Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 June tsamba 14-15
  • Tisamaweruze Anthu Chifukwa cha Maonekedwe Awo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tisamaweruze Anthu Chifukwa cha Maonekedwe Awo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Tigwiritse Chikhulupiriro Chathu Chamtengo Wapatali!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 June tsamba 14-15
Peter amene ankangoyendayenda mumsewu

Tisamaweruze Anthu Chifukwa cha Maonekedwe Awo

M’BALE wina wa ku Canada dzina lake Don amayesetsa kulalikira anthu ovutika amene amangoyendayenda mumsewu. Pofotokoza za munthu wina wotere, Don anati: “Peter anali wauve kwambiri kuposa anthu ena onse. Iye anali wovuta ndipo sankafuna kuti anthu ena azimuyandikira. Ankakananso kuti anthu azimuthandiza.” Komabe kwa zaka zoposa 14, Don ankayesetsa kumuchitira zinthu zabwino.

Don akulalikira Peter amene wakhala m’mbali mwa nsewu

Tsiku lina Peter anafunsa Don kuti: “N’chifukwa chiyani mumalimbana ndi ine? Anthu ena onse samandivutitsa. Kodi vuto lanu n’chiyani?” Don anagwiritsa ntchito malemba atatu poyesetsa kuti amufike pamtima. Choyamba, anafunsa Peter ngati akudziwa dzina la Mulungu ndipo anamupempha kuti awerenge lemba la Salimo 83:18. Kenako, pofuna kumusonyeza chifukwa chake amalankhula naye, Don anapempha Peter kuti awerenge lemba la Aroma 10:13, 14 lomwe limanena kuti “aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Pomaliza, Don anawerenga Mateyu 9:36 ndipo kenako anapempha Peter kuti aliwerengenso yekha. Lembali limati: “Poona chikhamu cha anthu, [Yesu] anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” Peter atawerenga vesili, misozi inayamba kulengeza m’maso ndipo anafunsa kuti: “Kusonyeza kuti ine ndili ngati nkhosazi?”

Peter anayamba kusintha. Iye anayamba kusamba, kumeta ndevu komanso kuvala zovala zabwino zimene Don anamupatsa.

Peter ankakonda kulemba zimene zinkamuchitikira tsiku lililonse m’kabuku kenakake. Poyamba zimene ankalembamo zinali zinthu zomvetsa chisoni zokhazokha, koma atakumana ndi Don anasintha. Mwachitsanzo, tsiku lina analembamo kuti: “Lero ndaphunzira dzina la Mulungu. Panopa ndikamapemphera, ndimapemphera kwa Yehova. Ndikusangalala kwambiri kuti ndadziwa dzina lake. Don anandiuza kuti Yehova angakhale mnzanga wapamtima yemwe ndikhoza kulankhula naye nthawi iliyonse komanso kumuuza chilichonse chimene ndikufuna.”

Mawu omaliza amene Peter analemba m’bukuli analembera azibale ake. Iye anati:

“Lero sindikumva bwino m’thupi. Mwina vuto ndi ukalamba. Koma ngakhale nditamwalira lero, ndikudziwa kuti ndidzaonananso ndi mnzanga [Don] m’Paradaiso. Ngati mukuwerenga mawuwa, ndiye kuti ndamwalira. Mukadzaona munthu wachilendo pamaliro anga, mudzalankhule naye ndipo chonde muwerenge kabuku kabuluu aka [ankanena za buku lakuti “Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya” lomwe anapatsidwa kalekale].a Kabukuka kamanena kuti ndidzaonananso ndi mnzangayo m’Paradaiso. Ndimakhulupirira zimenezi ndi mtima wonse. Ndine m’bale wanu, Peter.”

Pambuyo pa mwambo wa maliro, mchemwali wa Peter dzina lake Ummi anafotokoza kuti: “Zaka pafupifupi ziwiri zapitazo, Peter analankhula nane. Pa nthawiyo ankaoneka kuti wayamba kusangalala moti ankamwetulira.” Ummi anauza Don kuti: “Ndiwerenga buku limene anandiuza chifukwa ngati linafika mchimwene wanga pamtima liyenera kuti ndi lapadera kwambiri.” Ndipo anavomeranso kuti aziphunzira buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndi Mboni za Yehova.

Don akuphunzitsabe Peter ndipo tsopano wayamba kuvala bwino

Nafenso tiyenera kupewa kuweruza anthu chifukwa cha maonekedwe awo. Tizisonyeza chikondi komanso tizichita zinthu moleza mtima ndi anthu osiyanasiyana. (1 Tim. 2:3, 4) Tikamachita zimenezi tikhoza kuthandiza anthu ngati Peter omwe maonekedwe awo si abwino koma ali ndi mtima wabwino. Sitiyenera kukayikira kuti Mulungu amene “amaona mmene mtima ulili” angathandize anthu oyenerera kuti aphunzire choonadi.​—1 Sam. 16:7; Yoh. 6:44.

a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma silikusindikizidwanso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena