Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 1 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?
  • Kodi mavutowa adzatha?
  • Mavuto
    Galamukani!—2015
  • Funso Lachitatu: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Ndizivutika?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola kuti Anthu Azivutika?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Akuvutika Chonchi?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 1 tsamba 16
Mayi akukumbatira mwana wake pa nthawi ya nkhondo

Dzikoli langodzaza ndi mavuto okhaokha. Koma kodi Mulungu ndi amene akuchititsa zimenezi?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.” (Yobu 34:10) Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa komanso mavuto amene timakumana nawo.

Mfundo zinanso zomwe Baibulo limanena

  • Satana Mdyerekezi, yemwe ndi ‘wolamulira wa dzikoli,’ ndi amene amachititsa mavuto ambiri.—Yohane 14:30.

  • Anthu amakumananso ndi mavuto chifukwa chosasankha zinthu mwanzeru.—Yakobo 1:14, 15.

Kodi mavutowa adzatha?

Anthu ena amakhulupirira kuti anthu akhoza kuthetsa mavuto ngati atamachita zinthu limodzi polimbana ndi mavutowo, pomwe ena amaona kuti n’zosatheka kuti zinthu zisinthe kwambiri m’dzikoli. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

Mulungu adzathetsa mavuto. Baibulo limati: “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Mfundo zinanso zomwe Baibulo limanena

  • Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuti athetse mavuto onse amene Mdyerekezi wachititsa.—1 Yohane 3:8.

  • Anthu abwino adzakhala mwamtendere padzikoli mpaka kalekale.—Salimo 37:9-11, 29.

Kuti mudziwe zambiri zokhudza chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika, werengani mutu 11 m’buku ili,Zimene Baibulo Limaphunzitsa? lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena