Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 4 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi anthu ndi amene anayambitsa kupembedza?
  • Kodi munthu ayenera kukhala m’chipembedzo chinachake?
  • Zipembedzo
    Galamukani!—2014
  • Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Atakhala Kuti Sali M’chipembedzo Chilichonse?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 4 tsamba 16
Banja likuyang’anitsitsa nyumba zosiyanasiyana zopemphereramo

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi anthu ndi amene anayambitsa kupembedza?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti anthu anayambitsa okha zoti azipembedza. Ena amakhulupirira kuti Mulungu amagwiritsa ntchito chipembedzo pofuna kuthandiza anthu kuti akhale naye pa ubwenzi. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Pali “kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yakobo 1:27) Mfundoyi ikusonyeza kuti pali chipembedzo choona chimene Mulungu anayambitsa.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA

  • Mulungu amasangalala ndi chipembedzo chimene chimaphunzitsa mfundo za m’Baibulo.​—Yohane 4:23, 24.

  • Zipembedzo zimene zimaphunzitsa mfundo za anthu n’zosathandiza.​—Maliko 7:7, 8.

Kodi munthu ayenera kukhala m’chipembedzo chinachake?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Choncho Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira azisonkhana pamodzi mogwirizana.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA

  • Anthu omwe amalambira Mulungu mogwirizana amayenera kukhulupirira mfundo zofanana.​—1 Akorinto 1:10, 11.

  • Anthu a m’chipembedzo chimene Mulungu amavomereza ndi ogwirizana padziko lonse.​—1 Petulo 2:17.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku ili, Zimene Baibulo Limaphunzitsa?, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena