Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 November tsamba 18-19
  • Munthu Wopatsa Adzadalitsidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Munthu Wopatsa Adzadalitsidwa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • “Ntchitoyi Ndi Yaikulu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 November tsamba 18-19
Hana wabwera ndi Samueli kuchihema

Munthu Wopatsa Adzadalitsidwa

KUYAMBIRA kalekale anthu akhala akupereka nsembe polambira Yehova. Aisiraeli ankapereka nsembe za nyama ndipo Akhristu akhala akupereka nsembe zotamanda Mulungu. Koma palinso nsembe zina zimene Mulungu amasangalala nazo. (Aheb. 13:15, 16) Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza kuti munthu akapereka nsembe zoterezi amakhala wosangalala ndipo amadalitsidwa.

Hana ankatumikira Mulungu mokhulupirika ndipo ankafunitsitsa mwana wamwamuna koma anali wosabereka. Iye anapemphera kwa Yehova n’kulonjeza kuti akadzakhala ndi mwana wamwamuna adzamupereka “kwa Yehova masiku onse a moyo wake.” (1 Sam. 1:10, 11) Patapita nthawi, Hana anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina loti Samueli. Mwanayo atangosiya kuyamwa, anapita naye kuchihema mogwirizana ndi lonjezo lake. Yehova anadalitsa Hana chifukwa cha mtima wake wodzimana. Iye anakhalanso ndi ana ena 5 ndipo Samueli anakhala mneneri komanso wolemba Baibulo.​—1 Sam. 2:21.

Masiku anonso Akhristu ali ndi mwayi wotumikira Mlengi wawo ndi moyo wawo wonse. Yesu ananena kuti anthu amene amalolera kudzimana zinthu zina n’cholinga choti atumikire Yehova adzadalitsidwa kwambiri.​—Maliko 10:28-30.

Nthawi ya atumwi, panali Mkhristu wina dzina lake Dorika amene ankakonda “kuchita ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.” Koma kenako “anadwala n’kumwalira” ndipo mpingo wonse unadandaula kwambiri. Ndiyeno ophunzira atamva kuti Petulo ali m’deralo anamupempha kuti afike mwamsanga. Petulo atafika anaukitsa Dorika ndipo anthu anasangalala kwambiri. M’Baibulo, aka n’koyamba kuti mtumwi aukitse munthu. (Mac. 9:36-41) Mulungu sanaiwale nsembe zimene Dorika ankapereka. (Aheb. 6:10) Zimene ankachita pothandiza anthu zinalembedwa m’Baibulo kuti zikhale chitsanzo kwa ifeyo.

Mtumwi Paulo anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani yodzipereka kuti athandize anthu ena. Iye analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Ineyo ndidzagwiritsa ntchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipereka ndi moyo wanga wonse chifukwa cha miyoyo yanu.” (2 Akor. 12:15) Paulo anaona umboni wakuti munthu akamadzipereka kuti athandize ena amasangalala, koma chofunika kwambiri n’chakuti amasangalatsa Yehova ndipo amadalitsidwa.​—Mac. 20:24, 35.

Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amasangalala tikamadzipereka kwambiri kuti timutumikire komanso tithandize anzathu. Koma kodi pali njira zina zimene tingathandizire pa ntchito yolalikira? Inde zilipo. Kuwonjezera pa ntchito zathu zachikondi, tikhoza kulemekeza Mulungu tikamapereka ndalama zathu. Ndalama zimenezi zimathandiza pa ntchito yolalikira komanso posamalira amishonale ndi atumiki ena a nthawi zonse. Zimathandizanso pokonza ndi kumasulira mabuku ndi mavidiyo, kusamalira amene akumana ndi ngozi zadzidzidzi komanso kumanga Nyumba za Ufumu. Choncho tisamakayikire kuti munthu wopatsa adzadalitsidwa kwambiri. Komanso tikamapereka zinthu zathu zamtengo wapatali kwa Yehova timasonyeza kuti timamulemekeza kwambiri.​—Miy. 3:9; 22:9.

Zimene Ena Amapereka Pothandiza pa Ntchito Yapadziko Lonse

Mofanana ndi nthawi ya mtumwi Paulo, Akhristu ambiri amapanga bajeti kapena kuika kandalama kenakake pambali kuti akaponye m’bokosi la zopereka za “Ntchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopereka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha zopereka zanu kumaofesi ngati amenewa. Mungafunse ku ofesi ya nthambi imene imayang’anira dziko lanu kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi. Adiresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Mungapereke zopereka zanu m’njira zili m’munsizi ngati n’zotheka m’dziko lanu.

ZOPEREKA MWACHINDUNJI

  • Mukhoza kupempha banki yanu kuti ichotse ndalama mu akaunti yanu n’kutumiza ku akaunti ya ofesi ya nthambi. M’mayiko ena mukhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito jw.org kapena webusaiti ina.

  • Mukhoza kupereka ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali monga ndolo, mphete ndiponso zibangiri. Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti zinthuzo ndi zopereka.

ZONGOBWEREKA

  • Mungapereke ndalama n’kufotokoza kuti ngati nthawi ina mungadzazifune, mudzaziitanitsa.

  • Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti ndalamazo mwangowabwereka.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mwachindunji, pali njira zinanso zoperekera zinthu zothandiza pa ntchito ya Ufumu padziko lonse. Njira zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njira iliyonse, muyenera kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziwe njira zimene zingatheke m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenera kufunsanso anthu odziwa bwino za malamulo ndiponso misonkho.

Inshulansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandire ndalama za inshulansi kapena za penshoni.

Maakaunti a Kubanki: Mukhoza kukonza kuti gulu la Yehova lidzatenge ndalama za mu akaunti yanu ya kubanki mukadzamwalira. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke ku gulu la Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandire masheyawo mukadzamwalira.

Malo Kapena Nyumba: Mungapereke ku gulu la Yehova malo kapena nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri tsatirani linki yakuti, “Perekani Ndalama Zothandizira Ntchito ya Padziko Lonse” imene imapezeka m’munsi pawebusaiti ya jw.org, apo ayi imbani foni kapena kulemba kalata ku ofesi ya nthambi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena