Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 4 tsamba 14-15
  • Kodi Zimene Mumakhulupirira Zimagwirizana Ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zimene Mumakhulupirira Zimagwirizana Ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI ZIMENE TIMAKHULUPIRIRA TINGAZIYEREKEZERE BWANJI NDI BAIBULO?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Ndani Amene Amapita Kumwanba, ndipo Nchifukwa Ninji?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 4 tsamba 14-15

Kodi Mungayerekezere Zomwe Mumakhulupirira Ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa?

KODI ndinu Mkhristu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Padziko lonse pali anthu oposa 2 biliyoni omwe amati amatsatira Khristu, ndipo izi zikusonyeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa atatu alionse, ndi Mkhristu. Masiku ano pali zipembedzo zambiri zachikhristu, koma zimasiyana pa nkhani ya zikhulupiriro. Choncho zimene mumakhulupirira zingasiyane ndi zomwe anthu ena omwe amati ndi Akhristu amakhulupirira. Kodi kukhulupirira zilizonse kuli ndi vuto? Inde, chifukwa Akhristu amayenera kutsatira mfundo zopezeka m’Baibulo.

Anthu omwe ankatsatira Yesu Khristu anayamba kudziwika kuti “Akhristu.” (Machitidwe 11:26) Iwo sankadziwika ndi maina ena chifukwa panali chikhulupiriro chimodzi chokha chachikhristu. Popeza kuti Yesu Khristu ndi yemwe anayambitsa Chikhristu, Akhristu onse ankatsatira malangizo komanso zimene iye ankawaphunzitsa. Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwanu zimagwirizana ndi zimene Khristu ankaphunzitsa, komanso zomwe otsatira ake oyambirira ankakhulupirira? Kodi mungadziwe bwanji ngati zimagwirizana? Njira yabwino kwambiri n’kudziwa zimene Baibulo limanena.

Taganizirani izi: Yesu Khristu ankalemekeza kwambiri Malemba chifukwa ndi Mawu a Mulungu. Iye ankadana ndi anthu omwe ankalimbikitsa miyambo ya anthu m’malo mophunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Maliko 7:9-13) Choncho tinganene kuti otsatira enieni a Yesu amayenera kutenga zikhulupiriro zawo m’Baibulo. Ndiyetu Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwathu zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena?’ Kuti muyankhe funsoli, mungachite bwino kuyerekezera zimene mumaphunzira ku tchalitchi kwanuko ndi zimene Baibulo limanena.

Yesu ananena kuti tiyenera kulambira Mulungu m’choonadi ndipo choonadi chimenechi chimapezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti tidzapulumuka ngati timadziwa “choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Choncho zimene timakhulupirira ziyenera kugwirizana ndi mfundo zolondola za m’Baibulo. Zimenezitu n’zofunika kwambiri chifukwa kupanda kutero sitingadzapulumuke.

KODI ZIMENE TIMAKHULUPIRIRA TINGAZIYEREKEZERE BWANJI NDI BAIBULO?

Tikukupemphani kuti muwerenge mafunso 6 amene ali m’nkhaniyi komanso muone mmene Baibulo likuyankhira mafunsowo. Muwerenge mavesi amene aikidwawo ndipo muone ngati akugwirizana ndi mayankho amene ali pansi pa mafunsowo. Kenako mudzifunse kuti, ‘Kodi zimene ndimaphunzira kutchalitchi kwathu zikugwirizana ndi zimene Baibulo likunenazi?’

Mafunso komanso mayankho omwe ali m’nkhaniyi akuthandizani kwambiri. Kodi mukufuna kuyerekezera zinanso zimene mumaphunzira kutchalitchi kwanu ndi zomwe Baibulo limanena? A Mboni za Yehova akhoza kukuthandizani kuti mudziwe mfundo zolondola za m’Baibulo. Mungachite bwino kupempha wa Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere. Mukhozanso kupita pawebusaiti yathu ya jw.org/ny.

1 FUNSO: Kodi Mulungu ndi ndani?

YANKHO: Ndi Yehova amenenso ndi Atate ake a Yesu, alibe mapeto komanso ndi Mulungu yemwe analenga zinthu zonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Nthawi zonse tikamakupemphererani, timayamika Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.”​—Akolose 1:3.

“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse.”​—Chivumbulutso 4:11.

Onaninso Aroma 10:13; 1 Timoteyo 1:17.

2 FUNSO: Kodi Yesu Khristu ndi ndani?

YANKHO: Ndi Mwana woyamba wa Mulungu. Yesu anachita kulengedwa, choncho tingati ali ndi chiyambi. Ndipo amamvera mokhulupirika zimene Mulungu akufuna.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Atate ndi wamkulu kuposa ine.”​—Yohane 14:28.

“[Yesu] ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”​—Akolose 1:15.

Onaninso Mateyu 26:39; 1 Akorinto 15:28.

3 FUNSO: Kodi mzimu woyera n’chiyani?

YANKHO: Mzimu woyera ndi mphamvu yomwe Mulungu amagwiritsa ntchito kuti akwaniritse zomwe akufuna. Koma si munthu. Anthu akhoza kudzozedwa ndi mzimu woyera komanso kupatsidwa mphamvu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali m’mimba mwakemo linadumpha. Ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera.”​—Luka 1:41.

“Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.”​—Machitidwe 1:8.

Onaninso Genesis 1:2; Machitidwe 2:1-4; 10:38.

4 FUNSO: Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

YANKHO: Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Mfumu yake ndi Yesu. Posachedwapa Ufumuwu ukwaniritsa cholinga cha Mulungu padziko lonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Mngelo wa 7 analiza lipenga lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: ‘Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake. Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.’”​—Chivumbulutso 11:15.

Onaninso Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.

5 FUNSO: Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba?

YANKHO: Ayi. Mulungu anasankha anthu ochepa otchedwa “kagulu ka nkhosa” kuti akakhale kumwamba. Iwo akakhala mafumu limodzi ndi Yesu ndipo adzalamulira anthu padziko lonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.”​—Luka 12:32.

“Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye.”​—Chivumbulutso 20:6.

Onaninso Chivumbulutso 14:1, 3.

6 FUNSO: Kodi cholinga cha Mulungu chokhudza anthu komanso dziko lapansili n’chotani?

YANKHO: Mu Ufumu wa Mulungu, dziko lapansili lidzakhala paradaiso ndipo anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wathanzi, mtendere wochuluka ndipo sadzafanso.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:10, 11.

“Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Onaninso Salimo 37:29; 2 Petulo 3:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena