Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 5 tsamba 4-5
  • Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Angelo Ndi Otani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mmene Angelo Amatikhudzira
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Angelo—Kodi Amayambukira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 5 tsamba 4-5
Mkulu wa angelo komanso miyandamiyanda ya angelo

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Kodi mumafuna mutadziwa zoona zokhudza angelo? Mwachitsanzo, kodi angelo anachokera kuti, nanga amagwira ntchito yanji? Palibe kumene mungapeze mayankho olondola kuposa m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Ndiye kodi Baibulo limatiuza zotani zokhudza angelo?

  • Mofanana ndi mmene Mulungu alili, angelo ndi mizimu yosaoneka ndipo ‘alibe mnofu ndi mafupa.’ Angelo okhulupirika amakhala kumwamba ndipo amatha kuonekera pamaso pa Mulungu.​—Luka 24:39; Mateyu 18:10; Yohane 4:24.

  • Pa nthawi ina angelo anavala matupi a anthu kuti agwire ntchito imene Mulungu anawatuma padzikoli, ndipo atamaliza ntchitoyo anavula matupiwo n’kubwerera kumwamba.​—Oweruza 6:11-23; 13:15-20.

  • Ngakhale kuti Baibulo likamanena za angelo limawafotokoza ngati ndi aamuna, komanso akamaonekera kwa anthu amaoneka aamuna, sikuti pali angelo aamuna ndi aakazi. Angelo sakwatirana n’kubereka ana omwenso ndi angelo. Komanso sikuti angelo amayamba akhala kaye padzikoli ngati anthu kapena ana, kenako akamwalira n’kupita kumwamba. Angelo analengedwa ndi Yehova ndipo Baibulo limati ndi “ana a Mulungu woona.”​—Yobu 1:6; Salimo 148:2, 5.

  • Baibulo limati pali “malilime a anthu ndi a angelo,” kusonyeza kuti angelo amalankhula ndipo ali ndi chinenero chawo. Ngakhale kuti pa nthawi ina Mulungu ankagwiritsa ntchito angelo polankhula ndi anthu, iye safuna kuti tiziwalambira kapena kupemphera kwa iwo.​—1 Akorinto 13:1; Chivumbulutso 22:8, 9.

  • Pali miyandamiyanda ya angelo, mwinanso yokwana mabiliyoni ambiri.a​—Danieli 7:10; Chivumbulutso 5:11.

  • Angelo ndi “amphamvu” komanso anzeru kwambiri kuposa anthu. Iwo angathe kuyenda pa liwiro loposa chilichonse m’chilengedwechi.​—Salimo 103:20; Danieli 9:20-23.

  • Ngakhale kuti angelo ndi amphamvu komanso anzeru kwambiri, pali zinthu zina zimene sangathe kuchita komanso zimene sadziwa.​—Mateyu 24:36; 1 Petulo 1:12.

  • Angelo ndi osiyanasiyana ndipo ali ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo. Komanso Mulungu anawapatsa ufulu wosankha. Choncho mofanana ndi anthufe, nawonso angathe kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. N’zomvetsa chisoni kuti angelo ena anasankha kusamvera Mulungu.​—Yuda 6.

a Mwanda umodzi ndi 10,000. Choncho mwanda kuchulukitsa ndi mwanda ndi 100 miliyoni. Buku la Chivumbulutso limanena za angelo “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda.” Izi zikusonyeza kuti pali mamiliyoni mwinanso mabiliyoni a angelo.

Kodi Angelo Ali Ndi Maudindo Otani?

Yesu Khristu ndi mkulu wa angelo ndipo ali ndi udindo waukulu komanso mphamvu zochuluka. Malemba amasonyeza kuti dzina lake lina ndi Mikayeli.​—1 Atesalonika 4:16; Yuda 9.

Aserafi amagwira ntchito zapamwamba komanso amalandira ulemu wambiri poyerekeza ndi angelo ena. Aserafi ndi amene amakhala pafupi ndi mpando wachifumu wa Mulungu.​—Yesaya 6:1-3.

Akerubi nawonso amagwira ntchito zapamwamba komanso zapadera zogwirizana kwambiri ndi ulemerero wa Mulungu Wamphamvuyonse. Nthawi zambiri Baibulo limawafotokoza kuti amapezeka pamalo amene pali ulemerero wa Mulungu.—Genesis 3:24; Ezekieli 9:3; 11:22.

Angelo ena ambirimbiri amagwira ntchito zopereka mauthenga komanso amaimira Mulungu pokwaniritsa cholinga chake.b​—Aheberi 1:7, 14.

b Kuti mudziwe zambiri zokhudza angelo, werengani mutu 10 komanso Zakumapeto pamutu wakuti, “Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?” m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezekanso pawebusaiti ya www.jw.org/ny.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena