Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 October tsamba 32
  • Kodi Mukudziwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mukati Inde Akhaledi Inde
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kuchokera kwa Owerenga
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 October tsamba 32

Kodi Mukudziwa?

Kodi Ayuda anali ndi chizolowezi chotani chomwe chinachititsa Yesu kuuza anthu kuti asamalumbire?

Munthu akulumbira m’kachisi

CHILAMULO CHA MOSE chinkalola anthu kulumbira pa nkhani zinazake. Koma pofika nthawi ya Yesu anthu ankangolumbira pa nkhani iliyonse imene akunena. Ankachita zimenezi potsimikizira kuti akunena zoona. Koma kawiri konse Yesu anatsutsa chizolowezi chopanda tanthauzochi, ndipo anaphunzitsa anthu kuti: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”​—Mat. 5:33-37; 23:16-22.

Buku lina lofotokoza nkhani za m’Malemba Achigiriki limanena kuti Ayuda ankakonda kulumbira pofuna kutsimikizira chilichonse chimene ankanena. Bukuli limati mukhoza kuzindikira zimenezi mukamawerenga buku la Talmud chifukwa linachita kufotokoza mwatsatanetsatane malumbiro oyenera kuwakwaniritsa ndi osayenera kuwakwaniritsa.

Koma si Yesu yekha amene anatsutsa chizolowezi choipachi. Wolemba mbiri wina wachiyuda dzina lake Flavius Josephus ananena za gulu lina lampatuko la Ayuda kuti: “Anthu amenewa amakana kulumbira, ndipo amaona kuti munthu amene walumbira ndi woipa kuposa amene wanena bodza m’khoti. Iwo amati ngati munthu mungamukhulupirire pokhapokha atatchula Mulungu, ndiye kuti munthuyo ndi wabodza.” Nalonso buku lina lachiyuda lotchedwa Nzeru za Sidraki, kapena kuti Ekleziastiko, (23:11) limati: “Munthu amene amalumbira nthawi zonse ndiye kuti amachita zoipa.” Ndiye m’pomveka kuti Yesu anatsutsa kuti anthu azilumbira mwachisawawa. Ngati nthawi zonse timanena zoona, anthu amatikhulupirira ndipo sitingafunike kulumbira kuti atikhulupirire.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena