi wodzakhala mpaka muyaya. Kodi anachita zotani kuti zimenezi zitheke?

Lemba la Aroma 6:23 limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” Zimenezi zikutanthauza kuti imfa imabwera chifukwa cha uchimo. Adamu anachimwa ndipo anafa. Zimenezi n’zimenenso zimachitikira anthu ochimwafe chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa. Komabe sikuti anthufe timachita kufuna kuti tibadwe ochimwa. N’chifukwa chake Mulungu mwachikondi chake anatumiza Mwana wake Yesu kuti adzatifere ngati njira yolipirira machimo athu. Ndiye zimenezi zimatheka bwanji?

Anthu a mitundu yosiyanasiyana akusangalala mu Paradaiso

Imfa ya Yesu inathandiza kuti anthu adzakhale ndi moyo mpaka kalekale

Adamu yemwe anali munthu wangwiro anatipatsira uchimo ndi imfa chifukwa cha kusamvera. Choncho panafunikanso munthu wina wangwiro yemwe akanamvera mpaka imfa yake kuti atiwombole ku imfa. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Pakuti monga mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu, ambiri adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) “Munthu mmodziyu” ndi Yesu. Iye anachoka kumwamba n’kudzakhala munthu wangwirob ndipo kenako anatifera. Pa chifukwa chimenechi anthufe timatha kukhala olungama pamaso pa Mulungu ndipo timayembekezera kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANAVUTIKA MPAKA KUFA?

N’chifukwa chiyani Yesu anafunika kufa? Kodi Mulungu Wamphamvuyonse sakanatha kungokhazikitsa lamulo lina lomwe likanapatsa mwayi ana a Adamu kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale? Ndi zoona kuti ali ndi mphamvu zoti akanatha kuchita zimenezi. Komabe akanachita zimenezi ndiye kuti akanaphwanya lamulo limene anakhazikitsa yekha lakuti malipiro a uchimo ndi imfa. Lamulo limeneli linali lamphamvu komanso logwirizana ndi chilungamo cha Yehova moti sizikanatheka kungolisintha.—Salimo 37:28.

Mulungu akanati anyalanyaze mfundo zake zachilungamo pa nkhaniyi, anthu akanakayikira ngati angachite chilungamo pa zinthu zina. Mwachitsanzo, akanasankha kuti ana ena a Adamu apitirize kukhala ndi moyo mpaka kalekale, kodi chikanakhala chilungamo? Kodi anawo akanakhulupirira kuti Mulungu azikwaniritsa malonjezo ake? N’zosangalatsa kuti Mulungu sananyalanyaze mfundo zake zachilungamo. Ndipo zimene anachita pofuna kutipulumutsa ku uchimo ndi imfa zimatitsimikizira kuti nthawi zonse amachita zoyenera.

Mulungu anagwiritsa ntchito nsembe ya Yesu kuti apatse anthu mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Pa Yohane 3:16, Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Imfa ya Yesu imasonyeza kuti Mulungu amachita zinthu zachilungamo nthawi zonse. Koposa zonse, imasonyezanso kuti Mulungu amakonda anthu kwambiri.

Mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza kuti Yesu anavutika mpaka kufa mozunzika. Kodi n’chifukwa chiyani anafunika kufa mozunzika choncho? Zimene Yesu anachita pololera kuzunzidwa komanso pokhala wokhulupirika zinathandiza kuti atsutse zimene Mdyerekezi ananena zoti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati atakumana ndi mavuto. (Yobu 2:4, 5) Zimene Satana ananenazi zinkaoneka ngati zoona chifukwa anali atachititsa Adamu, yemwe anali wangwiro kuti achimwe. Koma Yesu, yemwenso anali wangwiro anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri. (1 Akorinto 15:45) Apatu n’zoonekeratu kuti Adamu nayenso akanatha kumvera Mulungu. Choncho Yesu anatisiyira chitsanzo kuti ifenso tizipirira tikamakumana ndi mavuto. (1 Petulo 2:21) Mulungu anapatsa Mwana wake Yesu moyo wosakhoza kufa kumwamba, chifukwa chakuti anakhala wokhulupirika mpaka imfa.

KODI INUYO MUNGAPINDULE BWANJI NDI IMFA YA YESU?

Nkhani yoti Yesu anaphedwa ndi yoona ndipo imfa yake ndi imene inathandiza kuti anthu akhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Kodi inuyo mumafuna mutadzakhala ndi moyo mpaka kalekale? Yesu ananena zimene tiyenera kuchita kuti tidzapeze moyo. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Amene amafalitsa magaziniyi akukulimbikitsani kuti mudziwe zambiri za Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, komanso Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wake. A Mboni za Yehova am’dera lanu angakonde kukuthandizani. Mungapezenso mfundo zina zothandiza pawebusaiti yathu ya www.jw.org.

a Onani nkhani yakuti, “The Historical Character of Genesis,” m’buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 922. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

b Mulungu anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya. Zimenezi zinachititsa kuti Mariya akhale ndi pakati. Ndipo mzimu woyera unateteza Yesu kuti asatengere uchimo kwa Mariya.—Luka 1:31, 35.

Akuyendetsa mbale ya mkate pa Chikumbutso

“Muzichita Zimenezi”

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anasonkhanitsa atumwi ake okhulupirika n’kuwalamula kuti azichita mwambo wokumbukira imfa yake. Iye anawauza kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Masiku anonso a Mboni za Yehova amamvera lamulo limeneli ndipo chaka chilichonse amasonkhana kuti akumbukire imfa ya Yesu. Chaka chatha anthu okwana 19,862,783, anapezeka pamwambowu.

Chaka chino Chikumbutso cha imfa ya Yesu chidzachitika Lachitatu, pa 23 March dzuwa litalowa. Tikukupemphani kuti mudzabwere limodzi ndi banja lanu komanso anzanu. Pamwambowu, mudzamvetsera nkhani yochokera m’Baibulo yomwe idzafotokoze kufunika kwa imfa ya Yesu komanso mmene inuyo mungapindulire ndi imfayi. Simudzalipira chilichonse kuti mupezeke pamwambowu ndipo sipadzayendetsedwa mbale ya zopereka. Kuti mudziwe nthawi komanso malo amene mwambowu udzachitikire, funsani a Mboni za Yehova am’dera lanu. Mungapitenso pawebusaiti yathu ya jw.org/ny.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena